Nyimbo 15
Moyo Wopanda Mapeto—Potsiriza!
1. Kodidi mungawone,
Anthu ali pamodzi?
Chisonicho Chathadi!
Mtendere wadzadi.
(Korasi)
2. Anthu ndi nyama ali
Pamodzi mumtendere.
Chakudyanso Chiripo
Chopatsidwa ndi Ya.
(Korasi)
3. M’nthaŵiyo nkhalambadi,
Khungu lidzasalala.
Mavutowo, Athadi
Sitimawopanso.
(Korasi)
4. Onsewo adzakondwa
Poimbira Mulungu.
Nthaŵi zonse tidzati
“Zikomo” kwa M’lungu!
(KORASi)
Imbani mokondwa.
Mungagaŵanemo.
Panthaŵiyo mudzati:
“Moyo wamuyaya!”