Mmene Akristu Amaonera Makonzedwe Osamalira Maliro ndi a Ukwati
1 Makonzedwe a Maliro: Imfa yakhala chinthu chofala kwambiri kwa anthu m’mbiri yonse. Chisoni chimene imadzetsa kwa ofedwa chimathetsa nzeru nthaŵi zonse. Chifukwa cha chisoni chimene imfa imachititsa ofedwa ndi ziphunzitso zosokoneza zimene chipembedzo chonyenga chimaphunzitsa za anthu akufa, ngakhalenso miyambo ya pamaliro kwina ndi kwina, nkwanzeru kuti Mkristu adziŵe zimene Malemba amanena pa miyambo yoteroyo kuti apeŵe kuchita zinthu zimene zingamuwonongere unansi wake ndi Yehova.—Deut. 18:9-13; 2 Akor. 6:14-18.
2 Kalata ya KU MIPINGO YONSE yomwe inali ndi deti la SA February 1, 1996, inanena za nkhani yakugona pabwalo la nyumba momwe muli mtembo. Tsopano tikuti tikufotokozereni mfundo zimene zinali mu Bokosi la Mafunso la Utumiki Wathu Waufumu wa March 1997, lomwe linali ndi mfundo yakuti: “Pamene mpingo wapemphedwa kuthandiza kusamalira maliro, pangabuke mafunso otsatirawa:
3 “Kodi ndani ayenera kupereka nkhani yamaliro? Apabanja ndiwo adzapanga chosankha chimenechi. Angasankhe mbale wobatizidwa aliyense wakaimidwe kabwino. Ngati bungwe la akulu lapemphedwa kupeza wokamba nkhani, iwo nthaŵi zambiri adzasankha mkulu wokhoza bwino kuti apereke nkhani yozikidwa pa autilaini ya Sosaite. Ngakhale sitikutamanda wakufayo mopambanitsa, kungakhale bwino kutchula mikhalidwe yopereka chitsanzo chabwino imene iye anali nayo.
4 “Kodi Nyumba ya Ufumu ingagwiritsiridwe ntchito? Inde ingatero ngati bungwe la akulu lapereka chilolezo ndipo ngati sizisokoneza nthaŵi yamsonkhano wanthaŵi zonse. Holo ingagwiritsiridwe ntchito ngati wakufayo anali ndi mbiri yabwino ndipo anali chiŵalo cha mpingo kapena mwana wamng’ono wa chiŵalo china. Ngati munthuyo anali atadzetsa chitonzo chodziŵika kwa anthu mwa khalidwe lina losakhala lachikristu, kapena ngati pali nkhani zina zimene sizingapereke chithunzi chabwino cha mpingo, akulu angasankhe kusalola kugwiritsira ntchito holo.—Onani buku la Uminisitala Wathu, masamba 62-3.
5 “Kwenikweni, Nyumba za Ufumu sizimagwiritsiridwa ntchito pamaliro a osakhulupirira. Zimenezo zingachitike kokha ngati achibale ake amoyo akugwirizana mwachangu ndi mpingo monga ofalitsa obatizidwa, ambiri mumpingo amamdziŵa wakufayo kuti anali wokonda choonadi wokhala ndi mbiri yabwino ya khalidwe lake m’chitaganya, ndipo palibe miyambo yakudziko imene idzaloŵetsedwa m’programuyo.
6 “Popereka chilolezo cha kugwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu, akulu adzalingalira ngati kuli kozoloŵereka kuti anthu amayembekezera kuona bokosi lamaliro pamaliropo. Ngati amatero, angaloleze kulibweretsa m’holo.
7 “Bwanji nanga za maliro a anthu akunja? Ngati wakufayo anali ndi mbiri yabwino m’chitaganya, mbale angapereke nkhani ya Baibulo yotonthoza kunyumba yamaliro kapena kumanda. Mpingo sudzavomera kusamalira maliro a munthu amene anali wodziŵika ndi khalidwe lachisembwere ndi losayeruzika kapena amene moyo wake unali wosemphana kotheratu ndi mapulinsipulo a Baibulo. Ndithudi mbale sangagaŵane ndi mtsogoleri wachipembedzo kuchititsa programu ya chikhulupiriro choloŵana kapena kugaŵanamo m’maliro alionse ochitidwira m’tchalitchi cha Babulo Wamkulu.
8 “Bwanji ngati wakufayo anali wochotsedwa? Nthaŵi zambiri mpingo sumaloŵamo. Nyumba ya Ufumu singagwiritsiridwe ntchito. Ngati munthuyo anali kusonyeza umboni wa kulapa ndi kusonyeza chikhumbo cha kubwezeretsedwa, chikumbumtima cha mbale chingamlole kupereka nkhani ya Baibulo kunyumba yamaliro kapena kumanda, kuti apereke umboni kwa osakhulupirira ndi kutonthoza achibale. Komabe, asanapange chosankha chimenechi kungakhale bwino kwa mbaleyo kufunsira kwa bungwe la akulu ndi kulingalira zimene iwo anganene. Pamikhalidwe imene sikungakhale kwanzeru kuti mbaleyo aloŵemo, kungakhale koyenera kuti mbale amene ali wambanja la munthu wakufayo apereke nkhani yotonthoza achibale.”
9 Sitikukayikira kuti pamene munaŵerenga kwa nthaŵi yoyamba Bokosi la Mafunso limeneli zinakukhudzani mtima kuona kuti gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” limatisamala mwa kutipatsa malangizo ameneŵa oti tizitsatira pamene tsoka latigwera monga imfa. Tsopano tikulimbikitsa onse kuliŵerenganso Bokosi la Mafunsolo mosamalitsa kuti alidziŵe bwino. Makamaka akulu afunikira kulidziŵa kwambiri ndi kugwiritsira ntchito malangizo ake paliponse pamene afunikira kutero chifukwa iwo ndiwo ali ndi udindo waukulu wakutonthoza banja lofedwa. Za mfundo yoti ndani adzakamba nkhani yamaliro, zimenezo nzoti apabanjalo asankhe ndiwo. Koma akulu angathandize ngati palibe wina m’banjamo yemwe angasankhe zimenezo.
10 Pakutonthoza banja lofedwa, Nsanja ya Olonda ya October 15, 1990, tsamba 31, pa Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga, inati: “Oyang’anira achikristu, ngakhale kuti angakhale otanganitsidwa koposa, ayenera kutsogolera m’kupereka chitonthozo ku gulu. Iwo amakumbukira kuti chitsanzo chawo Yesu, Mbusa Wabwino, anatumidwa ‘kudzamanga osweka mtima ndi kutonthoza mtima wa onse amene akulira maliro.’ (Yesaya 61:1, 2; Yohane 10:14) Yesu sanapereke chitonthozo choterocho kokha pamene kunali koyenera. Iye anali wofunitsitsa kuchita chilichonse chimene akanatha kukhala ndi anamalira achibale a Lazaro—kulira nawo limodzi. (Yohane 11:11, 17, 33) Ngakhale Akristu amene sangakhale okhoza kunena zambiri kwa ofedwa pamaliro angachite bwino mwa kungopezekapo. Ziŵalo za banja lolira zingapeze chitonthozo mwa kungoona kuti ambiri apezekapo—achichepere ndi achikulire—ochokera mu mpingo wachikristu. Kumbukirani mmene Ayuda ena ananenera pamene Yesu anapita kwa alongo ochita chisoni a Lazaro: “Taonani, anamkondadi!” (Yohane 11:36) Achibale osakhulupirira, anansi, kapena mabwenzi amalonda opezeka pamaliro achikristu amachita chidwi ndi chiŵerengero chachikulu cha Mboni zopezekapo ndipo motero akhala ovomereza kwambiri choonadi cha Baibulo choperekedwa.”
11 Kusamalira Manda: Kumadera ena kuli miyambo yokhudza kusamalira manda. Ngakhale azipembedzo zotchedwa “zachikristu” amaika madeti oti onse apite kumanda, nkulambula malowo ndi kulemekeza akufa. Nanga Akristu amachita bwanji? Makolo akale achiyuda ankakonda kusamalira manda. (Gen. 35:20) Manda onyalanyazidwa angadzetse chitonzo pa ife monga olambira Yehova. Ndiponso ndi nkhani yaumwini kuti aliyense asankhe kukaona manda ndi kukumbukiranso munthu yemwe anaikidwamoyo. Koma kodi Mkristu amafunikira kuchita kuika madeti ochitira zonsezo, makamaka madeti amene matchalitchi a Babulo Wamkulu amaika? Zinthu zimenezo angazichite tsiku lina lililonse. Monga momwedi sitimafunikira “Krisimasi” kuti tipatsane mphatso, sitifunikira madeti okaonera manda. Sitimafuna kufanana ngakhale pang’ono ndi anthu a Babulo Wamkulu kapena ena amene amalankhula ndi akufa, kuwatengera chakudya kapena kuchita mapwando ansembe zolemekeza akufa. Ochita zimenezo ndiwo aja amene Yesu anawatcha “akufa” mwauzimu, chifukwa amasamala kwambiri zinthu zokhudzana ndi kuika maliro, manda ndi makolo akufa. Choncho kwa ife mawu otsatiraŵa adakagwira ntchito, akuti: “Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu.”—Luka 9:60.
