Mutu 55
Ophunzira Ambiri Aleka Kutsatira Yesu
YESU akuphunzitsa m’sunagoge wa m’Kapernao ponena za mbali yake monga mkate wowona wochokera kumwamba. Mwachiwonekere nkhani yake yachokera m’kukambitsirana kumene kunayambidwa ndi anthu pamene iwo anampeza atachokera kumbali ya kummaŵa kwa Nyanja ya Galileya, kumene adadya mitanda ndi nsomba zoperekedwa mozizwitsa.
Yesu akupitirizabe mawu ake, kumati: “Mkate umene ndidzapatsa ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.” Zaka ziŵiri zokha zapitazo, m’ngululu ya 30 C.E., Yesu anauza Nikodemo kuti Mulungu anakonda dziko kwambiri kotero kuti anapereka Mwana wake monga Mpulumutsi. Motero, Yesu tsopano akusonyeza kuti aliyense wa dziko la anthu amene amadya mophiphiritsira thupi lake, mwa kusonyeza chikhulupiliro m’nsembe imene iye ali pafupi kupereka, angalandire moyo wosatha.
Komabe, anthuwo, akukhumudwa ndi mawu a Yesu. “Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake?” iwo akufunsa motero. Yesu akufuna kuti omvetsera ake azindikire kuti kudyedwa kwa thupi lake kukachitika mwanjira yophiphiritsira. Chotero, kuti agogomezere mfundoyi, iye akunena kanthu kena kamene kalinso kosavomerezeka kwambiri ngati kalingaliridwa mwanjira yeniyeni.
“Ngati simukadya thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa mwazi wake,” Yesu akutero, “mulibe moyo mwa inu nokha. Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha; ndipo ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza. Pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu. Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa ine, ndi ine mwa iye.”
Ndithudi, chiphunzitso cha Yesu chikamvekera kukhala chokhumudwitsa kwambiri ngati anali kupereka lingaliro la kudya nyama ya munthu. Koma, ndithudi, Yesu sakunena za kudya kwenikweni nyama ya munthu kapena kumwa mwazi. Iye akungogogomezera kokha kuti onse amene alandira moyo wosatha ayenera kusonyeza chikhulupiliro munsembe imene iye ati apange pamene apereka thupi lake laumunthu langwiro ndi kutsanulira mwazi wake wa moyo. Komabe, ngakhale ambiri a ophunzira ake sakupanga kuyesayesa kwa kuzindikira chiphunzitso chake ndipo chotero akutsutsa kuti: “Mawu aŵa ndiosautsa; akhoza kumva awa ndani?”
Pozindikira kuti ambiri a ophunzira ake akung’ung’udza, Yesu akuti: “Ichi mukhumudwa nacho? Nanga bwanji ngati mukawona Mwana wa munthu alikukwera kumene anali kale lomwe? . . . Mawu amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo. Koma pali ena mwa inu amene sakhulupilira.”
Yesu akupitirizabe kuti: “Chifukwa cha ichi ndinati kwa inu, Kuti palibe munthu angathe kudza kwa ine, koma ngati kupatsidwa kwa iye ndi Atate.” Atatero, ambiri a ophunzira ake akuchoka naleka kumtsatira. Chotero Yesu akutembenukira kwa atumwi ake 12 ndi kufunsa kuti: “Nanga inu mufuna kuchoka?”
Petro akuyankha kuti: “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha. Ndipo ife takhulupilira, ndipo tidziŵa kuti inu ndinu Woyera wa Mulungu.” Ndimawu abwino chotani nanga a kukhulupirika, ngakhale kuti Petro ndi atumwi ena angakhale asanazindikire mokwanira chiphunzitso cha Yesu pankhani imeneyi!
Ngakhale kuti wakondwera ndi yankho la Petro Yesu akunena kuti: “Kodi sindinakusankhani khumi ndi aŵiri, ndipo mwa inu m’modzi ali Mdyerekezi.” Iye akulankhula za Yudase Isikariote. Mwinamwake pamfundo ino Yesu wawona mwa Yudase ‘chiyambi,’ kapena kuyambika, kwa njira yolakwa.
Yesu wangogwiritsa kumene anthu mwala mwa kukana zoyesayesa zawo za kumpanga mfumu, ndipo iwo angakhale akulingalira kuti, ‘Kodi ameneyu angakhale Mesiya bwanji ngati iye savomereza malo oyenerera a Mesiya?’ Iyi, ingakhalenso nkhani imene idakali yatsopano m’maganizo mwa anthu. Yohane 6:51-71; 3:16.
▪ Kodi Yesu akupereka thupi lake kaamba ka ayani, ndipo kodi ameneŵa ‘akudya thupi lake’ motani?
▪ Kodi ndimawu ena otani a Yesu amene akunyansa anthu, komabe kodi iye akugogomezera chiyani?
▪ Pamene ambiri aleka kutsatira Yesu, kodi yankho la Petro nlotani?