Mutu 2
Kukonzekera Ukwati Wachipambano
1, 2. (a) Kodi Yesu anagogomezera motani kufunika kwa kukonzekera? (b) Kodi kukonzekera kuli kofunika makamaka m’mbali ziti?
KUMANGA nyumba kumafuna kukonzekera bwino. Maziko ake asanayalidwe, malo ayenera kupezedwa ndipo mapulani ayenera kulembedwa. Komabe, pali chinthu china chofunika kwambiri. Yesu anati: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?”—Luka 14:28.
2 Zimene zimagwira ntchito pomanga nyumba zimagwiranso ntchito pomanga ukwati wachipambano. Ambiri amanena kuti: “Ndikufuna kukwatira kapena kukwatiwa.” Koma kodi ndi angati amene amaima kaye ndi kulingalira za mtengo wake? Pamene Baibulo limathokoza ukwati, limachenjezanso za mavuto opezeka muukwati. (Miyambo 18:22; 1 Akorinto 7:28) Chifukwa chake, awo ofuna ukwati ayenera kulingalira moona mtima za madalitso limodzinso ndi mavuto a ukwati.
3. Kodi nchifukwa ninji Baibulo lili chithandizo chofunika kwa awo okonzekera ukwati, ndipo lidzatithandiza kuyankha mafunso atatu ati?
3 Baibulo likhoza kuthandiza. Uphungu wake uli wouziridwa ndi Woyambitsa ukwati, Yehova Mulungu. (Aefeso 3:14, 15; 2 Timoteo 3:16) Mwa kugwiritsira ntchito mapulinsipulo opezeka m’buku lophunzira limeneli, lamakedzana koma lapanthaŵi yake, tiyeni tione kuti (1) Kodi munthu angadziŵe motani kuti ali wokonzeka kuloŵa ukwati? (2) Kodi ayenera kufunanji mwa munthu amene afuna kukwatirana naye? ndi kuti (3) Kodi ndi motani mmene chibwenzi cha otomerana chingakhalire cholemekezeka?
KODI MULI WOKONZEKA KULOŴA UKWATI?
4. Kodi chofunika kwambiri nchiyani kuti ukwati ukhale wachipambano? Ndipo chifukwa ninji?
4 Kumanga nyumba kungalire ndalama zambiri, komanso kuisamalira kuti ikhalitse kumatenganso ndalama zambiri. Nchimodzimodzi ndi ukwati. Kukwatira kapena kukwatiwa kumaoneka kukhala kovuta; komabe, kusunga ukwati chaka ndi chaka kuyeneranso kulingaliridwa. Kodi kusunga unansi woterowo kumafunanji? Mbali yofunika kwambiri ndiyo kudzipereka ndi mtima wonse. Baibulo limalongosola unansi wa ukwati motere: “Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Yesu Kristu anapereka chifukwa chimodzi chokha cha Malemba cha chisudzulo ndi chilolezo cha kukwatiranso—“chigololo,” ndiko kuti, kugona ndi munthu wosakwatirana naye. (Mateyu 19:9) Ngati mukuganiza zokwatira kapena kukwatiwa, kumbukirani miyezo ya Malemba imeneyi. Ngati simuli wokonzeka kupanga choŵinda chimenechi, ndiko kuti simuli wokonzeka kuloŵa ukwati.—Deuteronomo 23:21; Mlaliki 5:4, 5.
5. Ngakhale kuti kupanga choŵinda cha ukwati kumachititsa mantha anthu ena, kodi nchifukwa ninji awo ofuna kukwatira kapena kukwatiwa ayenera kukuona kukhala kofunika kwambiri?
5 Kupanga choŵinda chimenechi kumachititsa mantha anthu ambiri. Mwamuna wachichepere wina anati: “Kudziŵa kuti aŵirife tinali ophatikana pamodzi kwa moyo wonse kunandichititsa kumva womangika, wopanikizika, wotsekerezedwa kotheratu.” Koma ngati mumakondadi munthu amene mufuna kukwatirana naye, kudzipereka kotero sikudzaoneka ngati mtolo. M’malo mwake, kudzapangitsa munthu kumva kukhala wosungika. Lingaliro la kudzipereka lotanthauzidwa muukwati lidzachititsa okwatirana kufuna kumamatirana m’nthaŵi zabwino ndi m’nthaŵi zovuta zomwe ndi kuchirikizana zivute zitani. Mtumwi wachikristu Paulo analemba kuti chikondi chenicheni “chikwirira zinthu zonse” ndipo “chipirira zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:4, 7) Mtsikana wina anati: “Kudzipereka kwa muukwati kumandipangitsa kumva wotetezereka kwambiri. Ndimamva bwino kuti tinalengeza poyera kwa ife eni ndi kwa anthu kuti tikufuna kuphatikana pamodzi.”—Mlaliki 4:9-12.