MAUKWATI
12 “Mapwando Aukwati Wachikristu Amene Amasangalatsa” unali mutu wa nkhani yabwino yophunzira mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1984. Nkhani yotsatira inali ndi mutu wakuti “Pezani Chisangalalo Chachikatikati pa Mapwando Achikristu.” Ambiri akhala Mboni za Yehova chiyambire pamene nkhanizo zinatuluka, choncho nkopindulitsa kupendanso mfundo zina zimene zidzatithandiza kuchita maukwati olemekeza Yehova, Woyambitsa ukwati.
13 Ngati mwakonza kudzakhala ndi nkhani yaukwati pambuyo potchata kuboma, kudzakhala kwanzeru kusalola masiku ambiri kupitapo. Ngati mwamunayo ndi mkaziyo akafuna kuti nkhani ya ukwati wawo ikakambidwe m’Nyumba ya Ufumu, ayenera kuonana ndi akulu a mpingo pasadakhale nkupempha holoyo kuti aigwiritsire ntchito. Akuluwo adzafuna kutsimikiza kuti makonzedwe a ukwatiwo adzawasiya ndi zikumbumtima zabwino. Ayenera kusankha nthaŵi yoti siidzaombana ndi zochita zilizonse za mpingo. Mbale yemwe wasankhidwa kudzakamba nkhani yaukwati adzaonana pasadakhale ndi mkwati ndi mkwatibwi kuti awapatse uphungu wothandiza ndi kuona kuti palibe zilizonse zokhudza chikhalidwe ndi lamulo zimene zingalepheretse ukwatiwo ndi kuti akugwirizana ndi makonzedwe onse a phwando lomwe lidzakhalapo.
14 Ukwati wachikristu uli mpata wabwino wosonyeza kuti ‘sitili a dziko lapansi.’ (Yoh. 17:14; Yak. 1:27) Kulongosoka kwathu kuyenera kuonekeratu. Zimenezo zikutanthauza kuti tidzafika panthaŵi yake, m’malo mopangitsa anthu kudikira, mwina nkudodometsa zochita zampingo. Makamaka mkwatibwi afunikira kusamala zimenezi, chifukwa achibale ake akunja angamlimbikitse kuchedwa—kuti zionekere kwambiri kuti wofunika ndi iyeyo. Mwa kufika msanga, mlongo wachikristu wokhwima maganizo angasonyeze kuti mikhalidwe yauzimu yonga kudzichepetsa ndi kulingalira ena, njofunika kwa iye! Ndiponso ngati mwaitanirapo wojambula zithunzi kuti adzajambule zochitikazo, ayenera kuchita zinthu molongosoka. Tingachite bwino kumuuza kuti tikufuna kuti abwere atavala jekete, tayi, ndi talauza laulemu, ndi kuti asadodometse nkhani pojambula zithunzi. Asajambule zithunzi zilizonse pamene anthu akupemphera. Kuchita kwathu zinthu mwadongosolo kudzalemekeza Yehova ndipo kudzapereka umboni wabwino. Palibe chifukwa chotsatirira miyambo ya anthu imene ingasokoneze tanthauzo lenileni la chochitikacho.
15 Sipachitofunikira madyerero kuti ukwati uyende bwino, komanso Malemba samaletsa nthaŵi yosangalala imeneyo. Komabe, kwa Akristu oona macheza oterowo ayenera kusiyana ndi madyerero achikunja, omwe amakhala opambanitsa, omwetsa moŵa, madyaidya, nyimbo zosokosera, ndi kuvina konyanyuka, ndipo ngakhale ndewu. Baibulo limati “mchezo” ndi ntchito zathupi. (Agal. 5:21) Nkwapafupi kulamulira zochitika pamenepo ngati silili gulu lalikulu kwambiri. Sitifunikira kumangapo hema kutsata miyambo yofala. Ngati ena angasankhe kumangapo hema chifukwa chofuna kuwonjezera malo kapena chifukwa cha dzuŵa kapena mvula, zimenezo nzofuna mwini.
16 Maukwati ena amakhala onkitsa olira ndalama zambiri, ndipo pamakhala operekeza mkwati ndi mkwatibwi ambirimbiri. Amakonzedwa pafupifupi ngati msonkhano wachigawo, ndi oyang’anira madipatimenti ambiri ndi owathandizira. Kodi maukwati amenewo amalemekezadi Yehova ndi lumbiro la ukwati la kukhala m’banja kwa moyo wonse, kapena amangokhala “matamandidwe a moyo”?—1 Yoh. 2:16.
