Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 117
  • Ululu m’Mundamo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ululu m’Mundamo
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Kupsyinjika Mtima m’Munda
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Anapemphera Pamene Anali ndi Chisoni Kwambiri
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Tsiku Lomaliza la Moyo Waumunthu wa Yesu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kukonzekeretsa Atumwi Kaamba ka Kuchoka Kwake
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 117

Mutu 117

Ululu m’Mundamo

PAMENE Yesu akutsiriza kupemphera, iye ndi atumwi ake okhulupirika 11 akuimba nyimbo zotamanda Yehova. Ndiyeno akutsika kuchokera m’chipinda chapamwambacho, natulukira mumdima wozizirira wa usiku, nabwereranso kupyola Chigwa cha Kidroni kumka cha ku Betaniya. Koma ali m’njira, iwo akuima pamalo okondeka, munda wa Getsemane. Umenewu uli pa kapena m’dera la Phiri la Azitona. Kaŵirikaŵiri Yesu wakumana ndi atumwi ake munomo pakati penipeni pa mitengo ya azitona.

Atasiya asanu ndi atatu a atumwiwo—mwinamwake pafupi ndi pachipata cha mundawo—akuwalangiza kuti: “Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.” Pamenepo iye amka ndi atatuwo—Petro, Yakobo, ndi Yohane—napita nawo mkati mwa mundawo. Yesu akumva chisoni ndipo ngwovutika maganizo kwambiri. “Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa,” iye akuwauza. “Khalani pano muchezere pamodzi ndi ine.”

Atapita patsogolo pang’ono, Yesu akugwera pansi ndipo nkhope yake italoza pansi ayamba kupemphera mwaphamphu. “Atate, ngati nkotheka, chikho ichi chindipitilire ine; koma simonga ndifuna ine, koma inu.” Kodi iye akutanthauzanji? Kodi nchifukwa ninji iye ali “ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa”? Kodi iye akupeŵa chosankha chake cha kufa cha kugaŵira dipo?

Kutalitali! Yesu sakuchondelera kuti asaphedwe. Ngakhale lingaliro la kupeŵa imfa yopereka nsembe, loperekedwa panthaŵi ina ndi Petro, nlosakondweretsa kwa iye. Mmalomwake, iye akuvutika maganizo chifukwa chakuti akuwopa kuti njira imene adzafa nayo mwamsanga—monga mpandu wokakala—idzadzetsa chitonzo padzina la Atate wake. Tsopano iye akuzindikira kuti m’maola oŵerengeka adzapachikidwa pamtengo wozunzirapo monga munthu woipitsitsa—wochitira mwano Mulungu! Kwakukulukulu chimenechi ndicho chimene chikumvutitsa maganizo.

Atapemphera kwanthaŵi yaitali, Yesu akubwerera ndi kupeza atumwi atatuwo atagona. Polankhula ndi Petro, iye akuti: “Nkutero kodi, simukhoza kuchezera ndi ine mphindi imodzi? Chezerani ndi kupemphera kuti, mungaloŵe m’kuyesedwa.” Komabe, povomereza, chitsenderezo chimene iwo akhala nacho ndi kuti npakati pa usiku, iye akuti: “Mzimutu uli wakufuna, koma thupi liri lolefuka.”

Ndiyeno Yesu amkanso kachiŵiri ndi kupempha kuti Mulungu achotse “chikho ichi,” ndiko kuti gawo limene anagaŵiridwa ndi Yehova, kapena chifuniro. Pamene iye abwerera, kachiŵirinso akupeza atatuwo atagona pamene akanayenera kukhala akupemphera kuti asaloŵe m’chiyeso. Pamene Yesu akulankhula kwa iwo, iwo akungokhala chete.

Potsirizira pake, nthaŵi yachitatu, Yesu akupita, pamtunda wotalikirapo, ndipo atagwada, ndi kufuula mwamphamvu ndi misozi, iye akupemphera kuti: “Atate, mukafuna inu, chotsani chikho ichi pa ine.” Yesu akumvadi ululu waukulu chifukwa cha chitonzo chimene imfa yake monga mpandu idzadzetsa padzina la Atate wake. Eya, kuweruzidwa monga wochitira mwano—munthu amene amatemberera Mulungu—kuli pafupifupi kosapilirika!

Mosasamala kanthu za zimenezo, Yesu akupitirizabe kupemphera kuti: “Sichimene ndifuna ine, koma chimene mufuna inu.” Yesu momvera akugonjetsera chifuniro cha Mulungu. Pamenepo, mngelo wakumwamba akuwonekera ndi kumchirikiza ndi mawu ena olimbikitsa. Mwachiwonekere, mngeloyo akuuza Yesu kuti iye ali ndi chivomerezo cha Atate wake.

Komabe, ndithayo lolemetsa chotani nanga pamapeŵa a Yesu! Moyo wake wa iye mwini wosatha ndi wa fuko lonse la anthu walenjekeka m’malere. Chitsenderezo cha malingaliro amkatikati nchachikulu koposa. Chotero Yesu akupitiriza kupemphera ndi phamphu koposerapo, ndipo thukuta lake likunga madontho a magazi pamene likugwera pansi. “Ngakhale kuti chimenechi chiri chochitika cha kamodzikamodzi kwambiri,” ikutero The Journal of the American Medical Association, “thukuta la magazi . . . lingawonekere m’mikhalidwe ya kupsinjika maganizo amkatikati.”

Pambuyo pake, Yesu akubwereranso kachitatu kwa atumwi ake, ndipo kachiŵirinso akuwapeza iwo atagona. Iwo atopa ndi kumva chisoni chokulirapo. “Gonani tsopano, nimupumule;” iye akudzuma motero. “Chakwanira, yafika nthaŵi; Wonani mwana wa munthu aperekedwa m’manja mwa anthu ochimwa! Ukani, tizimuka; wonani! wakundiperekayo ali pafupi.”

Ali chilankhulire, Yudase Isikariote akuyandikira, limodzi ndi khamu lalikulu lonyamula miyuni ndi nyali ndi zida. Mateyu 26:30, 36-47; 16:21-23; Marko 14:26, 32-43; Luka 22:39-47; Yohane 18:1-3; Ahebri 5:7.

▪ Atachoka m’chipinda chapamwamba, kodi nkuti kumene Yesu akutsogolera atumwiwo, ndipo kodi akuchitanji kumeneko?

▪ Pamene Yesu akupemphera, kodi atumwiwo akuchitanji?

▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akumva ululu, ndipo kodi akupanga pempho lotani kwa Mulungu?

▪ Kodi nchiyani chimene chikusonyezedwa ndi thukuta la Yesu kukhala monga madontho a magazi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena