Nyimbo 3
Kugonjetsa Dziko
1. Pamene timka tilaka
Mumphamvu ya Yehova,
Amachititsa kulaka
Munkhondo yolungama.
Timakwiyitsa mitundu
Mwa kufalitsa kwathu.
Modalira chilakiko,
Tidzamuka moguba.
2. M’dzikoli tidzavutika.
Tidziŵa zimenezo.
Yesu anati “Limbani!”
‘Ndidzakusunganibe.’
Tingapeze chilakiko,
Poti nkhondo siyathu.
Mulungu achita nkhondo;
Moto upha adani.
3. Tililaka dziko lino
Mokhulupira Kristu.
Popeza Ufumu wadza,
Amaponya lupanga.
Monga analaka dziko,
Ife tingateronso.
Modalira M’lungu wathu,
Tidzagonjetsa zedi.