6. Kodi nchifukwa ninji kuli kwabwino kwenikweni kusathamangira ukwati pausinkhu waung’ono?
6 Kuti tikhale mwa njira ya kudzipereka kotero tiyenera kukhala okhwima m’maganizo. Chifukwa chake, Paulo akulangiza kuti Akristu angachite bwino kusakwatira kufikira ‘atapitirira unamwali wawo,’ nyengo pamene chilakolako cha kugonana chimakhala champhamvu ndipo chikhoza kusokoneza kulingalira bwino kwa munthu. (1 Akorinto 7:36) Achichepere amasintha mofulumira pamene akukula. Ambiri amene amakwatira akali aang’ono kwambiri amapeza kuti patangopita zaka zoŵerengeka, zofuna ndi zokhumba zawo limodzinso ndi za anzawo a muukwati, zimasintha. Maumboni amasonyeza kuti achichepere amene amakwatira, ali othekera kwambiri kukhala osakondwa ndipo amafuna kuthetsa ukwati kuposa aja amene amayembekezerako. Motero, musathamangire ukwati. Zaka zingapo zimene mungakhale mbeta monga wachichepere wauchikulire, zingakupatseni chidziŵitso chamtengo wapatali chimene chidzakuchititsani kukhwima ndi kukhala mwamuna kapena mkazi wabwino. Kusathamangira ukwati kungakuthandizeninso kudzidziŵa bwino inu nokha—chinthu chofunika kwambiri ngati mufuna kudzakhala ndi unansi wachipambano muukwati wanu.
DZIDZIŴENI NOKHA CHOYAMBA
7. Kodi nchifukwa ninji aja ofuna kuloŵa ukwati ayenera choyamba kudzipenda okha?
7 Kodi nkwapafupi kwa inu kundandalika mikhalidwe imene mumafuna mwa munthu amene mungakonde kukwatirana naye? Kwa ambiri nzosavuta. Komabe, bwanji za mikhalidwe yanu? Kodi muli ndi mikhalidwe yotani imene idzakuthandizani kukhala ndi ukwati wachipambano? Kodi mudzakhala mwamuna kapena mkazi wotani? Mwachitsanzo, kodi mumavomereza zolakwa zanu mosavuta ndi kulandira uphungu, kapena kodi nthaŵi zonse mumayesa kudzichinjiriza pamene muwongoleredwa? Kodi nthaŵi zambiri mumakhala wosangalala ndi wachidaliro, kapena mumakonda kukhala wachisoni, wodandaula kaŵirikaŵiri? (Miyambo 8:33; 15:15) Kumbukirani, ukwati sudzasintha umunthu wanu. Ngati paumbeta wanu muli wonyada, wamtima wapachala, kapena wamsunamo, mudzakhala chimodzimodzi ngakhale mutakwatira kapena kukwatiwa. Popeza kuti nkovuta kudziona mmene ena amationera, bwanji osapempha kholo kapena bwenzi lodalirika kumakuuzani moona mtima ndi kumakuthandizani pa umunthu wanu? Ngati mwauzidwa mbali zimene muyenera kuwongolera, yesetsani kuziwongolera musanakwatire kapena kukwatiwa.
Pamene mudakali mbeta, kulitsani mikhalidwe, zizoloŵezi, ndi maluso amene adzakuthandizani muukwati
8-10. Kodi Baibulo limapereka uphungu wotani umene ungathandize munthu kukonzekera ukwati?
8 Baibulo limatilimbikitsa kulola mzimu wa Mulungu kugwira ntchito mwa ife, kuti tikulitse mikhalidwe yonga “cikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” Limatiuzanso kuti ‘tikonzeke, tikhale atsopano mu mzimu wa mtima’ ndi kuti ‘tivale umunthu watsopano, umene unalengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.’ (Agalatiya 5:22, 23; Aefeso 4:23, 24) Kugwiritsira ntchito uphungu umenewu pamene mukali mbeta, kudzakhala monga kuika ndalama m’banki—chinthu chimene chidzakuthandizani kwambiri mtsogolo, pamene mudzakwatira kapena kukwatiwa.
