Mutu 112
Paskha Womalizira wa Yesu Wayandikira
PAMENE lachiŵiri, Nisani 11, liri pafupi kutha, Yesu akumaliza kuphunzitsa atumwi pa Phiri la Azitona. Lakhala tsiku lotanganitsidwa, lantchito yakalavulagaga chotani nanga! Tsopano, mwinamwake pamene akubwerera ku Betaniya kukagona kumeneko, akuuza atumwi ake kuti: ‘Mudziŵa kuti akapita masiku aŵiri kuyambira tsopano paskha adzafika, ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa ndi kupachikidwa.’
Mwachiwonekere Yesu akuthera tsiku lotsatira, Lachitatu, Nisani 12, akupuma m’malo achete ndi atumwi ake. Patsiku lapitalo, anadzudzula atsogoleri achipembedzo poyera, ndipo akuzindikira kuti iwo akufunafuna kumupha. Chotero pa Lachitatu sakuwonekera poyera, pakuti safuna kuti kanthu kalikonse kadodometse kusunga kwake Paskha ndi atumwi ake madzulo otsatirawo.
Pakali pano, akulu ansembe ndi akulu ena a anthu asonkhana m’bwalo la mkulu wansembe, Kayafa. Akuvutikabe maganizo chifukwa cha kudzudzulidwa ndi Yesu tsiku lapitalo, iwo akulinganiza kumgwira mwamachenjera ndi kumupha. Komabe iwo akupitirizabe kunena kuti: “Padzuŵa la chakudya iyayi, kuti pasakhale phokoso la anthu.” Iwo akuwopa anthu, amene amayanja Yesu.
Pamene mwankhalwe atsogoleri achipembedzowo akulinganiza chiŵembu cha kupha Yesu, iwo akulandira mlendo. Mowadabwitsa, iye ndiye mmodzi wa atumwi a Yesu mwini, Yudase Isikariote, mwa amene Satana waika lingaliro loipa la kupereka Mbuye wake! Ngosangalala chotani nanga pamene Yudase akuwafunsa kuti: “Mufuna kundipatsa chiyani, ndipo ine ndidzampereka iye kwa inu?” Mokondwera iwo akuvomerezana kumlipira ndalama 30 zasiliva, mtengo wogulira kapolo malinga ndi pangano Lachilamulo cha Mose. Kuyambira pamenepo kumkabe mtsogolo, Yudase akufunafuna mpata wabwino woperekera Yesu kwa iwo popanda khamu pafupi.
Nisani 13 akuyamba pakuloŵa kwa dzuŵa pa Lachitatu. Yesu anafika kuchokera ku Yeriko pa Lachisanu, chotero uwu ndiwo usiku wachisanu ndi chimodzi womalizira ali m’Betaniya. Tsiku lotsatira, Lachinayi, makonzedwe omalizira a Paskha adzafunikira kupangidwa, amene amayamba pakuloŵa kwa dzuŵa. Ndiko kuti pamene mwana wa nkhosa wa Paskha ayenera kuphedwa ndiyeno kuwotchedwa wathunthu. Kodi iwo adzachitira kuti phwandolo, ndipo kodi ndani amene adzachita makonzedwewo?
Yesu sanapereke malangizo otero, mwinamwake kuti alepheretse Yudase kudziŵitsa akulu ansembe amene angagwire Yesu mkati mwa kuchita phwando la Paskha. Koma tsopano, mwinamwake kuchiyambiyambi kwa masana a Lachinayi, Yesu akutumiza Petro ndi Yohane kuchokera ku Betaniya, akumati: “Pitani mutikonzere ife Paskha, kuti tidye.”
“Mufuna tikakonzere kuti?” iwo akufunsa motero.
“Mutaloŵa m’mudzi,” Yesu akufotokoza motero, “adzakomana ndinu munthu alikusenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akaloŵako iye. Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Chipinda cha alendo chiri kuti, mmene ndikadye Paskha pamodzi ndi ophunzira anga? Ndipo iyeyo adzakuwonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokonzeka; mukakonzere kumeneko.”
Mosakayikira mwini nyumbayo ali wophunzira wa Yesu amene mwinamwake akuyembekezera pempho la Yesu la kugwiritsira ntchito nyumba yake kaamba ka chochitika chapadera chimenechi. Chotero, pamene Petro ndi Yohane afika m’Yerusalemu, akupeza zonse monga momwedi Yesu ananenera. Chotero aŵiriwo akutsimikizira kuti mwana wa nkhosa wakonzedwa ndi kuti makonzedwe ena onse akupangidwa kaamba ka kusamalira ochita Paskha okwanira 13 amenewo, Yesu ndi atumwi ake 12. Mateyu 26:1-5, 14-19; Marko 14:1, 2, 10-16; Luka 22:1-13; Eksodo 21:32.
▪ Kodi mwachiwonekere Yesu akuchitanji pa Lachitatu, ndipo chifukwa ninji?
▪ Kodi ndimsonkhano wanji umene ukuchitidwa kunyumba ya mkulu wansembe, ndipo kuli kaamba ka chifuno chotani kuti Yudase afike kwa atsogoleri achipembedzo?
▪ Kodi Yesu akutumiza yani kupita ku Yerusalemu pa Lachinayi, ndipo kaamba ka chifuno chotani?
▪ Kodi otumidwawo akupezanji chimene kachiŵirinso chikuvumbula mphamvu zozizwitsa za Yesu?