Nyimbo 29
Tiyeni, Mboninu!
1. Olimba munthaŵi yamapetoyi,
Ali atumiki oimira mbiri.
Ngakhale Satana atsutsa,
Mwamphamvu ya M’lungu sawopa.
(Korasi)
2. Anthu akana chowonadi ichi.
Otsutsa aletsa dzina la Yehova.
Abwezedwe kumalo awo
Ndi Akristu olimba mtima.
(Korasi)
3. As’kali a Ya safuna zofeŵa.
Sakondweretsa dziko pena mafumu;
Amakhala opanda banga,
Ndiosunga umphumphu wawo.
(KORASi)
Tiyenitu Mboninu, molimba mtima!
Sangalalani muntchito ya Mulungu!
Nenani za Dziko latsopanolo,
Mmene mudzakhala madalitso!