Mutu 8
‘Kulimbana ndi Makamu a Mizimu Yoipa’
1. Kodi nchifukwa ninji zochita za mizimu yoipa ziri zokondweretsa mwapadera kwa ife?
ANTHU a maganizo okondetsa zakuthupi angaseke lingaliro lamizimu yoipa. Komatu siiri nkhani yoseketsa. Kaya iwo akuzikhulupirira kapena ayi, zochita za ziwanda zikutsendereza aliyense. Olambira a Yehova sakusiyidwa. Kunena zowona iwo ndiwo chandamale chachikulu. Mtumwi Paulo akutichenjeza za nkhondoyi, kuti: “Tiri ndi nkhondo, osati yomenyana ndi mwazi ndi thupi, koma yomenyana ndi maboma [amene ali m’gawo lokhala amwazi ndi thupi], yomenyana ndi olamulira, yomenyana ndi olamulira adziko a mdima uno, yomenyana ndi makamu a mizimu yoipa mmalo akumwamba.” (Aef. 6:12) M’tsiku lathu chitsenderezo chafika pachimake chifukwa chakuti Satana wachotsedwa kumwamba ndipo ali wokwiya, akumadziwa kuti nthawi yake njayifupi.—Chiv. 12:12.
2. Kodi nkotheka bwanji kwa ife kulimbana mwachipambano ndi mizimu yoposa anthu?
2 Kodi ndimotani mmene mothekera yense waife angapezere chipambano m’nkhondo yomenyana ndi makamu amizimu? Kuli kokha mwa kudalira kotheratu pa Yehova. Tiyenera kumvetsera ndi kulabadira Mawu ake. Mwakutero, tingapulumuke chivulazo chakuthupi, chamakhalidwe, chamalingaliro ndi chamaganizo, chachisonkhezero chimene chimakhala ndi awo olamulidwa ndi Satana.—Aef. 6:11; Yak. 4:7.
Olamulira Adziko Mmalo a m’Mwamba
3. Kodi Satana akutsutsa mwankhalwe chiyani ndipo yani?
3 Yehova akutilongosolera momvekera bwino mkhalidwe wadziko monga momwe akuwonera kuchokera pamalo apatali m’miyamba. Anapatsa mtumwi Yohane masomphenya mu amene Satana analongosoledwa monga “chinjoka chofiira, chachikulu” chokonzekera kulikwira, ngati kutheka, Ufumu Waumesiya wa Mulungu mwamsanga pamene ukabadwa m’mwamba mu 1914. Atalephera mu zimenezo Satana anatulutsa motsutsana ndi oyimira owoneka a Ufumu umenewo, mbali yachiwiri yambewu ya “mkazi,” wa Mulungu liyambwe la chitsutso chankhalwe.—Chiv. 12:3, 4, 13, 17.
4. (a) Kodi Baibulo limatichenjeza za chenicheni chotani ponena za maziko amphamvu ya maboma aumunthu? (b) Kodi olamulira onse andale zadziko tsopano akusonkhanitsidwira kuchiyani, ndipo ndiyani?
4 Magwero amphamvu ndi ulamuliro wa maboma aumunthu anaululidwanso m’chivumbulutso chimenecho kwa Yohane. Anasonyezedwa chilombo cha mbali zingapo, cha mitu 7 ndi nyanga 10, chirombo chokhala ndi ulamuliro “pafuko lirilonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.” Ichi chikuimira, osati boma limodzi lokha, koma dongosolo landale zadziko ladziko lonse. Yohane anauzidwa kuti “chinjoka [Satana Mdyerekezi] chinapatsa chilombocho mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.” (Chiv. 13:1, 2, 7; yerekezerani Luka 4:5, 6.) Mosasamala kanthu za kudzitcha kukhala achipembedzo kwa olamulira andale zadziko, palibe aliyense wa chiwalo chamitundu ya “chirombo” akugonjera ku ulamuliro wa Yehova ndi kwa Mfumu yake yoikidwa, Yesu Kristu. Iwo onse akumenyera kusungabe ulamuliro wa wo. Lerolino, monga momwe Chivumbulutso chikusonyezera, “mizimu youziridwa ndi ziwanda” ikuwasonkhanitsira onse ku “nkhondo yatsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pa Harmagedo. (Chiv. 16:13, 14, 16) Ndithudi, monga momwe mtumwi Paulo analembera, “olamulira adziko” saali kokha anthu wamba koma “makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” (Aef. 6:12) Onse amene angadzitsimikizire kukhala olambira owona a Yehova afunikira kuzindikira tanthauzo lokwanira lachimenecho.
