Nyimbo 142
Chiyembekezo cha Chilengedwe cha Chimasuko
1. Chilengedwe chonse chivutika;
Chituta zofesa zake.
Chakana M’lungu; Chikugonjera
Kuzinthu zovulazadi.
2. Poyembekeza chipulumutso,
Anthu ayang’ane kwa Ya.
Ngwokoma mtima, athandizadi
Kwa onse obuulawo.
3. Kuchimasuko ndi kubwezera
Anthuwo adzapezadi.
Mwana wa M’lungu, wasankhidwadi
Kuti anthu ayanjidwe.
4. Kugwirizana ndi “mtundu” wa Ya
Kumadzetsa madalitso.
Adikilira, nayembekeza,
Kukondwera ndi Ufumu