Nyimbo 41
Tamandani Yehova, Thanthwe
1. ‘Imvani m’yamba; Ndinene, dziko.
Imvani mawu nonse ofatsa.
Kuphunzitsa kwanga kudzanga mame,
Chowonadi changa chidzanga mvumbi.’
2. O tilengeze Dzina la M’lungu,
Anthu adziŵe kutchuka kwake.
Ndi owetedwa atamande Thanthwe.
Ntchito zake zonse nzachilungamo.
3. Mulungu wathu; ndiwolungama.
Njirazo zake zonse nchikondi.
Ali wolungama ndi wa cho’nadi,
Yehova ali wokhulupirika.
4. Tiwope M’lungu pochita bwino;
Tikondwere ndi malamulowo.
Tisawonongetu mbali yathuyo,
Koma kutumikirabe Yehova.