9 Mwachitsanzo, ngati ndinu mkazi, phunzirani kuika chisamaliro chachikulu pa “munthu wobisika wamtima” kuposa chimene mumaika pa maonekedwe anu. (1 Petro 3:3, 4) Kudekha ndi kulama maganizo kudzakuthandizani kukhala ndi nzeru, “korona wokongola” weniweni. (Miyambo 4:9; 31:10, 30; 1 Timoteo 2:9, 10) Ngati ndinu mwamuna, phunzirani kuchitira akazi mokoma mtima ndi mwaulemu. (1 Timoteo 5:1, 2) Pamene mukuphunzira kupanga zosankha ndi kusenza mathayo, phunziraninso kukhala wodekha ndi wodzichepetsa. Mzimu wopondereza udzaloŵetsa ukwati wanu m’mavuto.—Miyambo 29:23; Mika 6:8; Aefeso 5:28, 29.
10 Ngakhale kuti kusintha maganizo a munthu m’mbali zimenezi nkovuta, kuli chinthu chimene Akristu onse ayenera kugwirirapo ntchito. Ndipo kudzakuthandizani kukhala mkazi kapena mwamuna wabwino muukwati.
ZIMENE MUYENERA KUFUNA MWA WOKWATIRANA NAYE
11, 12. Kodi aŵiriwo angadziŵe motani kuti ali oyenererana kapena ayi?
11 Kodi mkhalidwe wa kwanuko ndi uja wodzisankhira wekha munthu wokwatirana naye? Ngati ndi choncho, kodi muyenera kuyendetsa motani zinthu ngati mwakopeka ndi mkazi kapena mwamuna? Choyamba, dzifunseni kuti, ‘Kodi ine ndifunadi kukwatira kapena kukwatiwa?’ Kuseŵera ndi malingaliro a wina mwa kudzutsa ziyembekezo zonama ndiko nkhanza yeniyeni. (Miyambo 13:12) Ndiyeno dzifunseninso kuti, ‘Kodi ndili wokonzeka kukwatira kapena kukwatiwa?’ Ngati yankho lanu pa mafunso aŵiriŵa ndi lakuti inde, njira zotsatirapo zimene muyenera kutenga zidzakhala zosiyanasiyana zikumadalira pa mkhalidwe wa kwanuko. M’maiko ena, mutapenda munthuyo kwakanthaŵi, mungamfikire ndi kumuuza chifuno chanu kuti mukufuna kudziŵana naye bwino. Ngati akana, musaumirire kwambiri kwakuti achite kukukalipirani. Kumbukirani, nayenso ayenera kupanga chosankha pankhaniyo. Komabe, ngati avomera, mungapangane za kuchitira pamodzi zinthu zina zoyenera. Zimenezi zidzakupatsani mpata wakuona ngati kukwatirana ndi munthuyo kudzakhala kwanzeru.a Kodi muyenera kufunanji mwa iye panthaŵiyo?
12 Kuti tiyankhe funso limenelo, tayerekezerani ziŵiya zoimbira ziŵiri, tinene kuti piyano ndi gitale. Ngati chilichonse chitchunidwa bwino ndi kulizidwa pachokha, chingatulutse maimbidwe okongola kwambiri. Komabe, kodi chingachitike nchiyani ngati zonse zilizidwa pamodzi? Tsopano ziyenera kutchunidwa mwa njira yakuti ziyenderane. Nchimodzimodzinso kwa inu ndi amene mufuna kukwatirana naye. Aliyense wa inu wayesayesa “kutchuna” mikhalidwe ya umunthu wake payekha. Koma tsopano funso nlakuti: Kodi muli m’tchuni kwa wina ndi mnzake? M’mawu ena, kodi muli oyenererana?
13. Kodi nchifukwa ninji kuli kopanda nzeru kupalana chibwenzi ndi munthu wosiyana naye chikhulupiriro?
13 Nkofunika kwambiri kuti aŵirinu mukhale ndi chikhulupiriro chimodzi ndi mapulinsipulo ofanana. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupirira osiyana.” (2 Akorinto 6:14; 1 Akorinto 7:39) Ngati mukwatirana ndi munthu wosagwirizana nanu m’chikhulupiriro kwa Mulungu, nkothekera kwambiri kuti padzakhala kusamvana kwakukulu. Koma kudzipereka kogwirizana kwa Yehova Mulungu ndiko maziko a umodzi olimba koposa. Yehova amafuna kuti mukhale achimwemwe ndi kusangalala ndi unansi woyandikana kwambiri ndi munthu amene mukwatirana naye. Amafuna kuti mumangiriridwe kwa Iye ndi kwa wina ndi mnzake ndi chingwe cha nkhosi zitatu cha chikondi.—Mlaliki 4:12.
