Nyimbo 96
Kulemekeza Atate Wathu Yehova
1. Ya chilengedwe chiimba
Za mphamvu ndi ulemu.
Ndi chifuno zolengedwa
Zanu zinakhalapo.
Mupereka madalitso,
Ndi mphatso zabwinonso.
Mwachititsa ulosiwo
Kukwaniritsidwadi.
Pobadwa Yesu angelo
Anamulemekeza.
Kupyola mwa Mbuye Kristu,
Mwaperekatu dipo!
2. Tidziŵatu Mwana wanu
Anakwanitsa ntchito,
Analilaka dzikoli
Nasintha makhalidwe,
Monga Mfumu pachimpando
Apatsa malamulo,
Adziŵitsatu dzinalo
Kumitundu yadziko,
Eya tipeza chimwemwe
Pakuimbira inu:
‘Mbuye Ya wa kuunika,
Adzachotsa chisoni.’
3. Kodi tingamuimbire,
Ndi kumusangalatsa?
Tichite kudzipereka,
Ndi kumutumikira?
Tigwiritsitse dzinalo,
Ntchito itsirizidwe.
Chikondi chisazirale,
Changu chathu chisathe.
Koma ndi mitima yathu
Tikutumikirani.
Kulemekeza dzinalo
Tidzayesa kutero.