5. Kodi nchifukwa ninji chisamaliro chiri chofunika kuti tipewe kuchititsidwa kulowa m’kuchirikiza dongosolo la Satana?
5 Tsiku lirilonse miyoyo yathu ikukhudzidwa ndi nkhondo zimene zimagawanitsa anthu onse. Kuli kofala kwa anthu kugwirizana, mwa mawu kapena mwanjira ina, ndi mitundu, mafuko, kagulu ka chinenero kapena kagulu ka anthu kamene iwo ali mbali yake. Ngakhale pamene gawo lakutilakuti la anthuwo silikuphatikizidwa mwachindunji m’nkhondo yapanthawiyo, iwo angadzipeze iwo eni a kuyanja gulu limodzi koposa lina. Koma mosasamala kanthu za chimene dandaulolo lingakhale, mosasamala kanthu za munthu kapena chimene amavomereza, kodi iwo kwenikweni akuchirikiza chiyani? Baibulo limalongosola momvekera bwino kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) Pamenepa, kodi ndimotani, mmene munthu angapewere kusokeretsedwa limodzi ndi ena onse a amtundu wa anthu? Kokha mwa kupereka chichirikizo chodzala ku Ufumu wa Mulungu ndi kusunga uchete wotheratu ponena za nkhondo za pakati pamagulu adziko.—Yoh. 17:15, 16.
Machenjera Onyenga a Woipayo
6. Kodi pakati pa njira zimene Satana wagwiritsira ntchito kupatutsa anthu kuchoka kukulambira kowona paphatikizapo ziti?
6 Panyengo yonse ya m’mbiri Satana wagwiritsira ntchito chizunzo cha mawu ndi chathupi kutembenuza anthu kuchoka ku kulambira kowona. Koma iye wagwiritsiranso ntchito njira zamachenjera kwambiri—machitachita authyali ndi njira zobisika.
7. Kodi ndimotani mmene machenjera a Satana asonyezedwera m’kugwiritsira ntchito kwake chipembedzo chonyenga?
7 Mochenjera wachititsa gawo lalikulu la anthu kukhalabe mu mdima kupyolera mwachipembedzo chonyenga, akumawachititsa kuganiza, ngati iwo akufuna kutero, kuti akutumikira Mulungu. Popanda chikondi chowona kaamba ka chowonadi, iwo angakopedwe ndi mautumiki achipembedzo achinsinsi ndi otengeka maganizo kapena kuchititsa chidwi ndi ntchito zamphamvu. (2 Ates. 2:9, 10) Koma tikuchenjezedwa kuti, ngakhale pakati pa awo amene anatenga mbali m’kulambira kowona, “ena adzataya chikhulupiriro . . . kusamala mizimu yosokeretsa ndi maphunziro a ziwanda.” (1 Tim. 4:1) Kodi izi zingachitike motani?
8. Kodi ndimotani mmene Satana wakopera ngakhale ena amene anali kulambira Yehova kulowa m’chipembedzo chonyenga?
8 Mwa machenjera Mdyerekezi amasonkhezera zo-fooka zamunthu. Kodi akali chigwidwire ndi kuopa anthu? Ngati ziri choncho, iye angagonjere chipsinjo chochokera kwa achibale kapena anansi cha kugwirizana nawo m’machitachita amene anayambira m’chipembedzo chonyenga. Kodi munthuyu ngwonyada? Pamenepo iye angakhumudwe pamene apatsidwa uphungu kapena pamene ena sakuvomereza malingaliro amene iye amawachirikiza (Miy. 29:25; 15:10; 1 Tim 6:3, 4) Bwanji ngati kutenga mbali kwake mu utumiki wakumunda sikukusonkhezeredwa ndi chikondi? M’malo mwa kusintha lingaliro lake kugwirizana ndi chitsanzo cha Kristu, iye angakhoterere kwa awo amene ‘amakolokosa makutu ake’ mwa kunena kuti kungowerenga kokha Baibulo ndi kukhala ndi “moyo wabwino” nzokwanira. (2 Tim. 4:3) Kaya iye akugwirizana kwenikweni ndi gulu lina lachipembedzo kapena kungokhala kokha ndi mtundu wa iye mwini wa chipembedzo ziribe kanthu kwa Satana, malinga ngati iye sakulambira Yehova mwanjira imene Yehova akusonyeza kupyolera mwa Mawu ake ndi gulu lake.
