Mutu 122
Kuchokera kwa Pilato Kumka kwa Herode ndi Kubwereranso
NGAKHALE kuti Yesu sakuyesayesa kubisira Pilato kuti iye ndimfumu, akufotokoza kuti Ufumu wake suli chiwopsezo ku Roma. “Ufumu wanga suuli wadziko lino lapansi,” Yesu akutero. “Ufumu wanga ukadakhala wadziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suuli wochokera konkuno.” Chotero Yesu akuvomereza katatu kuti iye ali ndi Ufumu, ngakhale kuti suli wamagwero adziko lapansi.
Komabe, Pilato akupitirizabe kumfunsa kuti: “Nanga kodi ndiwe mfumu?” Ndiko kuti, kodi ndiwe mfumu ngakhale kuti Ufumu wako suli mbali yadziko lino?
Yesu akuchititsa Pilato kudziŵa kuti walondola, mwakuyankha kuti: “Munena kuti ndine mfumu. Ndanabadwira ichi ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi chowonadi. Yense wakukhala mwa chowonadi amva mawu anga.”
Inde, chifuno chenicheni cha kufika kwa Yesu padziko lapansi ndicho kuchitira umboni “chowonadi,” makamaka chowonadi chonena za Ufumu wake. Yesu ali wokonzekera kukhala wokhulupirika ku chowonadi chimenecho ngakhale ngati kungamtayitse moyo wake. Ngakhale kuti Pilato akufunsa kuti: “Chowonadi nchiyani?” iye sakuyembekezera mafotokozedwe ena owonjezereka. Iye wamva zokwanira kuti apereke chiŵeruzo.
Pilato akubwerera kukhamu loyembekezera kunja kwa pretorio. Mwachiwonekere Yesu ali pandunji pake, iye akuuza akulu ansembe ndi awo amene iwo ali nawo kuti: “Ine sindipeza konse chifukwa mwa iye.”
Atakwiya ndi chosankhacho, makamuwo akuyamba kuumirira kuti: “Amautsa anthuwo, naphunzitsa mu Yudeya lonse, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.”
Kutengeka maganizo kosalingalira kwa Ayuda kuyenera kuzizwitsa Pilato. Chotero, pamene akulu ansembe ndi akulu ena akupitirizabe kufuula, Pilato akutembenukira kwa Yesu nafunsa kuti: “Sukumva kodi zinthu zambiri zotere akunenera iwe?” Komabe, Yesu akhala chete. Kukhala kwake chete pamaso pazinenezo zabodza lamkunkhuniza kukuchititsa Pilato kuzizwa.
Podziŵa kuti Yesu ngwa ku Galileya, Pilato akuwona njira yopeŵera thayo pa iye. Wolamulira wa ku Galileya, Herode Antipa (mwana wa Herode Wamkulu), ali mu Yerusalemu kaamba ka Paskha, chotero Pilato akutumiza Yesu kwa iye. Nthaŵi yochepekera yapitayo, Herode Antipa anachititsa Yohane Mbatizi kudulidwa mutu, ndiyeno Herode anachita mantha pamene anamva za ntchito zozizwitsa zimene Yesu anali kuchita, akumawopa kuti Yesu kwenikweni anali Yohane amene anauka kwa akufa.
Tsopano, Herode akukondwera kwambiri pokhala ndi chiyembekezo cha kuwona Yesu. Izi siziri chifukwa cha kudera nkhaŵa ndi ubwino wa Yesu kapena kuti akufuna kupanga kuyesayesa kowona kulikonse kuti adziŵe ngati zinenezo zotsutsa Yesu ziri zowona kapena ayi. Mmalomwake, iye ali ndi chidwi chabe ndi ziyembekezo za kuwona Yesu akuchita chozizwitsa.
Komabe, Yesu, akukana kukhutiritsa maganizo a Herode. Kwenikweni, pamene Herode akumfunsa, akukhala chete. Atagwiritsidwa mwala, Herode ndi asilikali ake olonda akuseka Yesu. Akuveka Yesu chovala choyera ndi kumserewula. Pamenepo akumbwezera kwa Pilato. Monga chotulukapo, Herode ndi Pilato amene kale anali adani, akufikira kukhala mabwenzi.
Pamene Yesu abwerera, Pilato akuitana akulu ansembe, oweruza Achiyuda, ndi anthu pamodzi nanena kuti: “Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo tawonani, ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeze pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mumnenera; inde, ngakhale Herode yemwe; pakuti iye anambwezera iye kwa ife; ndipo tawonani, sanachita iye kanthu kakuyenera kufa. Chifukwa chake ndidzamkwapula ndi kummasula iye.”
Chotero Pilato akulengeza Yesu kaŵiri kuti ali wopanda liwongo. Iye ali wofunitsitsa kummasula, pakuti akuzindikira kuti kuli kokha chifukwa cha njiru kuti ansembe ampereka. Pamene Pilato akupitirizabe kuyesa kumasula Yesu, akulandira chisonkhezero champhamvu kwambiri cha kutero. Pamene ali pampando wake wakuŵeruza, mkazi wake akutumiza uthenga kumsokhezera kuti: “Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo, pakuti lero m’kulota ine [mwachiwonekere kochititsidwa ndi Mulungu] ndasauka kwambiri chifukwa cha iye.”
Komabe, kodi ndimotani mmene Pilato angamasulire mwamuna wosalakwa ameneyu, monga momwe akudziŵira kuti ayenera kutero? Yohane 18:36-38; Luka 23:4-16; Mateyu 27:12-14, 18, 19; 14:1, 2; Marko 15:2-5.
▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akuyankhira funso lonena za kukhala kwake mfumu?
▪ Kodi nchiyani chimene chiri “chowonadi” chimene Yesu anathera moyo wake akuchichitira umboni padziko lapansi?
▪ Kodi chiŵeruzo cha Pilato nchotani, kodi anthu akuchita motani, ndipo kodi Pilato akuchitanji ndi Yesu?
▪ Kodi Herode Antipa anali yani, kodi nchifukwa ninji anakondwera kwambiri kuwona Yesu, ndipo kodi iye anachitanji naye?
▪ Kodi nchifukwa ninji Pilato ali wofunitsitsa kumasula Yesu?