Chifukwa Chimene Kulambira Kwachikristu Kuliri Koposa
Mfundo Zazikulu Zochokera m’Kalata ya kwa Ahebri
YEHOVA MULUNGU anayambitsa mbali zoposa zakulambira pamene anatumiza Mwana wake, Yesu Kristu, ku dziko lapansi. Zinali tero chifukwa chakuti Yesu, Woyambitsa Chikristu, ngwoposa angelo ndi mneneri Mose. Unsembe wa Kristu ngwaukulu koposa utayerekezedwa ndi uja wa Alevi m’Israyeli wakale. Ndipo nsembe ya Yesu njoposa kwambiri nyama zoperekedwa pansi pa Chilamulo cha Mose.
Mfundozi zamveketsedwa bwino lomwe m’kalata ya kwa Ahebri. Mwachiwonekere inalembedwa ndi mtumwi Paulo m’Roma pafupifupi 61 C.E. ndipo inatumizidwa kwa akhulupiriri Achihebri m’Yudeya. Kuchokera pachiyambi, Akristu Achigiriki ndi Achiasia anavomereza kuti Paulo ndiye adailemba, ndipo ichi chachirikizidwa ponse paŵiri ndi kuzoloŵerana kozama kwa wolembayo ndi Malemba Achihebri ndi kugwiritsira ntchito kwake mawu oyamba otsatirika, chimene mtumwiyo anachizoloŵera kuchita. Iye mwina sanalitchule dzina lake chifukwa cha tsankho la Ayuda lotsutsana naye ndipo chifukwa chakuti anadziŵika monga “mtumwi wa anthu amitundu.” (Aroma 11:13) Tiyeni tsopano tipende mosamalitsa mbali za Chikristu zoposazo, monga momwe zavumbulidwira m’kalata ya Paulo kwa Ahebri.
Kristu Woposa Angelo ndi Mose
Choyamba kusonyezedwa ndicho udindo waukulu wa Mwana wa Mulungu. (1:1-3:6) Angelo amamgwadira iye, ndipo ulamuliro wake wachifumu wazikidwa pa Mulungu. Chotero tiyenera kupereka chisamaliro chapadera ku zimene Mwana anazilankhula. Kuwonjezera apa, tiyenera kukumbukira kuti ngakhale kuti mwamunayo Yesu anali wochepa pa angelo, iye anakwezedwa pamwamba pawo napatsidwa ulamuliro padziko lokhalidwa ndi anthu lomwe likudzalo.
Yesu Kristu ngwoposanso Mose. Motani? Eya, Mose anali kokha kalinde m’nyumba ya Mulungu ya Israyeli. Komabe, Yehova anaika Yesu woyang’anira pa nyumba yonseyo, kapena mpingo wa anthu a Mulungu.
Akristu Aloŵa Mumpumulo wa Mulungu
Chotsatira, mtumwiyo akusonya kuti nkotheka kuloŵa mumpumulo wa Mulungu. (3:7–4:13) Aisrayeli owonjoledwa muukapolo wa Aigupto analephera kuloŵamo chifukwa chakuti anali osamvera ndipo analibe chikhulupiriro. Komabe tingaloŵe mumpumulowo ngati tisonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu ndi kutsanzira Kristu momvera. Pamenepo, mmalo mwakungosunga Sabata pamlungu uliwonse, tidzasangalala masiku onse ndi madalitso oposa kupuma kuntchito zadyera zonse.
Kuloŵa mumpumulo wa Mulungu ndiko chimodzi cha zolonjezedwa ndi mawu ake, amene ‘ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse napyoza kufikira kugaŵira moyo ndi mzimu.’ Iwo amatero mlingaliro lakuti amapyoza nazindikira zolinga ndi zikhoterero, nagaŵa pakati zikhumbo zakuthupi ndi kaimidwe ka maganizo. (Yerekezerani ndi Aroma 7:25.) Ngati “wathu moyo,” kapena moyo monga munthu payekha, wagwirizana ndi “mzimu” waumulungu, kapena kaimidwe, tingaloŵe mumpumulo wa Mulungu.
