Nyimbo 7
Chiyembekezo cha Mpumulo wa Anthu
1. Chilengedwe chibuula.
Mosaphula kanthu.
Koma Sabata lafika.
Mpumulo wafika.
2. Chimasuko cha mtendere,
Kumasula zonse,
Kristu azadzibweretsa;
M’lungu am’lamula.
3. Mu’lamuliro wa Kristu,
Zonse zikonzedwa.
Chimasuko chidzathetsa
Ukapolo wonse.
4. Anthu a Ya abukitsa
Chiyembekezochi.
Nalindira kuyankhidwa
Kwa mapempho awo.