17 Zochitika zasonyeza kuti njira yabwino yochepetsera chiŵerengero cha opezekapo ndiyo mwa kuwalembera makhadi. Kuli bwino kuitana munthu mmodzimmodzi m’malo moitana mipingo yonse, ndipo poti ndife Akristu adongosolo, tiyenera kulemekeza makonzedwewo oitana anthu ochepa. Kuitana anthu mowalembera makhadi kungatithandizenso kupeŵa kukhala ndi munthu wochotsedwa paphwandolo, zimenezo zingasokoneze zinthu, pakuti ngati iye angabwerepo, abale ndi alongo ambiri angachokepo. (1 Akor. 5:9-11) Ngati mwamunayo ndi mkaziyo aitanirapo achibale ndi odziŵana nawo osakhulupirira, mosakayikira amenewo adzakhala oŵerengeka, nkusamala kwambiri “a pabanja lachikhulupiriro.” (Agal. 6:10) Ena amasankha kuti odziŵana nawo ndi achibale osakhulupirira awaitanire kunkhani yaukwati osati kuphwando. Chifukwa? Chabwino, pazochitika zina achibale akunja anachita zamanyazi kwambiri paphwando laukwati moti abale ndi alongo ambiri anaona kuti si bwino kukhalaponso. Nthaŵi zina, achibale akunja, mwina chifukwa chakuti anathandizira kugula zofunika pa ukwatiwo, amafuna kuti iwo ayendetse zinthu paphwandolo, namayesa kulamulira anthu okambapo mawu, ndi zina zotero. Ena amene akukwatirana amakonza chakudya chochepa cha iwo okha ndi mabanja awo ndi mabwenzi achikristu.
18 Malinga ndi Yohane 2:8, 9, nkwabwino kusankha “mkulu wa phwando.” Tiyenera kukumbukira kuti mkwatiyo ndiye ali ndi udindo pazonse zochitikapo, ndipo iye ayenera kusankha Mkristu yemwe amamdalira kuti aziona kuti zinthu zikuchitika mwadongosolo labwino ndi kuti pali khalidwe labwino kwambiri. Kumene mabwenzi angapereke mphatso, zimenezo zichitike popanda “matamandidwe a moyo.” (1 Yoh. 2:16) Nyimbo zingakhale zosangalatsa ngati zilibe mawu okayikitsa, si zaphokoso kwambiri, kapenanso zamaimbidwe osadekha. Ambiri amaona kuti ndi bwino kuti mkulu amvetsere pasadakhale nyimbo zimene ziti zikaimbidwepo. Kuvina kungakhale kosangalatsa koma kuli ndi ngozi zake, chifukwa mavinidwe ambiri amwambo anatengedwa kumavinidwe akubala, ndipo amanyanyula. “Mphindi ya moŵa ndi makeke” nthaŵi zina imakhala chizindikiro kwa anthu akunja kuti tsopano akhoza kumasuka. Akristu ambiri amene akukwatirana amasankha kusakhala ndi moŵa pamapwando awo aukwati, kuti apeŵe mavuto. Popeza kuti timafuna kulemekeza Yehova, tidzapeŵa kudzionetsera kuti anthu atitame.
19 Koma bwanji za kukhala nawo paukwati wa anansi, ogwira nawo ntchito yakudziko, kapena achibale chapatali ndi odziŵana nawo? Mkristu aliyense ayenera kudzisankhira zochita pankhaniyo. Ndi bwino kumakumbukira kuti nthaŵi yathu njamtengo wapatali, poti timafuna nthaŵi ya utumiki wathu, ya phunziro laumwini, ya zinthu zina zokhudza banja ndi mpingo. (Aef. 5:15, 16) Pamawikendi sitimafuna kuphonya misonkhano ndi utumiki wakumunda. (Aheb. 10:24, 25) Nthaŵi za maukwati ena zingaombane ndi misonkhano yadera ndi utumiki wina wapadera. Tisamalole kusokonezedwa pantchito zathu zachikristu chifukwa chowononga nthaŵi yambiri tili ndi anthu akudziko tikumachita zinthu zosalemekeza Mulungu. (1 Pet. 4:3, 4) Pankhani imodzimodziyi, Nsanja ya Olonda ya December 15, 1974, (yachingelezi) inafunsa kuti “Kodi Mboni za Yehova zimaganiza bwanji za kupezeka paukwati wa mnzawo kapena wachibale wakudziko?”
