Nyimbo 103
Umsenze Yehova Nkhaŵa Zako
1. Imvani pemphero langa;
M’lungu musadzibise.
Mundiyankhe, M’lungu wanga,
Ndisade nkhaŵa konse.
(Korasi)
2. Nkadakhala ndi mapiko,
Ndikadaulukira
Kumalo achisungiko,
Kuchoka kwa oipa.
(Korasi)
3. Ndidzaitana Yehova,
Pampando wachifumu.
Amapereka mtendere,
Ndi kuombola moyo.
(KORASi)
Umsenzetu nkhaŵa zako;
Iye adzakusunga.
Adzakuthandiza iwe
Kukhala wolimba nji.