Nyimbo 30
“Achangu Pantchito Zokoma”
1. Tikhale achangu pazabwino
Polalikira za Ufumu.
Tidziŵa Yehovayo ngwa Nsanje.
Tidzakhalabe m’nyumba yake.
2. Chikondi chikhaletu chowona,
Pomatumikira abale.
Poyandikana ndi Armagedo,
Tisachoke muutumiki.
3. Changu, chikhulupiro, chikondi.
Izi ziri ndi mbali zake.
Kufunitsa kumakhutiritsa,
Ngati moto mumtima mwathu.
4. Tikhale olimba m’masautso,
Chikondi chathu chisazime.
Changu cha kuyeretsa dzina la
Mulungu chitisonkhezera.