Mutu 14
Baibulo ndi Inu
Osuliza amakono amanena kuti Baibulo liri losakhala lausayansi ndi lodzitsutsa lokha, kuti liri nthanthi chabe zongosonkhanitsidwira pamodzi. Yesu, kumbali ina, anati: “Mawu anu [Mulungu] ndiwo chowonadi.” (Yohane 17:17, “NW”) Umboni ukuchirikiza Yesu mmalo mwa osuliza. Zenizeni zimasonyeza kuti Baibulo liri lowona mogwirizana ndi mbiri. Ndiponso, kugwirizana kwake kwapaderako, kunena zowona kwa maulosi ake, nzeru yake yakuya, ndi mphamvu yake yotulutsa ubwino m’miyoyo ya anthu zonsezo zimasonyeza kuti Baibulo liri Mawu olembedwa a Mulungu. Monga momwe mtumwi Paulo analembera kuti: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu ndipo lipindulitsa.”—2 Timoteo 3:16.
1. (Phatikizamoni mawu oyamba.) (a) Kodi zenizeni zikutsimikiziranji ponena za Baibulo? (b) Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la chenicheni chakuti Baibulo liri Mawu ouziridwa a Mulungu?
CHENICHENI chakuti Baibulo liri mawu a Mulungu, osati a anthu, chiri ndi ziyambukiro zamphamvu. Chimatanthauza kuti Mulungu walankhuladi ndi anthu. Iye wayankha ochuluka a mafunso athu ndipo wasonyeza zothetsera za mavuto athu ochulukawo. Chimatanthauzanso kuti ziyembekezo za mtsogolo zofotokozedwa m’Baibulo ziri zowona. Ufumu wa Mulungu ukulamuliradi ndipo m’nthaŵi yake udzachitapo kanthu kuchotsa padziko lapansi chisalungamo chonse, chitsenderezo, ndi kuvutika.
2. Kodi chidziŵitso chakuti Baibulo liri Mawu a Mulungu chiyenera kukusonkhezerani kuchitanji?
2 Tsopano, funso nlakuti: “Kodi mudzachitanji ndi chidziŵitso chimenechi? Kunena zowona, chidziŵitso chakuti Baibulo liri Mawu a Mulungu chiyenera kukulimbikitsani kulisanthula. Wamasalmo analonjeza chimwemwe kwa awo amene amatero pamene iye analemba kuti: “Wachimwemwe ndiye munthu amene sayenda muuphungu wa oipa . . . koma chikondwerero chake chiri m’lamulo la Yehova, ndipo m’lamulo lake amaŵerenga mosamveketsa mawu usana ndi usiku.”—Salmo 1:1, 2, NW.
Landirani Thandizo
3, 4. (a) Monga momwe Baibulo lenilenilo limasonyezera, kodi tiyenera kuchitanji pamene tipeza zinthu m’Baibulo zimene sitimvetsetsa? (b) Kodi ndani amene nthaŵi zonse ali ofunitsitsa kuthandiza anthu kumvetsetsa bwino kwambiri Baibulo?
3 Mosakakikira, m’kuŵerenga kwanu Baibulo, mudzapeza zinthu zimene simukuzimvetsetsa. (2 Petro 3:16) Chochitika cholembedwa m’bukhu la Baibulo la Machitidwe chimasonyeza kuti zimenezi ziyenera kuyembekezeredwa. Mwamsanga pambuyo pa imfa ya Yesu, Mwitopiya anali kuŵerenga m’maulosi a Baibulo a bukhu la Yesaya. Mlaliki Wachikristu Filipo anakumana ndi munthuyo ndipo anamfunsa kuti: “Kodi ukumvetsetsa kwenikweni zimene ukuŵerenga?” Mwitopiyayo sanatero, chotero anapempha Filipo kumthandiza kumvetsetsa.—Machitidwe 8:30, 31, NW.
4 Mkazi wina mu United States anali m’mkhalidwe wofananawo. Iye anali woŵerenga Baibulo wa nthaŵi zonse, koma panali ziphunzitso zambiri zofunika za Baibulo zimene iye sanafikire pakuzimvetsetsa m’kuŵerenga kwake kwa iye mwini. Kunali kokha pamene iye anakhala ndi makambitsirano ndi Mboni za Yehova kuti iye anaphunzira zowonadi za maziko za Baibulo, kuphatikizapo kufunika kwa Ufumu wa Mulungu ndi madalitso ochuluka amene Ufumuwo udzadzetsera mtundu wa anthu. Ngati inunso muziitana, Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukuthandizani kuti nanunso mumvetsetse bwino kwambiri zimene mukuŵerenga m’Baibulo.