9. Kodi ndimotani mmene Satana mwachinyengo akugwiritsirira ntchito kugonana kukwaniritsa zolinga zake?
9 Mwa machenjera Satana wakopanso anthu kukhutiritsa zikhumbo zawo zachibadwa mwanjira zolakwa. Iye wachita ichi ndi chikhumbo cha maubwenzi m’zakugonana. Pokana chiphunzitso cha Baibulo cha khalidwe labwino, ochuluka m’dziko amawona kugonana pakati pa anthu osakwatirana monga chikondwerero choyenera mwalamulo kapena monga njira yotsimikizira kuti iwo ali achikulire. Ndipo bwanji ponena za anthu okwatirana? Sikwachilendo kwa anthu audziko okhala ndi mavuto a ukwati kusudzulana ndi kukwatiranso kapena kungolekana ndi kukhala ndi mnzawo wina. Pamene tiwona njira iyi yamoyo, kodi timamva kuti tikutaikiridwa ndi kanthu kena, kuti njira Yachikristu iri yoletsa mopambanitsa? Mchitidwe wa machenjera wa Satana ndiwo kuchititsa munthu kuganiza kuti Yehova akummana kanthu kena kabwino. Amatichirikiza kuganiza za chikondwerero chimene tingakhale nacho tsopano—osati chiyambukiro cha nthawi yaitali pa ife eni ndi ena, ndipo ndithudi osati paunansi wathu ndi Yehova ndi Mwana wake.—Agal. 6:7, 8; 1 Akor. 6:9, 10.
10. Kodi Satana akuyesa mwanjira iti kukhotetsera malingaliro athu kulinga ku chiwawa?
10 Chikhumbo china chachibadwa chiri cha zosangulutsa. Pamene chiri chabwino, chingakhale chotsitsimula mwakuthupi, mwamaganizo ndi chisonkhezero. Koma kodi kachitidwe kathu ndikotani pamene Satana mochenjera agwiritsira ntchito nyengo za kusanguluka kuyesa kuchititsa maganizo anthu kutalikirana ndi a Mulungu? Mwachitsanzo, tidziwa, kuti Yehova amada anthu okonda chiwawa. (Sal. 11:5) Koma pamene zithunzi zosonyezedwa patelevizheni kapena kunyumba yowonererera akanema azisonyeza, kodi timangokhala duu ndi kuwonerera zonse? Kapena pamene chisonyezedwa m’dzina lamasewero, kodi timachivomereza ndipo mwinamwake kufuula kuchemerera osewerawo?—Yerekezerani Genesis 6:13.
11. Kodi ndimwanjira ziti zimene ngakhale munthu wodziwa chowonadi chonena za kulankhula ndi mizimu angatcheredwere msampha ngati saali wogalamuka?
11 Tikuzindikiranso kuti awo ophatikizidwa mu mpangidwe uliwonse wa kukhulupirira mizimu—kuombeza, ufiti kapena kuyesa kulankhula ndi akufa—ali “onyansa kwa Yehova.” Ife sitikanaganiza za kufunsira kwa obwebweta ndipo ndithudi sitingawavomereze kudza m’nyumba mwathu kudzachitiramo machitachita awo a ziwanda. Koma kodi tikawamvetsera ndi kuwawonerera mwachidwi ngati anawonekera patelevizheni yathu? Ngakhale kuli kwakuti sitikanalola kulandira mankhwala a sing’anga, kodi tingamangirire kachingwe pamkono wa khanda lobadwa chatsopano ndi lingaliro lakuti mwanjira yakutiyakuti kangatetezere mwanayo ku chivulazo? Kapena, podziwa kuti Baibulo limatsutsa ‘kuchesa ena,’ kodi ife tikanalola munthu wamatsenga kulamulira maganizo athu, ngakhale kwakanthawi?—Deut. 18:10, 12; Agal. 5:19-21.
12. (a) Kodi ndimotani mmene nyimbo zagwiritsidwira ntchito kutichititsa kukondwera ndi malingaliro amene timadziwa kuti ngolakwa? (b) Kodi ndimotani mmene zovala zamunthu, mapesedwe a tsitsi kapena malankhulidwe zingasonyezere kukhumbira kwake awo okhala ndi kakhalidwe kosavomerezeka ndi Yehova? (c) Kodi chofunika nchiyani ku mbali yathu ngati titi tipewe kukhala okodwa ndi machitachita a machenjera ausatana?
12 Tawerenga m’Malemba kuti ‘dama ndi chidetso chonse, limodzi ndi maganizo osayenera, zisatchulidwe konse pakati pathu.’ (Aef 5:3-5) Koma bwanji ngati mitu yankhani imeneyi mwanzeru yagwirizanitsidwa ndi nyimbo zimene ziri ndi malimba okondweretsa, ndi mamvekedwe okoma kapena maliridwe osonkhezera? Kodi mwinamwake ife ngakhale mosazindikira tingayambe kubwereza nyimbo zimene zimatamanda kugonana popanda ukwati, kugwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa kaamba ka chikondwerero ndi zina zotero? Kapena, pamene tidziwa kuti tiyenera kutsanzira njira yamoyo ya anthu amene amachita zinthu zoterozo, kodi timakhoterera ku kudzichititsa kufanana nawo mwakutsanzira njira yawo ya kavalidwe, kapesedwe kawo ka tsitsi kapena kalankhulidwe kawo? Ha ndiwochenjera chotani nanga mmene Satana aliri! Ha ndizobisika chotani nanga mmene njira zake ziliri zimene iye amagwiritsira ntchito kunyenga anthu kugwirizana ndi maganizo ake oipa! (2 Akor. 4:3, 4) Kuti tisakhale okodwa m’machenjera ake onyenga, tiyenera kupewa kutengeka ndi dziko. Tifunikira kukumbukira amene “olamulira adziko lino lamdima” ali ndipo mwaphampu kulimbana motsutsana ndi chisonkhezero chawo.—Aef. 6:12; 1 Pet. 5:8.
Kukonzekeretsedwa Kukhala Olakika
13. Kodi ndimotani mmene kuliri kotheka kwa ife, ndi kupanda ungwiro kwathuku, kulaka dziko limene Satana akulamulira?
13 Imfa ya Yesu isanachitike iye anati kwa ophunzira ake: “Limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi ine.” Chotero, iwonso, akanakhala olakika; ndipo zaka zoposa 60 pambuyo pake mtumwi Yohane analemba kuti: “Koma ndani iye wolilaka dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu?” (Yoh. 16:33; 1 Yoh. 5:5) Chikhulupiriro chotere chimasonyezedwa mwa kumvera kwathu malamulo a Yesu ndi kudalira pa Mawu a Mulungu, monga momwedi iye anachitira. Kodi nchiyaninso chikufunika? Kuti tikhale pafupi ndi mpingo umene iye ali mutu wake. Pamene tilephera, tiyenera kulapa mowona mtima ndi kufunafuna chikhululukiro cha Mulungu pamaziko ansembe ya Yesu. Mwanjira iyi, mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwathu, nafenso tingakhale olakika.
14. (a) Werengani Aefeso 6:13-18. (b) Gwiritsirani ntchito mafunso ndi malemba operekedwa monga maziko okambitsiranira mapindu ochokera ku mbali iriyonse ya zida zankhondo zauzimu.
14 Kuti tipambane, tifunikira kuvala “zida zonse za Mulungu,” osanyalanyaza mbali yake iriyonse. Chonde tsegulani Baibulo lanu pa Aefeso 6:13-18 ndi kuwerenga kufotokoza kwake zida zimenezo. Pamenepo, mwa kuyankha mafunso ali pansipawa, lingalirani mmene mungapindulire ndi chitetezero choperekedwa ndi chirichonse cha zidazo.
