Nyimbo 61
“Ndine Yehova”!
1. Imvani mafumu a dziko
Anyalanyazadi Yehova.
Sasankha kuvomereza ufumu,
Ndipo anyoza mphamvu yake.
Kodi ndani anagwetsa magulu,
Nawonongedwadi mwamanyazi?
Indedi ndani anatontholetsa
Ndi kupatsa anthu chipambano?
(Korasi)
2. Mafumu a dziko amvana
Mukutsutsana ndi Mwanayo!
Koma amphamvuwo ali ndi mantha,
Pomwe amphaŵi abuula.
Kodi ndani adzathyola golilo
Napulumutsa ofatsa m’dziko?
Ndani adzasandutsa chilungamo
Chisoni nachikhala chimwemwe?
(KORASI)
Ndine Mbuye; palibe wina.
Ndine Mbuye; Ndinedi Yehova.
Ndakhazika Mfumu yanga paphiri;
Mgwadireni! Yesu alamula.