Nyimbo 137
Nthaŵi Zoikidwiratu Ziyandikira
1. O Yehova, Woyera,
Thanthwe lakalelo,
Mu Ziyoni m’bangula;
Chiweruzo chidza.
Ngakhale chikachedwa,
Tidziŵa chidzabe.
Ona mapeto afika;
Tiyembekezera.
2. Mudzadzetsa lupanga
Lanu mosachedwa.
Tikuwona tsopano,
Kulambira kwadza.
Oipawo anyada
Navulaza ife,
Koma nthaŵiyo yafika
Yoti mulamule.
3. Mbuye Mfumu, Yehova,
Ndilo dzina lanu.
Anthu akhale chete
Adziŵe za inu.
Mulamula mwa Yesu
Munjira yamphamvu.
Wokhala pampando, O Ya,
Mulamula dziko.
4. Tifuula mokondwa;
Ndi kuimbira Ya.
Mudzetsa ndi Kristuyo
Chipulumutsocho.
O Wamkulu Wammwamba,
Ndinthaŵi yanudi.
Chotero tiyembekeza
Chilakiko chanu.