Unsembe ndi Pangano Zoposazo
Chotsatira Paulo akusonyeza kuposa kwa unsembe wa Kristu ndi pangano latsopano. (4:14–10:31) Yesu Kristu wosachimwayo ngwachifundo kwa anthu ochimwa chifukwa chakuti mofanana nafe, iye wayesedwa m’mbali zonse. Kuwonjezera apa, Mulungu wamuika kukhala ‘wansembe wanthaŵi zonse monga mwa dongosolo la Melikizedeke.’ Mosiyana ndi akulu ansembe Achilevi, Yesu ali ndi moyo wosakhoza kufa ndipo motero safunikira mloŵa mmalo m’ntchito yake yopulumutsa. Iye safunikira kupereka nsembe za nyama, popeza kuti walipereka thupi lake loposalo lopanda uchimo ndipo waloŵa kale m’mwamba ndimtengo wa mwazi wake.
Pangano latsopano, lokhalitsidwa lalamulo ndi mwazi wa Yesu, nloposa pangano la Chilamulo. Awo okhala m’pangano latsopano ali ndi malamulo a Mulungu m’mitima yawo ndipo amasangalala ndikukhululukidwa machimo. (Yeremiya 31:31-34) Kuyamikira ichi kumaŵasonkhezera kupanga chilengezo chapoyera cha chiyembekezo chawo ndi kusonkhana limodzi ndi akhulupiriri anzawo. Mosiyana ndi iwo, ochimwira dala alibenso nsembe ya machimo.
Chikhulupiriro Nchofunika!
Kuti tipindule ndi pangano latsopano loposalo, timafunikira chikhulupiriro. (10:32–12:29) Chipiriro chimafunikanso ngati titi tilandire zimene Yehova walonjeza. Monga chotilimbikitsa kupirira, tiri ndi ‘mtambo waukulu’ wamboni zotizinga zomwe zinakhalako Chikristu chisanakhale. Komabe, tiyenera makamaka kulingalira mosamalitsa njira yopanda banga ya Yesu pansi pakuvutika. Kuvutika kulikonse kumene Mulungu amakulola kutigwera ife kungalingaliridwe mwapang’ono kukhala chilango chimene chingabweretse chipatso chamtendere cha chilungamo. Kudalirika kwa malonjezo a Yehova kuyenera kuwonjezera chikhumbo chathu cha kupereka utumiki wopatulika kwa iye “ndi mantha aumulungu ndi ulemu.”—NW
Paulo akumaliza ndi machenjezo. (13:1-25) Chikhulupiriro chiyenera kutisonkhezera kusonyeza chikondi cha pa abale, kuchereza alendo, kukumbukira akhulupiriri anzathu ovutitsidwa, kulemekeza ukwati, ndi ‘kukwanira ndi zimene tiri nazo.’ Tiyenera kutsanzira chikhulupiriro cha otitsogolera mumpingo ndi kuŵagonjera. Kuwonjezera apa, tiyenera kupeŵa mpatuko, tinyamule chitonzo chomwe Yesu ananyamula, ‘tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu,’ ndi kupitirizabe kuchita zabwino. Mkhalidwe woterowo ulinso pakati pa mbali zoposa za Chikristu chowona.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 24]
Maubatizo Osiyanasiyana: Mbali za kulambira pa chihema cha Israyeli zinakhudza “zakudya ndi zakumwa zokha ndi maubatizo osiyanasiyana.” (Ahebri 9:9, 10, NW) Maubatizoŵa anali masambidwe amwambo ofunidwa ndi Chilamulo cha Mose. Zotengera zodetsedwa zinatsukidwa, ndipo dzoma lakuyeretsa linaphatikizapo kuchapa zovala za munthuwe ndi kusamba. (Levitiko 11:32; 14:8, 9; 15:5) Ansembe adasamba, ndipo zinthu zogwiritsira ntchito popereka nsembe zopsereza zinatsukidwa m’madzi. (Eksodo 29:4; 30:17-21; Levitiko 1:13; 2 Mbiri 4:6) Koma “maubatizo osiyanasiyana” sanaphatikizepo mwambo wa ‘kubatiza zikho, miphika, ndi zotengera zamkuwa’ kochitidwa ndi Ayuda ena panthaŵi imene Mesiya anafika; ndipo Ahebri 9:10 sakusonya kuubatizo womizidwa m’madzi wochitidwa ndi Yohane Mbatizi kapena ubatizo wa awo ozindikiritsa kudzipereka kwawo kwa Mulungu monga Akristu.—Mateyu 28:19, 20; Marko 7:4; Luka 3:3.