Nyimbo 129
Tsopano Ndiyo Nthaŵi!
1. Tsono tilaliketu,
Chowonadi chimveke.
Musakhale ndi mantha;
Sonyeza Ufumu wa M’lungu.
Tichenjezetu anthu onse.
Kuti athawe mu Babulo
Kupulumuka imfa yake.
Awonetse changu pa M’lungu.
Ndinthaŵi tiwonetse changu.
2. Sonyezani kuwona
M’kusonyeza chikondi,
Kuthandiza abale,
Tingachuluke tingachepe.
Titumikiretu Mulungu,
Ndi kukonda cho’nadi chake,
Tiwone chiyanjo chakecho
Ndi kusunga umphumphu wonse.
Ndinthaŵi yosunga umphumphu.
3. Nkhondo idzamenyedwa,
Cho’nadi chidzalaka.
Mdima udzatha psiti.
Tikhale miyuni yoŵala.
Akufa onse adzauka,
Adzadyadi Mkate Wamoyo.
Sitidzawopanso zoipa.
Zonsezi Yehova wanena.
Ndinthaŵi tinene mawuwo.