Nyimbo 32
“Kumka Kunyumba ndi Nyumba”
1. Kumka kunyumba ndi nyumba,
Tilalika Mawu.
Mumidzi ndi mumindanso,
“Nkhosa” zidyetsedwa.
Mbiri Yaufumuyitu,
Yesu ananena,
Ikulalikidwa m’dziko
Ndi am’sinkhu yonse.
2. Tilalike chilanditso,
Kunyumba ndi nyumba.
Chodza kwa oitanira
Dzina la Yehova.
Adzaitana motani
dzina Salidziŵa?
Chotero Dzina Loyera
Limke kunyumbazo.
3. Sikhomo lonse tipeza
Khutu lomvetsera;
Nthaŵi zina tinyozedwa
Ndi okana kumva.
Zinateronso kwa Yesu;
Onse sanamvera.
“Nkhosa” zimva mawu ake;
Ife sitileka.
4. Timke kukhomo ndi khomo
Kulalika mbiri.
Anthu asankhe kukhala
“Nkhosa” pena “mbuzi.”
Tidzatchula dzina Lake,
Ndi cho’nadi Chake.
Popita pamakomowo,
Tidzapeza “nkhosa.”