Gwiritsirani Ntchito Uphungu wa Baibulo
5. Malinga ndi kunena kwa Baibulo, kodi ndinjira yotani imene imadzetsa chimwemwe?
5 Tikulimbikitsidwa osati kokha kuŵerenga Baibulo komanso kuchitapo kanthu pazimene tikuŵerenga. (Salmo 119:2) Kuwonjezerapo, Baibulo limalimbikitsa kuti: “Laŵani ndi kuwona kuti Yehova ali wabwino, Oo anthu inu; wachimwemwe ndiye munthu wolimba amene amathaŵira mwa iye.” (Salmo 34:8, NW) M’chenicheni, limatipempha kuyesa Mulungu. Yesani kukhala ndi moyo mogwirizana ndi malamulo a makhalidwe abwino a Mulungu, kusonyeza kuti mumadalira Mulungu kudziŵa zimene ziri zabwino kopambana kwa inu. Npokhapo pamene inu mudzawona kuti imeneyi iridi njira yoyenera. Awo amene ali ndi chidaliro choterocho mwa Mulungu alidi achimwemwe.
6. Kodi nkotheka kuyesa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo ya Baibulo lerolino? Fotokozani.
6 Ena amanena kuti palibe aliyense amene angathe kukhala ndi moyo mogwirizana ndi malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo m’Dziko lino losawona mtima, lopanda makhalidwe abwino, ndi lachiwawa. Komabe, chowonadi nchakuti, ambiri akutero. Ndani? Mnyamata wina mu Afrika anapeza kagulu ka anthu oterowo. Iye akulemba kuti: “Ndakhala ndikupenda kwazaka zoŵerengeka zapitazo kuti muno m’Zimbabwe anthu inu, Mboni za Yehova, ndinokhanu amene mukuyesayesa, kutsatira chitsanzo chake cha Kristu . . . Ndinu kagulu kokha, kufikira patsopano lino, kamene kakhoza kundikhutiritsa maganizo ponena za chikondi cha Mulungu ndi mphamvu ya uthenga Wake wabwino, kupyolera mwa makhalidwe anu ndipo osati kokha kupyolera mwa mawu ndi zolemba. Inu mukukhala ndi moyo ndi kulalikira uthenga wabwino pamene anthu ambirimbiri, akulalikira uthenga wabwino koma osakhala ndi moyo mogwirizana nawo.”
Vomerezani Ulamuliro Wake
7. Kodi ndizizoloŵezi zotani zofala lerolino zimene ziri zosemphana ndi zimene Baibulo limanena?
7 Mtumwi Paulo ananena kuti Baibulo liri “lopindulitsa pakuphunzitsa, pakudzudzula, pakuwongolera zinthu.” (2 Timoteo 3:16, NW) Komabe, nthaŵi zina, zimene Baibulo limanena siziri zovomerezeka mofala. Mwachitsanzo, Baibulo limatsutsa machitachita a kugonana kwa aziŵalo zofanana, komatu kugonana kwa aziŵalo zofanana kukuwonedwa mofala monga njira ya moyo yovomerezeka. (Aroma 1:24-27; 1 Akorinto 6:9-11; 1 Timoteo 1:9-11) Baibulo limanenanso kuti moyo wa mwana wosabadwa ngwofunika ndipo suuyenera kuwonongedwa mwadala, koma kutaya mimba pafupifupi mamiliyoni 50 kukuchitidwa padziko lonse lapansi chaka chirichonse. (Eksodo 21:22, 23; Salmo 36:9; 139:14-16; Yeremiya 1:5) Bwanji ngati ife enife tikupeza kukhala kovuta kuvomereza zimene Baibulo limanena pankhani zoterozo?
8, 9. Pamene ife poyamba tikuwona kukhala kovuta kuvomereza mfundo ina m’Baibulo, kodi nchiyani chimene tiyenera kukumbukira, ndipo kodi ndimiyezo yayani imene ife nthaŵi zonse tiyenera kuivomereza?
8 Eya, Akristu aphunzira kuti nthaŵi zonse nkwanzeru kutsatira Mawu a Mulungu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti m’kupita kwanthaŵi, kutsatira zimene Baibulo limanena nthaŵi zonse kumakhala ndi zotulukapo zabwino kopambana kwa aliyense. (Miyambo 2:1-11) Chenicheni nchakuti, anthu ngopereŵera kwambiri panzeru. Iwo kaŵirikaŵiri samawoneratu zotulukapo zotsirizira za machitidwe awo. Mneneri Yeremiya anavomereza kuti: “Ndidziŵa bwino lomwe, O Yehova, kuti munthu wapansi pano njira yake siiri yake. Sikwamunthu woyenda ngakhale kulungamitsa mapazi ake.”—Yeremiya 10:23, NW.
9 Tingofunikira kuunguzaunguza motizinga kuti tiwone kuti mawu ameneŵa ngolondola. Ochuluka a mavuto amene akukantha dziko ali zotulukapo zachindunji za kusatsatira kwa anthu uphungu wa Mawu a Mulungu. Mbiri ya nthaŵi yaitali ya kuvutika kwa mtundu wa anthu yasonyeza kuti anthu sangathe mwachipambano kudzisankhira iwo eni m’nkhani za makhalidwe abwino. Mulungu ali ndi nzeru zosapimika kuposa ife. Bwanji nanga osavomereza zimene iye amanena, mmalo mwa kudalira panzeru ya ife eni?—Miyambo 28:26; Yeremiya 17:9.
