Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Babulo Wamkulu
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa anthu amene sanadziŵe chowonadi cha Baibulo koma amene anakhala ndi moyo nafa kaleromonga mbali ya Babulo Wamkulu?

      Mac. 17:30: “Nthaŵi za kusadziŵako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima.”

      Mac. 24:15: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Kuti ndianthu “osalungama” ati amene adzaukitsidwa, Mulungu adzasankha.)

      Yobu 34:12: “Ndithudi zowonadi, Mulungu sangachite choipa, ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu.”

  • Baibulo
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Baibulo

      Tanthauzo: Mawu olembedwa a Yehova Mulungu kwa anthu. Anagwiritsira ntchito alembi aumunthu okwanira 40 mkati mwa nyengo ya zaka mazana 16 kulilemba, koma Mulungu mwiniyo anatsogoza kwenikweni kulembedwako mwa mzimu wake. Chotero liri louziridwa ndi Mulungu. Mbali yaikulu ya cholembedwacho njopangidwa ndi mawu enieni onenedwa ndi Yehova ndi malongosoledwe onena za ziphunzitso ndi ntchito za Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu. Mmenemu timapezamo mawu onena za malamulo a Mulungu kaamba ka atumiki ake ndi zimene adzachita kukwaniritsa chifuno chake chachikulu kaamba ka dziko lapansi. Kuti azamitse chiyamikiro chathu kaamba ka zinthu zimenezi, Yehova anasunganso m’Baibulo cholembedwa chosonyeza zimene zimachitika pamene anthu ndi mitundu amvetsera Mulungu ndi kugwira ntchito mogwirizana ndi chifuno chake, kudzanso chotulukapo pamene ayenda m’njira ya iwo eni. Kupyolera mwa cholembedwa cha m’mbiri chodalirika chimenechi Yehova amatidziŵitsa ntchito zake ndi anthu ndipo motero ndi umunthu wake wodabwitsa.

      Zifukwa zophunzirira Baibulo

      Baibulo lenilenilo limati nlochokera kwa Mulungu, Mlengi wa anthu

      2 Tim. 3:16, 17: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino.”

      Chiv. 1:1: “Chivumbulutso cha Yesu Kristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achiwonetsere akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa.”

      2 Sam. 23:1, 2: “Atero Davide mwana wa Jese . . . mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine, ndi mawu ake anali pa lilime langa.”

      Yes. 22:15: “Atero Ambuye Yehova wamakamu.”

      Tikayembekezera uthenga wa Mulungu kwa anthu onse kukhala wopezeka kuzungulira dziko lapansi. Baibulo, lathunthu kapena mbali yake, latembenuzidwira m’zinenero zokwanira 1 800. Kufalitsidwa kwake, kukufikira mabiliyoni ambiri. The World Book Encyclopedia imati: “Baibulo ndiro bukhu loŵerengedwa mofala koposa mabukhu onse m’mbiri. Mwinamwake lirinso lachisonkhezero kuposa onse. Makope ochulukirapo a Baibulo agaŵiridwa kuposa a bukhu lina lirilonse. Latembenuziridwanso m’zinenero zochulukirapo kuposa bukhu lina lirilonse.”—(1984), Vol. 2, p. 219.

      Ulosi wa Baibulo umalongosola tanthauzo la mikhalidwe ya dziko

      Atsogoleri adziko ambiri amavomereza kuti mtundu wa anthu uli pa mphembenu pa tsoka. Baibulo lidaneneratu mikhalidwe imeneyi kalekale; limalongosola tanthauzo lake ndi chimene chidzakhala chotulukapo chake. (2 Tim. 3:1-5; Luka 21:25-31) Limasimba zimene tiyenera kuchita kuti tipulumuke chiwonongeko choyandikiracho chadziko, kuti tikhale ndi mwaŵi wa kupeza moyo wamuyaya m’mikhalidwe yolungama pano padziko lapansi.—Zef. 2:3; Yoh. 17:3; Sal. 37:10, 11, 29.

      Baibulo limatikhozetsa kuzindikira chifuno cha moyo

      Limayankha mafunso onga akuti: Kodi moyo unachokera kuti? (Mac. 17:24-26) Kodi nchifukwa ninji tiri pano? Kodi ndiko kokha kuti tikhale ndi moyo zaka zoŵerengeka, kupeza zimene tingathe m’moyo, ndiyeno nkufa?—Gen. 1:27, 28; Aroma 5:12; Yoh. 17:3; Sal. 37:11; Sal. 40:8.

      Baibulo limasonyeza mmene tingakhalire ndi zinthu zenizenizo zimene okonda chilungamo amakhumba koposa

      Limatiuza kumene tingapeze atsamwali abwino amene amakondanadi wina ndi mnzake (Yoh. 13:35), chimene chingatipatse chitsimikiziro chakuti tidzakhala ndi chakudya chokwanira kaamba ka ife eni ndi mabanja athu (Mat. 6:31-33; Miy. 19:15; Aef. 4:28), mmene tingakhalire achimwemwe mosasamala kanthu za mikhalidwe yovuta yotizinga.—Sal. 1:1, 2; 34:8; Luka 11:28; Mac. 20:35.

      Limalongosola kuti Ufumu wa Mulungu, boma lake, udzachotsa dongosolo loipa liripoli (Dan. 2:44), ndipo mu ulamuliro wake anthu adzakhoza kukhala ndi thanzi langwiro ndi moyo wamuyaya.—Chiv. 21:3, 4; yerekezerani ndi Yesaya 33:24.

      Ndithudi bukhu limene limanena kuti nlochokera kwa Mulungu, limene limalongosola ponse paŵiri tanthauzo la mikhalidwe yadziko ndi chifuno cha moyo, ndi limene limasonyeza mmene mavuto athu adzathetsedwera nloyenera kulingaliridwa.

      Maumboni a kuuziridwa

      Nlodzala ndi maulosi osonyeza chidziŵitso chokwanira chamtsogolo—chinthu chosatheka kwa anthu

      2 Pet. 1:20, 21: “Palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pachokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu ogwidwa ndi mzimu woyera analankhula.”

      ◼ Ulosi: Yes. 44:24, 27, 28; 45:1-4: “Yehova . . . amene nditi kwa nyanja yakuya, Iphwa, ndipo ndidzaumitsa nyanja zako; ndi kunena za Koresi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzachita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kachisi, Maziko ake adzaikidwa. Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Koresi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, ndipo ndidzamasula m’chuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pake ndi zipata sizidzatsekedwa: ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzathyolathyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapichi achitsulo . . . chifukwa cha Yakobo mtumiki wanga ndi Israyeli wosankhidwa wanga; ndakuwonjezera dzina.” (Kulemba kwa Yesaya komalizidwa pafupifupi 732 B.C.E.)

      ◻ Kukwaniritsidwa: Koresi anali asanabadwe pamene ulosiwu unalembedwa. Ayuda anali asanatengeredwe kuundende ku Babulo kufikira 617-607 B.C.E., ndipo Yerusalemu ndi kachisi wake zinali zisanawonongedwe kufikira 607 B.C.E. Ulosiwo unakwaniritsidwa mokwanira kuyambira mu 539 B.C.E. Koresi anapatutsa madzi a Mtsinje wa Firate kukhala nyanja yokumba, zipata za kumtsinje wa Babulo zinasiyidwa zotseguka mosasamala mkati mwa nthaŵi yamadyerero mumzindawo,

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena