Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 113
  • Kudzichepetsa pa Paskha Womalizira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudzichepetsa pa Paskha Womalizira
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Kudzichepetsa pa Paskha Womalizira
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Anawaphunzitsa Kudzichepetsa pa Pasika Womaliza
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Munthu Wamkulu Koposa Onse Achita Utumiki Wodzichepetsa
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Paskha Womalizira wa Yesu Ali Pafupi
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 113

Mutu 113

Kudzichepetsa pa Paskha Womalizira

PETRO ndi Yohane, molangizidwa ndi Yesu, afika kale ku Yerusalemu kukapanga makonzedwe a Paskha. Yesu, mwachiwonekere limodzi ndi atumwi ena khumi, akufika pambuyo pake madzulowo. Dzuŵa likuloŵa pamonekera pamene Yesu ndi kagulu kake akutsika Phiri la Azitona. Kumeneku kuli kuwona mzindawo masana komalizira kwa Yesu kuchokera paphirili kufikira pambuyo pa chiukiriro chake.

Mwamsanga Yesu ndi kagulu kake akufika mumzindawo ndipo akupita kunyumba kumene adzachitira Paskha. Iwo akukwera makwerero omka kuchipinda chachikulu chapamwamba, kumene akupeza makonzedwe onse atapangidwira kuchita kwawo mtseri Paskhayo. Yesu wakhala akuyang’anira m’tsogolo ku chochitikachi, monga momwe akunenera kuti: “Ndinalakalaka ndithu kudya Paskha uwu pamodzi ndinu, ndisanayambe kusautsidwa.”

Mwamwambo, ochita Paskha ankafunikira kumwa zikho zinayi za vinyo. Atalandira chimene mwachiwonekere chiri chikho chachitatu, Yesu akuyamika nati: “Landirani ichi, muchigaŵane mwa inu nokha; pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano ine sindidzamwako chipatso cha mpesa, kufikira ufumu wa Mulungu udzafika.”

Panthaŵi ina mkati mwa chakudyacho, Yesu akunyamuka, navula chovala chake chakunja, akutenga thaulo, nadzadza beseni ndi madzi. Mwachizoloŵezi, wochereza ankatsimikizira kuti mapazi a alendo asambitsidwa. Koma pakuti pachochitikachi palibe wochereza, Yesu akuchita utumiki umenewu iye mwini. Aliyense wa atumwiwo akanatenga mwaŵi wa kutero; komabe, mwachiwonekere chifukwa chakuti mkangano wakutiwakuti udakalipobe pakati pawo, palibe amene akutero. Tsopano iwo akuchita manyazi pamene Yesu akuyamba kusambitsa mapazi awo.

Pamene Yesu akufika pa Petro, iye akukana kuti: “Simudzasambitsa mapazi anga kunthaŵi yonse.”

“Ngati sindikusambitsa iwe ulibe cholandira pamodzi ndi ine,” Yesu akutero.

“Ambuye,” Petro akuyankha motero, “simapazi anga okha, komanso manja ndi mutu.”

“Amene anatha kusamba,” Yesu akuyankha, “alibe kusoŵa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma sinonse ayi.” Iye akunena izi chifukwa akudziŵa kuti Yudase Isikariote akulinganiza kumpereka.

Yesu atasambitsa mapazi a 12 onsewo, kuphatikizapo mapazi a wompereka, Yudase, iye akuvala chovala chake chakunja naseyama pagome kachiŵirinso. Pamenepo akufunsa kuti: “Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi? Inu munditcha ine Mphunzitsi ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene. Chifukwa chake, ngati ine Ambuye ndi mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake. Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga ine ndakuchitirani inu, inunso muchite. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Kapolo saali wamkulu ndi mbuye wake; kapena mtumwi saali wamkulu ndi womtuma iye. Ngati mudziŵa izi, odala inu ngati muzichita.”

Ndiphunziro labwino kwambiri chotani nanga la utumiki wodzichepetsa! Atumwiwo sayenera kufunafuna malo oyamba, akumaganiza kuti iwo ngofunika koposa kuti nthaŵi zonse ena ayenera kuwatumikira. Iwo afunikira kutsatira chitsanzo choperekedwa ndi Yesu. Kumeneku sindiko mbali ya dzoma la kusambitsa mapazi. Ayi, koma kuli mbali ya kufunitsitsa kutumikira mopanda tsankho, mosasamala kanthu za mmene ntchitoyo ingakhalire yosanunkha kanthu kapena yosakondweretsa. Mateyu 26:20, 21; Marko 14:17, 18; Luka 22:14-18; 7:44; Yohane 13:1-17.

▪ Kodi nchiyani chimene chiri chapadera ponena za kuwona Yerusalemu kwa Yesu pamene akuloŵa mumzindawo kukachita Paskha?

▪ Mkati mwa Paskhayo, kodi ndichikho chiti mwachiwonekere chimene Yesu akupereka kwa atumwi 12 atatha kuyamika?

▪ Kodi ndiutumiki waumwini wotani umene mwamwambo unachitidwira alendo pamene Yesu anali padziko lapansi, ndipo nchifukwa ninji sukuperekedwa mkati mwa kuchitidwa kwa Phwando la Paskha kwa Yesu ndi atumwiwo?

▪ Kodi chifuno cha Yesu pochita utumiki wotsika wa kusambitsa mapazi a atumwi ake chinali chotani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena