Nyimbo 125
‘Yehova Ali Kumbali Yanga’
1. Mtima wanga pa Yehova
Udalira kwambiri.
Ndikhumba kuyenda naye
Ndi kumumamatira.
Munjirayo mungakhale
Mikhalidwe yovuta,
Koma M’lungu ali nane.
Mtima wanga ukondwa!
(Korasi)
2. Ndidziŵa munthaŵi ino Kuti ndidzayesedwa.
Mdani ndi ziwanda zake
Afunatu kundipha.
Koma ndingawapambane,
Mwachithandizo cha Ya.
Okhala ndi dzina lake
Mulungu awakonda.
(Korasi)
3. Yehova wakulitsadi
Mtundu wake woyera.
Ambiri adza nasunga
Malamulo akewo.
Achirikiza onsewo;
Mwa iwo akondwera.
Nanenso ndichite changu
Kumlingo waukulu.
(KORASI)
Ya ali kumbali yanga;
Ndidzamutamanda kosatha.