14, 15. Kodi kukhala ndi chikhulupiriro chimodzi ndiko mbali yokha yochititsa umodzi muukwati? Fotokozani.
14 Pamene kuli kwakuti kulambira Mulungu pamodzi ndiko kuli imodzi ya mbali zofunika koposa pa umodzi, palinso zina zoloŵetsedwamo. Kuti mukhale m’tchuni kwa wina ndi mnzake, muyenera kukhala ndi zonulirapo zofanana ndi amene mufuna kukwatirana naye. Kodi zonulirapo zanu nzotani? Mwachitsanzo, kodi aŵirinu mumalingalira motani ponena za kukhala ndi ana? Kodi ndi zinthu zotani zimene zili zofunika koposa m’moyo wanu?b (Mateyu 6:33) Muukwati wachipambano chenicheni, okwatiranawo amakhala mabwenzi enieni ndipo amakonda kukhala pamodzi. (Miyambo 17:17) Pachifukwa chimenechi, afunikira kukhala ofanana m’zokonda zawo. Nkovuta kusunga ubwenzi wathithithi—makamaka ukwati—ngati anthuŵo ali osiyana. Ngakhale ndi choncho, ngati amene mufuna kukwatirana naye amakonda kuchita chinthu china, monga kuyenda maulendo, ndipo inu simukonda zimenezo, kodi ndiye kuti simuyenera kukwatirana? Osati kwenikweni. Mwinamwake zilipo zinthu zina zofunika kwambiri zimene nonsenu mumakonda. Ndiponso, mungapatse chimwemwe amene mufuna kukwatirana nayeyo mwa kuchita naye zinthu zoyenera zimene iye amakonda.—Machitidwe 20:35.
15 Ndithudi, kuyenererana kumadalira kwakukulukulu pa mmene aŵirinu mungakhozere kusintha kuti muyenererane ndi mnzanuyo, osati kwenikweni mmene mulili ofanana. M’malo mofunsa kuti, “Kodi timavomerezana pa chilichonse?” ndi bwino kufunsa kuti: “Kodi chimachitika nchiyani pamene sitivomerezana? Kodi tingakambirane mavuto mwabata ndi molemekezana? Kapena kodi kukambitsirana kwathu kaŵirikaŵiri kumathera m’mikangano yokalipirana?” (Aefeso 4:29, 31) Ngati mukufuna kukwatira kapena kukwatiwa, khalani maso ndi munthu wonyada ndi wodzigangira, wosafuna kulolera, kapena wolamulira nthaŵi zonse ndi kuchita mwamachenjera kuti apeze zimene akufuna.
DZIŴANI PASADAKHALE
16, 17. Kodi mwamuna kapena mkazi ayenera kufuna chiyani mwa munthu amene afuna kukwatirana naye?
16 Mumpingo wachikristu, aja amene amapatsidwa mathayo ‘amayamba ayesedwa.’ (1 Timoteo 3:10) Inunso mungagwiritsire ntchito pulinsipulo limeneli. Mwachitsanzo, mkazi angadzifunse kuti, “Kodi mwamunayu ali ndi mbiri yotani? Kodi mabwenzi ake ndani? Kodi amasonyeza kudziletsa? Kodi amachita motani ndi okalamba? Kodi amachokera ku banja lotani? Kodi amachita motani ndi banja lake? Kodi ndalama amaziona motani? Kodi amamwetsa moŵa? Kodi ali wamtima wapachala, ndipo mwina wachiwawa? Kodi ali ndi mathayo otani mumpingo, ndipo amawachita motani? Kodi ndikhoza kumpatsa ulemu waukulu?”—Levitiko 19:32; Miyambo 22:29; 31:23; Aefeso 5:3-5, 33; 1 Timoteo 5:8; 6:10; Tito 2:6, 7.
