Nyimbo 146
Thaŵirani ku Ufumu wa Mulungu!
1. Funani Yehova inu ofatsa;
Chilungamo ndi kufatsa lero.
Potero pena mutsiku lamkwiyo
Kuti mudzabisikadi.
(Korasi)
2. Inu anjalatu ya chowonadi;
Bwanji mufu’la mowawa mtima?
Funani njira kuthaŵa opsinja,
Gonjani kwa Kristu Mfumu.
(Korasi)
3. Kwezani mitu, E, mosangalala.
Zitsimikizo za Ufumuwo!
Chingamira kuŵala kwa Yehova,
Muwopeni iye yekha!
(KORASi)
Thaŵirani ku Ufumu wake;
Imani molimbika. (molimba.)
Kumeneko mudzabisikakodi;
Kangazani kumumva. (kumumva.)