Nyimbo 144
Tiyenera Kukhala ndi Chikhulupiliro
1. Nthaŵi zakale M’lungu ananena
Kupyolera mwa aneneri ake.
Koma tsono wanena mwa Mwana’ke;
Mwa kumvetsera tidzapulumuka.
(Korasi)
2. Tisataye ufulu wa kunena,
Tikhale olimba polalikira.
Tikatsanza chitsanzo cha Ambuye,
Yehova adzatifupadi ife.
(Korasi)
3. Sitidzabwerera kuchitayiko,
Komatu tiri okhulupirika.
Nkana adaniwo akutizinga,
Tidzakhulupilirabe Yehova.
(KORASI)
Tikhulupiriretu mu Baibulo.
Kuti tipulumuke nkhondo ya M’lungu.
Tiri ndi chikhulupiro cha ntchito?
Nchimenecho tidzapulumuka.