17 Mwamuna angadzifunse kuti: “Kodi mkaziyu amasonyeza chikondi ndi ulemu kwa Mulungu? Kodi ali wokhoza kusamalira nyumba? Kodi banja lake lidzafunanji kwa ife? Kodi ali wanzeru, wantchito, ndi wosawononga ndalama? Kodi amakonda kulankhula za chiyani? Kodi amadera nkhaŵa kwenikweni za ena, kapena amangosamala zake, wodyerana miseche? Kodi ali wodalirika? Kodi ali wokonzeka kugonjera ku umutu, kapena kodi ali waliuma, mwinamwake wa mzimu wachipanduko?”—Miyambo 31:10-31; Luka 6:45; Aefeso 5:22, 23; 1 Timoteo 5:13; 1 Petro 4:15.
18. Ngati muona zifooko zazing’ono m’chibwenzi chanu, kodi muyenera kukumbukira chiyani?
18 Musaiŵale kuti mukuchita ndi mbadwa ya Adamu yopanda ungwiro, osati mwamuna kapena mkazi wotchuka uja wa m’mabuku a zachikondi. Munthu aliyense ali ndi zophophonya, ndipo zina za zimenezi mudzangofunikira kuzinyalanyaza—ponse paŵiri zanu ndi za amene mufuna kukwatirana naye. (Aroma 3:23; Yakobo 3:2) Ndiponso, chifooko chimene chingaoneke chingapereke mpata wa kukula. Mwachitsanzo, tinene kuti mkati mwa chibwenzi chanu mukhala ndi mkangano. Talingalirani: Ngakhale anthu amene amakondana ndi kulemekezana kwambiri, nthaŵi zina amatsutsana. (Yerekezerani ndi Genesis 30:2; Machitidwe 15:39.) Kodi mwina aŵirinu mungofunikira ‘kulamulira mtima’ wanu mokulirapo ndi kuphunzira kuthetsa mikangano mwamtendere? (Miyambo 25:28) Kodi amene mukufuna kukwatirana naye amasonyeza kuti akufuna kuwongolera? Kodi inu mumatero? Kodi mungaphunzire kukhala wosakwiya msanga, woleza mtima? (Mlaliki 7:9) Kuphunzira kuthetsa mavuto kungakhazikitse njira ya kulankhulana koona mtima kumene kuli kofunika kwambiri ngati aŵirinu mukwatirana.—Akolose 3:13.
19. Kodi chanzeru kuchita nchiyani ngati mkati mwa chibwenzi mwabuka mavuto aakulu?
19 Koma bwanji ngati muona zinthu zimene zikuvutitsani maganizo kwambiri? Zikayikiro zoterozo ziyenera kulingaliridwa mosamala. Mosasamala kanthu za chikondi chimene mungakhale nacho kapena chikhumbo cha kukwatira kapena kukwatiwa, musanyalanyaze zododometsa zazikulu. (Miyambo 22:3; Mlaliki 2:14) Ngati muli pachibwenzi ndi munthu amene mukumkayikira kwambiri, kuli kwanzeru kuthetsa chibwenzicho ndi kusadzipereka kwa munthu wotero.
KHALANI NDI CHIBWENZI CHOLEMEKEZEKA
20. Kodi ndi motani mmene apachibwenzi otomerana angadzisungire mwanjira yopanda chinenezo?
20 Kodi mungakhale motani ndi chibwenzi cholemekezeka? Choyamba, tsimikizirani kuti mukudzisungira mwanjira yopanda chinenezo. Kodi kwanuko, kugwirana manja, kupsompsonana, ndi kukumbatirana kwa anthu osakwatirana kumaonedwa kukhala mkhalidwe woyenera? Ngakhale ngati machitidwe osonyezana chikondi otero sali onyumwitsa ena, ayenerabe kuchitika kokha pamene chibwenzicho chafika pamlingo wakuti ukwati wakhala wotsimikizirika. Samalani kuti machitidwe osonyezana chikondi asapyole malire ndi kukhala chidetso kapena ngakhale kufikira pakuchita dama. (Aefeso 4:18, 19; yerekezerani ndi Nyimbo ya Solomo 1:2; 2:6; 8:5, 9, 10.) Chifukwa chakuti mtima uli wonyenga, kungakhale kwanzeru kupeŵa kukhala muli aŵiriŵiri m’nyumba, m’chipinda, m’galimoto loimikidwa, kapena kwina kulikonse kumene kungapereke mpata wa kuchita cholakwa. (Yeremiya 17:9) Kukhala ndi chibwenzi choyera kumapereka umboni wabwino wakuti muli odziletsa ndi kuti mumaika nkhaŵa yanu yopanda dyera patsogolo pa zofuna zanu kaamba ka ubwino wa mnzanu. Chofunika koposa nchakuti, chibwenzi choyera chimakondweretsa Yehova Mulungu, yemwe amalamula atumiki ake kupeŵa chodetsa ndi dama.—Agalatiya 5:19-21.
