Nyimbo 225
Kuyandikira kwa Yehova
1. Chiyanjo chanu O Ya,
Ndichodalirika.
Monga odzipereka,
Tiyandikira’nu.
Ndi chuma chapatali
Ngati muli bwenzi.
Chikondi chanu nchoyera.
Tikuyamikani.
2. Ndinu Mbusa wamkulu,
Mutisamalira
Mwa Kristu mwatidzetsa,
Talisiya dziko.
Mwatikhululukira
Mwachifundo chanu.
Ndinu wabwino; tikondwa
Pokhala ndi inu.
3. Tinaphunzira zanu
Ndi kukutamani.
Chikondi ndi ukoma,
Zimatidabwitsa.
Tifuna kudziŵanu,
Ndi kuyandikabe.
Mutichitire mokoma;
Tichite chifuno.