Nyimbo 107
Imbani Chitamando cha Yehova Molimbika!
1. Titame Yehova molimbika,
M’nyonga yake timenya nkhondo.
Mdani asatiwopseze konse.
Musawawope, tiyenitu.
(Korasi)
2. Titame Yehova molimbika
Tichenjeze onse mokweza;
Kuti Mfumu idzatha oipa,
Inde nthaŵi yayandikira.
(Korasi)
3. Titame Yehova molimbika,
Pophunzitsa owona mtima,
Kuwasonyeza mwaŵi wantchito,
Ofuna kuchita za M’lungu.
(KORASi)
Lengeza chipulumutso chake.
Thandiza anthu kudzipereka.
Titame Yehova molimbika,
Kwezani dzina loyeralo.