21. Kodi ndi kulankhulana koona mtima kotani kumene kungakhale kofunika kuti pakhale chibwenzi cholemekezeka?
21 Chachiŵiri, chibwenzi cholemekezeka chimaphatikizaponso kulankhulana koona mtima. Pamene chibwenzi chanu chikuyandikira ukwati, nkhani zina zidzafuna kukambitsirana koona mtima. Kodi mudzakhala kuti? Kodi nonse aŵiri mudzagwira ntchito? Kodi mukufuna kukhala ndi ana? Ndiponso, ndi bwino kuulula zinthu zina, mwinamwake za moyo wakumbuyo, zimene zingayambukire ukwati. Zimenezo zingaphatikizepo ngongole zazikulu kapena mathayo kapena nkhani za thanzi, monga matenda aakulu alionse kapena mkhalidwe wina umene mungakhale nawo. Popeza kuti anthu ambiri amene ali ndi HIV (kachirombo kochititsa AIDS) samasonyeza zizindikiro mwamsanga, sikungakhale kulakwa ngati munthu kapena makolo osamala apempha kuti munthu amene sanali kuyenda bwino kumbuyoku kapena amene anali kugwiritsira ntchito anamgoneka mwa jekeseni, akapimitse mwazi kuona ngati ali ndi AIDS. Ngati kupimako kupeza kuti munthuyo ali ndi kachirombo, iye sayenera kukakamiza mnzake wofuna kukwatirana naye kuti apitizire chibwenzi chawo ngati kuti mnzakeyo tsopano akufuna kuti chithe. Ndithudi, munthu aliyense amene kumbuyoku anali ndi moyo wokhala pangozi yotenga matenda angachite bwino kupita yekha kukapimitsa mwazi kaamba ka AIDS asanayambe kupalana chibwenzi ndi wina.
KUONA NDI ZAPAMBUYO PA PHWANDO LA UKWATI
22, 23. (a) Kodi ndi motani mmene munthu angalepherere kukhala wachikatikati pokonzekera phwando la ukwati? (b) Kodi ndi lingaliro loyenera lotani limene liyenera kusungidwa polingalira za phwando la ukwati ndi ukwati?
22 M’miyezi yomalizira ukwati utayandikira, mwachionekere nonse aŵiri mudzakhala otanganitsidwa kwambiri ndi kukonzekera phwando la ukwati. Mungachepetse nkhaŵa zazikulu mwa kukhala achikatikati. Phwando la ukwati ladzaoneni lingakondweretse achibale ndi anthu ena, koma lingasiye okwatiranawo ndi mabanja awo ali otopa kwambiri ndi kuwasiyanso pa vuto la ndalama. Kutsatira chizoloŵezi chakumaloko kungakhale kwabwino, koma kutsatira machitidwe opambanitsa ndi ampikisano kungaphimbe tanthauzo la chochitikacho ndi kukusoŵetsani chisangalalo chimene muyenera kukhala nacho. Pamene kuli kwakuti nkofunika kumvetsera malingaliro a ena, mkwati ndiye kwenikweni ali ndi thayo la kugamula zimene zidzachitika pa phwando la ukwati.—Yohane 2:9.
23 Kumbukirani kuti phwando la ukwati wanu lidzakhala tsiku limodzi chabe, koma ukwati wanu ndi wa moyo wonse. Peŵani kuika maganizo onse pa chochitika cha kukwatirana. M’malo mwake, yang’anani kwa Yehova kaamba ka chitsogozo, ndipo konzekerani pasadakhale moyo wa kukhala muukwati. Mukatero, mudzakhala mutakonzekera bwino ukwati wachipambano.
a Zimenezi zimagwira ntchito m’maiko kumene kuli kololeka pakati pa Akristu kwa mwamuna ndi mkazi kupita kokacheza.
b Ngakhale mumpingo wachikristu, mungakhale ena oima ndi mwendo umodzi, titero kunena kwake. M’malo mokhala atumiki a Mulungu amtima wonse, iwo angasonkhezeredwe ndi malingaliro ndi makhalidwe a dzikoli.—Yohane 17:16; Yakobo 4:4.