“Mutadzimangira m’mchuuno mwanu ndi chowonadi”
Ngakhale kuli kwakuti tingadziwe chowonadi, kodi ndimotani mmene phunziro lokhazikika, kusinkhasinkha chowonadi cha Baibulo ndi kufika pamisonkhano kumatitetezera? (Afil 3:1; 4:8, 9; 1 Akor. 10:12, 13; 2 Akor. 13:5; 1 Pet. 1:13, Kingdom Interlinear)
“Chapachifuwa cha chilungamo”
Kodi umenewu uli muyeso wayani wachilungamo? (Chiv. 15:3)
Longosolani mwafanizo mmene kusamvera malamulo a Yehova, chifukwa cha kulephera kukulitsa kukonda njira zake, kungachititsire munthu kuvulala kwambiri mwauzimu. (Wonani 1 Samueli 15:22, 23; Deuteronomo 7:3, 4.)
“Mapazi atavekedwa makonzedwe a uthenga wabwino wamtendere”
Kodi nkotetezera motani kwa ife kuchititsa mapazi athu kukhala otanganitsidwa kutipititsa kukalankhula ndi anthu za makonzedwe a Mulungu amtendere? (Aroma 10:15; Sal. 73:2, 3; 1 Tim. 5:13)
“Chikopa chachikulu cha chikhulupiriro”
Ngati tiri ndi chikhulupiriro chokhazikika zolimba, kodi tidzatani titayang’anizana ndi zoyesayesa zimene zikufuna kutichititsa kukaikira kapena mantha? (Yerekezerani ndi 2 Timoteo 1:12; 2 Mafumu 6:15-17.)
“Chisoti cha chipulumutso”
Kodi ndimotani mmene chiyembekezo cha chipulumutso chimathandizira munthu kupewa kutcheredwa msampha ndi kudera nkhawa mopambanitsa ndi chuma chakuthupi? (1 Tim. 6:7-10, 19)
“Lupanga lamzimu”
Kodi nthawi zonse tiyenera kudalira pa chiyani polimbana ndi ziukiro zotsutsana ndi mkhalidwe wathu wauzimu kapena wa ena? (Sal. 119:98; Miy. 3:5, 6; yerekezerani ndi Mateyu 4:3, 4.)
Mogwirizana ndizimenezo, pa Aefeso 6:18, 19, kodi nchiyaninso chimene chasonyezedwa kukhala chofunika kuti tipambane m’nkhondo yauzimu? Kodi chiyenera kugwiritsiridwa ntchito mwakawirikawiri chotani? Kaamba ka chiyani?
15. (a) Kodi iri chabe nkhondo yauzimu ya munthu mwini imene ife tikumenya? (b) Kodi ndimotani mmene tingachitirepo kanthu m’nkhondoyo?
15 Monga asilikali Achikristu tiri mbali ya gulu lankhondo lalikulu limene likumenya nkhondo yauzimu. Ngati tikhala odikira ndi kugwiritsira ntchito bwino chovala chankhondo chathunthu chochokera kwa Mulungu, sitidzakhala ophedwa m’nkhondo iyi. M’malo mwake, tidzakhala chithandizo cholimbikitsa atumiki anzathu a Mulungu. Tidzakhala okonzekera ndi aphamphu kuchitapo kanthu, kufalitsa mbiri yabwino ya Ufumu Waumesiya wa Mulungu, bomalo limene Satana amalitsutsa mwachiwawa kwambiri.
Makambitsirano a Kupenda
● Kodi nchifukwa ninji olambira Yehova amayesayesa kusunga uchete kotheratu m’mikangano yokhala pakati pa anthu adziko?
● Kodi ndi ati amene ali ena a machenjera onyenga amene akugwiritsiridwa ntchito ndi Satana kuwonongera Akristu mwauzimu?
● Kodi ndimotani mmene zida zankhondo zoperekedwa ndi Mulungu ziimatitetezerera m’njira zimene ziri zofunika kwambiri m’nkhondo yauzimu imeneyi?