Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mbadwo Wanga—Wapadera ndi wa Mwaŵi Wapamwamba!
    Nsanja ya Olonda—1987
    • nacho chako chachikulu koposa m’chowonadi?” Popanda kusinkhasinkha ndimayankha: “Kuwona kukwaniritsidwa mkati mwa mbadwo wanga kwa maulosi a Baibulo okonzekeretsedwa ndi amuna owuziridwa ndi odzipereka zaka mazana ambiri zapita.”

      Ziwalo za mbadwo wanga kunja kwa gulu la teokratiki, ndithudi, zakhala kwenikwenidi monga mmene Chitsanzo cha Zithunzithunzi cha Chilengedwe cha 1914 chinanenera kuti iwo adzakhala: openga ndi ndalama, openga ndi zosangalatsa, ndi openga ndi ulemerero. Awo a ife amene ali mkati mwa gulu la Ambuye tayesera, mu njira iriyonse yothekera, kutembenuzira chidwi chawo ku uthenga wamoyo. Tagwiritsira ntchito mawu, kusatsa kosindikizidwa pa masamba athunthu, wailesi, magalimoto okuza mawu, makina okhoza kunyamulidwa osewerera mawu ojambulidwa, misonkhano yaikulu ndi khamu lomakulakula la aminisitala a kunyumba ndi nyumba. Ntchito imeneyi yatumikira kugawanitsa anthu​—awo a mu chiyanjo cha Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu kumbali imodzi kuchokera kwa awo amene amatsutsana naye ku mbali ina. Iyi ndi ntchito imene inanenedweratu ndi Yesu kaamba ka mbadwo wanga!​—Mateyu 25:31-46.

      Kufikira pamene “mtima wotopa” wanga umenewu udzagunda pamapeto ake, udzapitiriza kugunda mu chiyamikiro kaamba ka mwawi womwe ndasangalala nawo wa kukhala mbali ya mbadwo wapadera. Udzapitirizabe kugunda mu chikondwerero kaamba ka mwawi umene ndiri nawo tsopano wa kuwona mamiliyoni a nkhope zomwetulira zomwe zakhazikitsidwa kupitirizabe kumwetulira kosatha.

  • Wachichepere Alemekeza Yehova
    Nsanja ya Olonda—1987
    • Wachichepere Alemekeza Yehova

      MWAWl wokulira wakuchitira umboni uli wotseguka kwa achichepere pamene iwo ali ndi chikhumbo champhamvu cha kutumikira Yehova. Ichi chinawoneka mu chokumana nacho cha mnyamata wa zaka zisanu wa ku madzulo mu Kenya.​—Mlaliki 12:1.

      Mayi wake anamufunsa iye: ‘‘Kodi nchiyani chimene ufuna kudzakhala pamene wakula?”Mnyamatayo anali atawonapo mpainiya wapadera mu mpingo ndipo anayankha: “Ndikufuna kudzakhala mpainiya wapadera monga Mbale F​——.” Mayi anayankha: “Koma ichi nchosatheka; sungakhale ngakhale mpainiya wokhazikika chifukwa ulibe phunziro la Baibulo.” Mnyamatayo anafunsa kuti: “Kodi nchiyani chimene ndingachite tsopano?“ Mayi wake analingalira kwa iye kuyesa kuphunzitsa osewera nawo anzake kuchokera mu kope lake la Bukhu Langa la Nkhaniza Baibulo.

      Mnyamata wa zaka zisanuyo anatenga Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndi kupita kuitanira pa mabwenzi ake, kuwaitana iwo kuphunzira Baibulo ndi iye. Chotulukapo chake?

      lye anapanga gulu la khumi lomwe akanaphunzira nalo. lye anapanga kugwiritsira ntchito kwabwino kwa zithunzi, anafunsa mafunso achitokoso ambiri, ndi kufunsa mafunso obwereramo pamapeto pa phunziro. Ngati iwo sanakumbukire, iye anabwereramo mu nkhaniyi ndi iwo kachiwirinso. Mayiyo analongosola kuti chinalidi chimwemwe chenicheni kuwona achichepere onsewo atakhala pansi kutsogolo kwa nyumba yake kuphunzira limodzi! Pamenepo panali mwana wake wamwamuna wa zaka zisanu akufunsa mafunso, ndipo kenaka manja onse anapita pamwamba kuti ayankhe.

      Chinali chimwemwe chowonjezereka kwa mayiwo, limodzinso ndi mpingo, kuwona asanu ndi atatu a ana amenewa akupezeka pa misonkhano ya mpingo. Ena awiriwo anali a ang’ono kwambiri. Zonsezo zinachitika chifukwa cha wa zaka zisanu yemwe anafuna kulemekeza Yehova ndi kuthandiza ena.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena