Nyimbo 191
Pangani Chowonadi Kukhala Chanu
1. Njira ya chowonadi ndiyo yabwino.
Palibe yoposa iyi.
Yesu anatiphunzitsatu kupatsa,
Kuti chimwemwe chikule.
M’khale owona.
M’sonye chikhulupiro.
Mwamakhalidwe anu inu
Mudziŵitsa cho’nadi nchanu.
2. Mwa kuika Ya poyamba ndi kumtama,
Mudzasiyana ndi dziko.
Kwa osakhulupilira nkodabwitsa
Kusankhadi chilungamo.
M’khale owona.
Siyanani ndi dziko.
Poyandikira kwa Yehova,
Mudziŵitsa cho’nadi nchanu.
3. Mdyerekezi adzayesa kutinyenga,
Koma mungathe kumtsutsa.
Chidaliro chidzakutetezerani
Ndi kupeŵa mivi yake.
M’khale owona.
Satana timamdziŵa.
Potenga zovala za M’lungu,
Mudziŵitsa cho’nadi nchanu.
4. Thupi nlofo’ka ndipo mtima ngwoipa.
Tilimbana ndi uchimo.
Tsimikizani kuti Mungagonjetse,
M’lungu ndi Mthandizi wanu.
M’khale owona.
Mukanetu zoipa.
M’kaletsa ziŵalo zathupi,
Mudziŵitsa cho’nadi nchanu.