Nyimbo 123
Pitani Patsogolo!
1. Pita patsogolo ku’chikulire!
Mulungu afuna kuti tipeze luso.
Yesetsa kuwongola utumiki,
M’lungu adalitsa ntchito.
Pali malo antchito kwa onse;
Nditchito Yesu anachitayo.
Yang’anani kwa M’lungu kuti m’sagwe.
Imirani chilungamo.
2. Pita patsogolo kulalikira!
Lengeza mbiri yabwino kwa anthu onse.
Tamandani Yehova Mfumu yathu
Mwa kuchitira umboni.
Nkana oipa akuwopseni,
Musabwevukeko amve onse
Ufumu wa Yehova wayandika.
Lengezani chowonadi.
3. Pita patsogolo; Wongoleranso
Luso pali ntchito yambiri yochitapo!
Mzimu wa M’lungu udzakuthandiza
Kuti upeze chimwemwe.
Kondani abale anu onse;
Chifukwa cha dzina la Mulungu.
Athandize kupita patsogolo,
Kuŵalitsa kuunika.