Nyimbo 195
Iri Nditsiku la Yehova
1. Tsiku nla Yehova. Kulamula nkwake.
Waikatu mu Ziyoni mwala.
Kwezanidi mawu Kuyamika M’lungu,
Poti mwa Yehova timakhulupira.
(Korasi)
2. Kristu alamula, Mapeto afika.
Dziko la Satana likupita.
Lalikira Mawu; Thandiza ofatsa
Kumveratu malamulo a Mulungu.
(Korasi)
3. Titama Mfumuyo; Imatidabwitsa.
Ikudza mudzina la Mulungu.
Loŵa pazipata! O tiyanjidwetu
Kuti tikhalebe mu’tumiki wake.
(KORASi)
Udzetsanji, Ufumu wa Ya?
Chilakiko cha Cho’nadi.
Nchiyaninso, Ufumu wa Ya?
Moyo wosatha m’chimwemwe.
Tamani Mfumu Yosatha
Ka’mba ka chikondicho.