Kodi Nkutsatiriranji Wotipatsa Chitsanzo Wamkulu?
1 Chifukwa cha buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, kuyamikira Ambuye wathu Yesu Kristu kwakulitsidwa kwambiri. Tafikira pa kumdziŵa bwino kwambiri kuposa kale lonse. Ndipo nkoyenerera chotani nanga kuti mutu wathu wa nkhani ukuitanira ife tonse kuti titsatire Kristu Yesu mosamalitsa monga chitsanzo cha ife eni m’moyo! Pamene kuli kwakuti sitingakwaniritse mwangwiro chitsanzo chimene anatisiyira, ndithudi ife, ndi khalidwe lathu labwino ndi ntchito zabwino, tingathe kupereka umboni wa chikhumbo chathu chachikulu cha kuchita zomwe tingathe mu nkhaniyi.
2 Anthu ochuluka amakonda kutsanzira kapena kutsatira munthu winawake. Ambiri amachita motero pa zifukwa zadyera, akumaganiza kuti adzapeza zinthu zakuthupi, kutchuka, kapena kupeza ulamuliro pa ena. Mfarisiyo Gamaliyeli ananena za zolinga zotero pa Machitidwe 5:35-37. M’nthaŵi zamakono mamiliyoni ambiri amene anatsata Hitler mwakhungu ndi enanso onga iye anatsogoleredwa osati kunkhondo kokha komanso ku chinyengo, kulefulidwa, kugwiritsidwa mwala, ndi imfa.—Mat. 15:14.
3 Njira yachikristu sindiyo ya kutsatira munthu mwakhungu, koma kuzindikira bwinobwino ndi kukhala ndi chidaliro chachikulu mwa munthu amene Mulungu waika kukhala Mtsogoleri ndi Wokwaniritsa wa chikhulupiriro chathu, Yesu Kristu. (Yes. 55:4; Aheb. 12:2, 3, NW) Ngati timtsatira timatsimikizira za thandizo la Mulungu. Yesu anadziŵidwa mosaphonya kukhala uyo amene Mulungu anamvomereza. Yohane Mbatizi anaona umboni umenewu pa iye. (Mat. 3:16, 17) Kristu anaitana ena kukhala omtsatira, kuphatikizapo atumwi. Anadzionera okha ntchito zamphamvu zimene Yesu anachita ndi kumva uthenga wake wa Ufumu wosonkhezera mtima, ndipo anapereka umboni kwa ena wonena za zinthu zimenezi. (Mac. 2:22; 3:22-24) Petro, Yakobo, ndi Yohane anali mboni zodzionera za ulemerero wa Mwana wa Mulungu monga Mfumu yamtsogolo yolamulira. Yehova mwiniyo analengeza kuti ayenera kumvera Mwana wake. (Mat. 17:5) Ngakhale kuti ena sanakhulupirire mwa Yesu, aja amene anamdziŵa bwino anafunitsitsa kotheratu kutsatira iye yekhayo.—Yoh. 6:66-69.
4 Lerolino tili ndi umboni wa m’Malemba wakuti Yesu Kristu ndiye Wotipatsa Chitsanzo Wamkulu, munthu amene tiyenera kumtsata mosamalitsa. Umboni wa m’Malemba umenewu ngwonena za moyo wake, utumiki wake, imfa yake, ndi chiukiriro chake. Tiyenera kumtsatira mosamalitsa monga momwe mtumwi Paulo anachitira.—1 Akor. 11:1.
5 Tili ndi zifukwa zabwino zotsatirira mosamalitsa Wotipatsa Chitsanzo Wamkulu, kaya takhala m’choonadi kwa nthaŵi yaitali kapena ndife odzipatulira atsopano, achichepere kapena okalamba. Madalitso amafika kwa onse amene amatsatira mokhulupirika Wotipatsa Chitsanzo, Kristu Yesu. Kuchita motero kumalemekeza Mulungu ndi Atate wathu, Yehova.