Nyimbo 164
Ana—Mphatso za Mtengo Wapatali Zochokera kwa Mulungu
1. Ana ndimphatso za Mulungu,
Ayenera kuphunzitsidwa.
Mongatu mivi ya ngwaziyo
Tiwalunjikitse ’cholinga.
Mphatso za M’lungu;
‘Mutenge nthyole.’
Tisamalire mwachikondi,
Tiwaphunzitse mwapemphero.
2. Kudziŵa zolinga za ana
Kufunikira luso lathu.
Koma mwa kuyamba mwansanga
Tingasonkhezere cho’nadi.
Tifika mtima
Tikakangaza.
Daliranitu kwa Mulungu,
Pogwiritsa ntchito mawuwo.
3. Polankhulana nthaŵi zonse,
Ana athu adzamasuka
Adzalankhula mosawopa;
Tidzakhala mabwenzi awo.
Musawanyoze.
Lankhulanani.
Tisakhale onenezedwa
Pakulunjikitsa miviyi.
4. Choloŵa chathu ndicho ana
—Komadi ali a Mulungu.
Nzipatso zodzetsa mapindu
Tikawaphunzitsa zabwino.
Ha tifunadi
Kuti adziŵe.
Dalirani Ya mufupidwe.
Ndi ana athu timtamande.