Nyimbo 220
Paradaiso Wathu: Tsopano ndi Mtsogolo
1. Titamanda Yehova M’lungu
Ka’mba ka paradaiso,
Pophunzira ndi posonkhana
Timakhala anzeru.
Tiyamikiretu
Madalitsowo
Tisangalalatu
Ndi ntchito yanu!
Chikondi chanu ndi cha mnansi
Nchomangira cholimba.
Chitigwirizanitsa m’ntchito,
Kuti ife tisagwe!
2. Kulamulira kolungama
Mwapatsa Kristu Mfumu.
Padzanja lanu lamanjalo
Alamula ponsepo.
Titama Yehova,
Potidziŵitsa
Chifuniro chanu
Chosonkhanitsa.
Khalidwe lathu likhalebe
Loyenera mbiriyo,
Kuti tisakhumudwitsetu
Anthu onga nkhosawo!
3. Nkhondo yaikulu itatha
Yomenyedwa ndi M’lungu,
Satana ndi ziwanda zake
Ataponyedwa m’phompho,
Atumiki anu Adzaukadi,
Kudzatumikira
Mu Paradaiso.
Anthu adzakhala angwiro
Kupyolera munsembe;
Ndiyeno padziko kosatha,
Padzakhala chimwemwe.