Palibe Aliyense Amene Ali Wangwiro
10, 11. (a) Kodi ndizenizeni zotani ponena za mmene ife tinapangidwira ndi dziko m’limene tikukhala zimene zimachititsa mavuto pamene tiyesa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo ya Baibulo? (b) Kodi ndimayanjano otani amene Baibulo limatilimbikitsa kufunafuna, ndipo kodi tingapeze kuti mayanjano oterowo?
10 Baibulo limatichenjeza za mbali inanso mu imene ife tifunikira thandizo. Tonsefe talandira mwa choloŵa chizoloŵezi cha kuchita uchimo. “Chikhoterero cha mtima wa munthu nchoipa kuyambira paubwana.” (Genesis 8:21, NW; Aroma 7:21) Vuto limeneli likupangitsidwa kukhala lalikulu ndi chenicheni chakuti tikukhala ndi moyo m’dziko limene silimatsatira malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo. Chotero, tifunikira thandizo osati kokha kuti timvetsetse Baibulo komanso kuchita zinthu zimene timaphunzira. Ndicho chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuyanjana ndi anthu amene amafuna kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo yaumulungu. Wamasalmo analemba kuti: “Ndadana nawo msonkhano wa ochita zoipa, ndipo sindimakhala pansi ndi anthu oipa. . . . Pakati pa nantindi wa osonkhana ndidzadalitsa Yehova.” Ndipo salmo lina limati: “Nkwabwino chotani ndi kosangalatsa chotani nanga mmene kuliri kuti abale akhalire pamodzi muumodzi!”—Salmo 26:5, 12; 133:1, NW.
11 Kusonkhana pamodzi kuli mbali yofunika kwambiri ya kulambira kwa Mboni za Yehova. Izo ziri ndi misonkhano ingapo mlungu uliwonse, kudzanso misonkhano yaikulu yanthaŵi ndi nthaŵi, kumene iwo amaphunzirira Baibulo pamodzi ndi kukambitsirana mmene malamulo a makhalidwe abwino angagwiritsiridwire ntchito m’miyoyo yawo. Izo zimapanga “gulu la abale” la padziko lonse m’limene aliyense akulimbikitsidwa ndi kuthandizidwa kusungabe miyezo yapamwamba kwambiri ya Baibulo imeneyi. (1 Petro 2:17, NW) Bwanji nanga osafika paumodzi wa misonkhano yawo ndi kuwona mmene chitaganya chimenecho chingakuthandizireni inunso?—Ahebri 10:24, 25.
Khalani ndi Moyo Mogwirizana ndi Mawu a Mulungu
12. Kodi ndimadalitso otani amene amadza kuchokera m’kudziŵa kuti Baibulo liri Mawu a Mulungu?
12 Chotero, kudziŵa kuti Baibulo liri Mawu a Mulungu kumadzetsa madalitso ndi mathayo. Timadalitsidwa chifukwa chakuti timapeza chitsogozo kaamba ka khalidwe lathu la tsiku ndi tsiku chimene sichimapezeka kwina kulikonse. Ndiponso, timaphunzira za chikondi cha Mulungu m’kupereka Mwana wa iye yekha kudzatiombola kotero kuti tikhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (Yohane 3:16) Timazindikira kuti Yesu tsopano akulamulira monga Mfumu ndipo posachedwapa adzachitapo kanthu kuchotsa kuipa konse padziko lapansi. Ndipo ife mwachidaliro timayembekezera “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” zolungama zimene Mulungu mwini wazilonjeza.—2 Petro 3:13, NW.
13. Kodi ndimathayo otani amene amadza paife pamene tilandira Baibulo monga Mawu a Mulungu?
13 Komabe, kumbukirani, kuti tiri ndi thayo la kuphunzira Baibulo ndi kulabadira zimene iro limanena. Mulungu iye mwini amatifulumiza kuti: “Mwananga, usaiŵale malamulo anga, ndipo mtima wako usunge malangizo anga.” (Miyambo 3:1, NW) Ngakhale ngati ochuluka amawona Baibulo kukhala mawu a anthu, ife molimba mtima tiyenera “kulola Mulungu kukhala wowona, ngakhale anthu onse kupezeka onama.” (Aroma 3:4, NW) Lolani kuti nzeru ya Mulungu itsogoze moyo wanu. “Dalirani mwa Yehova ndi mtima wanu wonse . . . M’njira zanu zonse m’kumbukireni.” (Miyambo 3:5, 6, NW) Kulabadira mwanzeru Mawu a Mulungu mwanjira imeneyi kudzayambukira moyo wanu kuti ukhale wabwino ponse paŵiri tsopano ndi kuumuyaya wonse.
[Mawu Otsindika patsamba 187]
Sitiyenera kungoŵerenga chabe Baibulo komanso kuchitapo kanthu pazimene tikuŵerenga
[Mawu Otsindika patsamba 188]
Kutsatira zimene Baibulo limanena nthaŵi zonse kumakhala ndi zotulukapo zabwino kopambana