Nyimbo 215
Kusonyeza Chifundo kwa Ena
1. Polamula za chigumulacho
Kuwononga anthu akale,
Yehova anati kwa Nowayo:
‘Umange lalika adziŵe!’
Kodi Nowa ananyala nyaza
Kumangatu chingalaŵacho?
Ayi, mwachifundo cha Mulungu,
Anamanga nalalikabe.
2. Dongosolo lakale likutha,
Mwachifundo M’lungu wanena
Kuti mbiriyo iperekedwe,
Kuti yense wofuna amve.
Kodi mwati: “Sindingala like;
Ndiri wosadziŵa kunena”?
Ngati mwalandirapo chifundo,
Mzimu udzakuthandizani.
3. Chisangalalo chikupezeka
Mwachowonadi ndi chifundo.
Kulaŵa za Ufumu wa M’lungu
Kuchoka m’dzanja la Yehova!
Tisonyeze chifundo kwa ena
Mwa kulimbitsa anthu onse:
Pangani kudzipereka msanga;
Ku Ufumu wa Mulunguwo.