20 Ngati ali ana okha amene akuganiza zokapezekapo, makolo awo ndiwo adzasankha zochita. Koma ili nkhani yosankha mwini ngati Mkristu aliyense akufuna kusenza udindo wake. Komabe, pali mapulinsipulo a m’Malemba ndi mikhalidwe yambiri yosiyanasiyana yoti ailingalire.
21 Ukwatiwo ungachitikire m’nyumba yachipembedzo, ndipo akumawakwatitsa mtsogoleri wachipembedzo. Zimenezo zingausiyanitse ndi ukwati umene boma linakwatitsa. Chikumbumtima cha Mkristu woona sichingamlole kupemphera nawo kapena kuchita nawo zinthu zachipembedzo zimene akudziŵa kuti nzosemphana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Ndipo sikuti angafune kuona mmene angafikire pafupi ndi mpatuko popanda kudumpha malire. Ayenera kumvera lamulo la m’Malemba lakuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigaŵana bwanji ndi chosalungama? . . . Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira? . . . Chifukwa chake, Tulukani pakati pawo, ati Ambuye, ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka.”—2 Akor. 6:14-17.
22 Mpomveka kuti yemwe waitanidwa kukakhala nawo paukwati wa achibale ndi anzake akudziko angakumane ndi vuto. Mwachitsanzo, omwe aitanidwawo angakhale mkazi wachikristu limodzi ndi mwamuna wake wosakhulupirira. Mwamunayo mwina adzaganiza kuti zingakhale bwino kuti onsewo akapezeke paukwatiwo. Koma mkaziyo zingamvute. Iye angalingalire kuti atakapezeka paukwati wam’tchalitchi, mikhalidwe kumeneko ingampangitse kuchita kanthu kena kolakwika. Kwinakunso, mkaziyo angaganize kuti poti mwamuna wake akufuna kuti apite onse, adzangopita nkukhala wopenyerera waulemu, koma nkutsimikiza kuti sakachita nawo chilichonse chachipembedzo.
23 Mosasamala kanthu za mmene mkaziyo adzaionera nkhaniyo, zingamkomere ngati angamfotokozere mwamuna wake mosamkhumudwitsa mmene akumvera. Ngati zimene wafotokoza mkaziyo zapangitsa mwamunayo kuganiza kuti ngati mkazi wake ati akakhalepo angakamnyazitse, angasankhe kupita yekha. Kapena mwamunayo angafunebe kutsagana ndi mkazi wake, koma kuti azikangopenyerera ali phee, pamenepo mpamene mkaziyo angasankhe kupita kapena kusapita.
24 Chinthu china choyenera kuchilingalira ndicho mmene zidzawakhudzira okhulupirira anzathu akationa tili paukwati m’nyumba yachipembedzo. Kodi zingavulaze chikumbumtima cha ena? Kodi zimene mwachitazo zingawafooketse pakuyesayesa kwawo kukana kulambira mafano? Pulinsipulo la Baibulo limene limabwera m’maganizo nlakuti: ‘Tsimikizirani zinthu zofunika kwambiri, kuti mukhale opanda cholakwa ndi osakhumudwitsa ena kufikira tsiku la Kristu.’—Afil. 1:10, NW; onaninso 1 Akorinto 8:9-13.
25 Nthaŵi zina mukaitanidwa ku ukwati kumakhala kuli koti mukakhala m’gulu la operekeza. Bwanji ngati mukafunikira kutengamo mbali m’zinthu zina zachipembedzo? Mwachionekere munthu wofuna kukondweretsa Mulungu sangachite nawo zinthu zachipembedzo chonyenga; munthuyo ayenera kumvera Mawu ake. Koma Mkristu angafotokoze mmene akumvera ndi kulongosola kuti sakufuna kuipitsa m’njira iliyonse chikondwerero cha tsiku laukwatilo mwa kuchita chinthu china chimene chingachititse manyazi.
26 Pankhani zonga zimenezi, Akristu ayenera kumapenda zinthu zonse mosamala. M’mikhalidwe ina angaganize kuti sipakhala vuto lililonse ngati atapezekapo monga openyerera aphee. Kwinakunso, mikhalidwe mwina ingafune kuti Mkristu alingalire kuti kuvulaza chikumbumtima chake kapena cha ena mwa kupezeka paukwati wakudziko kungakhale kwakukulu kuposa zimene adzapindula nazo mwa kupezekapo. Mulimonse mmene mkhalidwewo ungakhalire, Mkristu ayenera kuona kuti zimene wasankha kuchitazo sizidzaipitsa chikumbumtima chake chabwino pamaso pa Mulungu ndi pa anthu.