Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/98 tsamba 1
  • Tingachite Ntchito Zoposa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tingachite Ntchito Zoposa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • “Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzira Anga”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
  • “Pitani Mukaphunzitse Anthu a Mitundu Yonse”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Otanganitsidwa m’Ntchito Zakufa Kapena Muutumiki wa Yehova?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kugwira Ntchito ndi Yehova Mokhulupirika
    Nsanja ya Olonda​—1990
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 9/98 tsamba 1

Tingachite Ntchito Zoposa

1 Utumiki wa Yesu Kristu unadziŵika ndi ntchito zodabwitsa. Mozizwitsa anadyetsa zikwi za anthu, kuchiritsa odwala ochuluka, ndi kuukitsa ena kwa akufa. (Mat. 8:1-17; 14:14-21; Yoh. 11:38-44) Zochita zake zinachititsa chidwi anthu onse a mtunduwo. Komabe, usiku wotsatana ndi imfa yake anauza otsatira ake okhulupirika kuti: “Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi.” (Yoh. 14:12) Kodi tingachite ntchito “zoposa” motani?

2 mwa Kufola Gawo Lokulirapo: Yesu anagwira ntchito yake m’Palestina mokha, pamene kuli kwakuti ophunzira ake oyambirira anauzidwa kuchitira umboni ku “malekezero ake a dziko,” kutali kwambiri ndi kumene Yesu mwiniyo analalikirako. (Mac. 1:8) Ntchito yolalikira imene iye anayamba tsopano ikuchitidwa padziko lonse, m’maiko 232. (Mat. 24:14) Kodi mumagwira nawo ntchito mokwanira m’gawo la mpingo wanu?

3 mwa Kufikira Anthu Ochuluka: Yesu anasiya ophunzira ochepa kwambiri kuti apitirize ntchito yolalikira. Komabe, chifukwa cha kuchitira umboni kwawo mwachangu pa Pentekoste mu 33 C.E., anthu ngati zikwi zitatu analandira choonadi nabatizidwa tsiku lomwelo. (Mac. 2:1-11, 37-41) Kusonkhanitsa “ofuna moyo wosatha” kwapitiriza kufikira m’tsiku lathu, pamene tikubatiza anthu oposa 1,000 pa avareji tsiku lililonse. (Mac. 13:48, NW) Kodi mukuchita zonse zimene mungathe kuti mufikire anthu oona mtima kulikonse kumene angapezeke ndi kubwererako mofulumira kuti mukakulitse chidwi chawo?

4 mwa Kulalikira kwa Nthaŵi Yaitali: Yesu anachita utumiki wake padziko lapansi kwa zaka zitatu ndi theka zokha. Ambiri a ife takhala tikulalikira kwa zaka zoposa pamenepo. Mosasamala kanthu za nthaŵi imene tidzaloledwa kuchitabe ntchitoyi, timasangalala kuthandiza wophunzira watsopano aliyense kuti ayambe kuyenda panjira yopita kumoyo. (Mat. 7:14) Kodi mwezi uliwonse mumakhala ndi zambiri zochita mu ntchito ya Ambuye?—1 Akor. 15:58.

5 Tingakhalebe nchidaliro chakuti popeza Yesu akutichirikiza, ife monga ophunzira ake oona tidzachitabe ntchito zoposa.—Mat. 28:19, 20.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena