Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 6/15 tsamba 9-12
  • Kuleza Mtima—Nchifukwa Ninji Sikumaonekaoneka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuleza Mtima—Nchifukwa Ninji Sikumaonekaoneka?
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zitsanzo za Kusaleza Mtima
  • Zochititsa Kusaleza Mtima
  • Kuleza Mtima​—Chifukwa Chake Kuli Kofunika Kwambiri
  • Zitsanzo Zolimbikitsa
  • Mfupo za Kuleza Mtima
  • Pitirizani Kukhala Oleza Mtima
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kodi Mungasonyeze Kuleza Mtima?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Tsanzirani Kuleza Mtima kwa Yehova
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Tsanzirani Kuleza Mtima kwa Yehova ndi Yesu
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 6/15 tsamba 9-12

Kuleza Mtima​—Nchifukwa Ninji Sikumaonekaoneka?

EMILIO anali m’zaka zake za ma 60.a Iye anali atapita ku Oahu pa ulendo wachisoni​—kukaika mwana wake wamwamuna wachikulire. Pamene anali kuyenda mu msewu wina wabata wa m’mbali mwa kaphiri ndi kumakambitsirana ndi mabwenzi ake ena, Emilio anadzidzimutsidwa ndi galimoto limene linali kubwera chafutambuyo mwaliŵiro kwambiri mu msewu wochokera panyumba ina. Galimotolo linatsala pang’ono kumgunda, ndipo chifukwa cha kukwiya ndi kusaleza mtima, Emilio anakalipira woyendetsayo ndi kumenya galimoto ndi dzanja lake. Ndiyeno panabuka mkangano. Zikuchita ngati kuti woyendetsayo anakankha Emilio, amene anagwa namenyetsa mutu wake m’kanjira ka konkire ka m’mbali mwa msewu. Patapita masiku oŵerengeka, Emilio anafa chifukwa cha kuvulala kwake mutu. Nchotulukapo chomvetsa chisoni chotani nanga!

Tikukhala m’dziko limene kuleza mtima kuli mkhalidwe wosaonekaoneka. Oyendetsa galimoto owonjezereka akuyendetsa mwaliŵiro kwambiri. Ena amayendetsa mwangozi kwambiri​—molondola pafupi kwambiri galimoto zina​—kuposa pa lamulo la liŵiro. Enanso amayendetsa galimoto mokhotakhota chifukwa chakuti sangathe kupirira kukhala akutsatira m’mbuyo mwa galimoto lina. Panyumba, ziŵalo za banja zingamakwiyirane ndi kukhala zachiwawa. Ngakhalenso Akristu ena angakwiye kwambiri chifukwa cha zophophonya kapena zolakwa za abale awo auzimu.

Kodi nchifukwa ninji kuleza mtima sikumaonekaoneka? Kodi kwakhala kotero nthaŵi zonse? Kodi nchifukwa ninji kuli kovuta kwambiri kukhala woleza mtima m’nthaŵi yathu?

Zitsanzo za Kusaleza Mtima

Baibulo limasimba za mkazi wina amene sanayembekezere kufunsa mwamuna wake asanapange chosankha chachikulu. Dzina lake anali Hava. Popitira patsogolo Adamu, mwinamwake chifukwanso cha kusaleza mtima, anadya chipatso choletsedwa. (Genesis 3:1-6) Bwanji za mwamuna wake? Nayenso angakhale atasonyeza kusaleza mtima mwa kutsatira Hava kuloŵa m’tchimo popanda kufikira choyamba Atate wake wakumwamba, Yehova, kuti afunsire chithandizo kapena chitsogozo. Umbombo wawo, mwinamwake limodzi ndi kusaleza mtima zimene zinawaloŵetsa mu uchimo, zinali ndi zotulukapo za imfa kwa ife tonse. Talandiranso kwa iwo choloŵa cha chikhoterero cha kuchita machimo, kuphatikizapo a kuuma khosi ndi a kusaleza mtima.​—Aroma 5:12.

Patapita pafupifupi zaka 2,500 makolo athu oyamba atachimwa, anthu osankhidwa a Mulungu, Aisrayeli, anasonyeza kusoŵa chikhulupiriro kwakukulu kosalekeza, ndi kusaleza mtima. Ngakhale kuti Yehova anali atangowapulumutsa kumene mu ukapolo ku Igupto, “anaiŵala ntchito zake msanga” ndipo “sanalindira uphungu wake.” (Salmo 106:7-14) Iwo anagwera m’cholakwa chachikulu mobwerezabwereza chifukwa chakuti sanali oleza mtima. Anapanga mwana wang’ombe wagolidi ndi kumlambira; anang’ung’udza ponena za chakudya cha mana chimene Yehova anawapatsa; ndipo ambiri a iwo anapandukiradi Mose, woimira wosankhidwa mwaumulungu ndi Yehova. Zoona, kusaleza mtima kwawo kunawatsogolera ku chisoni ndi tsoka.

Mfumu yaumunthu yoyamba ya Israyeli, Sauli, inataya mwaŵi wa ana ake wa kukhala omloŵa ufumu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti inalephera kuyembekezera mneneri Samueli, amene anayenera kupereka nsembe kwa Yehova. Kuwopa munthu kunachititsa Sauli kupitira patsogolo Samueli ndi kupereka nsembe. Tangolingalirani mmene anamvera pamene Samueli anatulukira Sauli atangomaliza kumene mwambowo! Akanangoyembekezera kwa mphindi zina zoŵerengeka chabe!​—1 Samueli 13:6-14.

Hava akanangoyembekezera Adamu m’malo mwa kutchera chipatsocho modudukira! Aisrayeli akanangokumbukira za kuyembekezera uphungu wa Yehova! Inde, kuleza mtima kukanapulumutsa iwo ndi ife pa zisoni zambiri ndi mavuto.

Zochititsa Kusaleza Mtima

Baibulo limatithandiza kuzindikira chochititsa chachikulu cha kusaleza mtima lerolino. Timoteo Wachiŵiri chaputala 3 amafotokoza za mbadwo wathu uno kukhala ukukhala ndi moyo mu “nthaŵi zoŵaŵitsa.” Amati anthu “adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza . . . osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino,” (Mavesi 2, 3) Umbombo wotero ndi mkhalidwe waliuma umakhala m’mitima ndi m’maganizo a anthu ambiri, ukumachititsa zinthu kukhala zovuta kwa onse, ngakhale kwa Akristu enieni, kuti asonyeze kuleza mtima. Pamene tiona anthu adziko akuyendetsa galimoto mwaliŵiro kwambiri kapena kuloŵera ena kutsogolo kapena kutitukwana, kuleza mtima kwathu kungayesedwe kwambiri. Tingayesedwe kuwatsanzira kapena kuwabwezera, motero tikumafanana nawo pa mkhalidwe wawo wa kunyada.

Nthaŵi zina ali malingaliro athu olakwa amene amatichititsa kutaya mkhalidwe wa kuleza mtima. Taonani mmene Mfumu yanzeru Solomo anasonyezera mgwirizano umene uli pakati pa mkhaliwe wa phuma, wa kalingaliridwe kolakwa ndi mtima wapachala, wofulumira kupsa mtima: “Wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima. Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m’chifuwa cha zitsiru.” (Mlaliki 7:8, 9) Ngati tipatula nthaŵi yakuti tidziŵe chithunzi chonse cha mkhalidwe wonse wa nkhani tisanachitepo kanthu, mwachionekere tidzakhala omvetsetsa kwambiri, achifundo kwambiri, oleza mtima kwambiri ndi ena. Komanso, mzimu wodzitukumula, ndi waliuma ungatichititse kukhala ofinimpha maganizo, amtima wapachala, ndi opwetekedwa mtima, monga ngati Aisrayeli ong’ung’udza, ouma khosi amene anasautsa Mose.​—Numeri 20:2-5, 10.

Chochititsa china cha kusaleza mtima kowonjezereka kwa dzikoli ndicho mkhalidwe wake wa kupanda chiyembekezo, umene ulipo chifukwa cha kutalikirana ndi Yehova. Davide anafotokoza za kufunika kwa munthu kuyembekeza mwa Yehova: “Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa iye.” (Salmo 62:5) Anthu ambiri amene sadziŵa Yehova ali ndi lingaliro loona pafupi ndi losatsimikizirika, chotero amayesayesa kupeza chikondwerero chilichonse chaching’ono ndi phindu limene angapeze asanafe. Mofanana ndi atate wawo wauzimu, Satana Mdyerekezi, kaŵirikaŵiri iwo samasamala za mmene zochita zawozo zingayambukirire ena.​—Yohane 8:44; 1 Yohane 5:19.

Mposadabwitsa kuti lerolino kuleza mtima sikumaonekaoneka. Dongosolo la zinthu limeneli loipa ndi ladyera, limene mulungu wake ali Satana, ndi zikhoterero zauchimo za thupi lathu lochimwali zimapangitsa zinthu kukhala zovuta kwa aliyense, ngakhale kwa oona mtima, kuti akhale oleza mtima. Komabe, Baibulo limatilimbikitsa ‘kuleza mtima,’ makamaka pa kukwaniritsidwa kwa zifuno za Mulungu. (Yakobo 5:8) Kodi nchifukwa ninji kuleza mtima kuli kofunika kwambiri? Kodi ndi mfupo zotani zimene kungatipatse?

Kuleza Mtima​—Chifukwa Chake Kuli Kofunika Kwambiri

“Kumathandiza awo okha amene amaimirira ndi kuyembekezera.” Mawu amenewo ananenedwa ndi wolemba ndakatulo Wachingelezi John Milton zaka zoposa mazana atatu zapitazo m’ndakatulo yake yakuti “On His Blindness.” Kumayambiriro kwa ndakatuloyo, anafotokoza za kugwiritsidwa mwala ndi nkhaŵa yake pa malingaliro ake a kulephera kutumikira Mulungu mokwanira chifukwa chakuti anakhala wakhungu m’zaka zake za ma 40. Koma monga momwe mzera womaliza wogwidwa mawuwo wa ndakatulo ukusonyezera, anazindikira kuti munthu angalambire Mulungu mwa kupirira nsautso moleza mtima ndi kufunafuna modekha mipata ya kumtumikira imene ilipo. Milton anaona kufunika kwa kudalira pa Mulungu moleza mtima.

Ambiri a ife tingakhale tili ndi maso oona bwino, koma tonsefe tili ndi zimene timalephera kuchita zimene zingatichititse kukhala akupsa mtima kapena ankhaŵa. Kodi ndimotani mmene tingapezere ndi kusonyezera kuleza mtima?

Zitsanzo Zolimbikitsa

Baibulo limatipatsa zitsanzo zingapo za kuleza mtima. Kuleza mtima kwa Yehova kumakhozetsa anthu miyandamiyanda kupeza moyo wosatha. (2 Petro 3:9, 15) M’pempho lake lokoma mtima lakuti tisenze goli lake ndi ‘kupeza mpumulo wa miyoyo [yathu],’ Yesu amasonyeza mwangwiro kuleza mtima kwabwino koposa kwa Atate wake. (Mateyu 11:28-30) Kusinkhasinkha pa zitsanzo za Yehova ndi Yesu kungatithandize kukhala oleza mtima kwambiri.

Munthu amene anaoneka kukhala ndi chifukwa choyenera cha kukwiya, kupwetekedwa mtima, kapena cha kulipsira anali mwana wa Yakobo, Yosefe. Abale ake anamchitira mwankhanza kwambiri, analinganiza imfa yake ndipo potsirizira pake anamgulitsa mu ukapolo. Ku Igupto, ngakhale kuti anatumikira Potifara mosamala ndi mokhulupirika, Yosefe anaimbidwa mlandu mosayenera ndi kuikidwa mu ukaidi. Moleza mtima iye anapirira nsautso zake zonse, mwinamwake akumazindikira kuti mayeso otero adzakwaniritsa zifuno za Yehova. (Genesis 45:5) Chifukwa chakuti anakulitsa chikhulupiriro ndi chiyembekezo mwa Yehova limodzi ndi kudzichepetsa ndi kuzindikira, Yosefe anakhoza kusonyeza kuleza mtima ngakhale pa mikhalidwe yovuta kwambiri.

Thandizo lina lofunika ndilo mzimu woyera wa Yehova. Mwachitsanzo, ngati tili ndi mtima wapachala ndi lilime loluma, tingapempherere thandizo la mzimu woyera kotero kuti tikulitse zipatso zake. Kusinkhasinkha chilichonse cha zipatso zimenezi, monga ngati kupirira, ndi chiletso, zidzatithandiza kuona mmene zimagwirizanira kwambiri ndi kuleza mtima.​—Agalatiya 5:22, 23.

Mfupo za Kuleza Mtima

Kukhala woleza mtima kungatibweretsere mapindu ambiri. Kumalimbitsa umunthu wathu ndi kutitetezera pa kuchita zinthu zopusa mwaphuma. Kodi ndani wa ife amene sanapangepo zophophonya zopweteka chifukwa cha kukhala kwathu ochitapo kanthu mwaphuma pa mikhalidwe yovuta ndi yopsinja? Tingakhale titanena mawu ankhanza kwa wina kapena kuchita mwachipongwe. Tingakhale titalola chochitika china chaching’ono kukhala nkhondo yaikulu yosatha ndi wokondedwa wathu wina. Pambuyo pa kukwiya kwakukulu, kugwiritsidwa mwala, ndi kupwetekedwa mtima, mwachisoni tingalingalire kuti, ‘Ndikanangoyembekezera pang’ono pokha.’ Kusonyeza kuleza mtima kungatitetezere pa mitundu yonse ya chisoni. Choonadi chokhachi chimapatsa miyoyo yathu mtendere wochuluka, bata, ndi chikhutiro.​—Afilipi 4:5-7.

Kukhala woleza mtima kungatithandizenso kukhala ndi mtima wabata ndi wachidaliro. Zimenezi zingatichititse kukhala ndi thanzi labwinopo la kuthupi, la malingaliro, ndi lauzimu. (Miyambo 14:30) Ngati sulamuliridwa, mkwiyo waukulu ungachititse munthu kupsinjika mtima, kudwala ndi imfa. Komanso, mwa kukhala woleza mtima tingakhale ndi chithunzi chabwino kwambiri cha ena, makamaka abale athu auzimu ndi ziŵalo za banja lathu. Pamenepo tidzakhala ofunitsitsa kukhala olingalira ena ndi kuwathandiza m’malo mwa kukhala amtima wapachala ndi osuliza. Motero, ena nawonso adzaona kukhala kosavuta ndi kokondweretsa kuyanjana nafe.

Makamaka akulu mumpingo Wachikristu afunikira kusonyeza kuleza mtima. Nthaŵi zina, Akristu anzawo angawafikire ndi mavuto aakulu. Anthu oona mtima ameneŵa angakhale ali ozunguzika, okwiya, kapena opsinjika maganizo, pamene kuli kwakuti akulunso angakhale otopa kapena osokonezedwa ndi mavuto aumwini kapena a banja. Komabe, kuli kofunika chotani nanga kuti akulu asonyeze kuleza mtima m’mikhalidwe yoyesa yoteroyo! Mwanjira imeneyi iwo angalangize “mofatsa” ndi “kuchitira gulu mwachikondi.” (2 Timoteo 2:24, 25; Machitidwe 20:28, 29, NW) Miyoyo ya mtengo wapataliyi ili pachiswe. Akulu okoma mtima, achikondi, ndi oleza mtima ali dalitso labwino chotani nanga ku mpingo!

Mitu ya mabanja iyenera kuchitira mabanja awo moleza mtima, momvetsetsa, ndi mokoma mtima. Ayeneranso kuyembekezera ndi kulimbikitsa ziŵalo zonse za banja kusonyeza mikhalidwe imodzimodziyi. (Mateyu 7:12) Zimenezi zidzachirikiza kwambiri chikondi ndi mtendere m’banja.

Kusonyeza kuleza mtima pamene ali mu utumiki wakumunda kudzathandiza atumiki Achikristu kusangalala ndi utumiki umenewu mokwanira kwambiri. Adzakhala okhoza bwino kwambiri kupirira ndi mphwayi iliyonse ndi chitsutso zimene angakumane nazo. M’malo mwa kutsutsana ndi eni nyumba okwiya, atumiki oleza mtima adzakhoza kuyankha mofatsa kapena kuchoka mwakachetechete, motero akumasunga mtendere ndi chimwemwe. (Mateyu 10:12, 13) Ndiponso, pamene Akristu achitira munthu aliyense moleza mtima ndi mokoma mtima, onga nkhosa adzakopedwa ndi uthenga wa Ufumu. Yehova wadalitsa zoyesayesa za kuleza mtima za padziko lonse, pamene zikwi mazana ambiri za ofuna choonadi akuloŵa mumpingo wachikondi wa Yehova chaka chilichonse.

Zoonadi, kuleza mtima kudzatibweretsera mfupo zabwino kwambiri. Tidzapeŵa ngozi zambiri ndi mavuto ochititsidwa chifukwa cha phuma kapena chifukwa cha kufulumira kulankhula kwathu. Tidzakhala achimwemwepo, amtenderepo, ndipo mwinamwake athanzipo. Tidzakhala ndi chisangalalo chokulira ndi mtendere mu utumiki wathu, mumpingo, ndi panyumba. Koma choposa zonsezo, tidzakhala ndi unansi wapafupi kwambiri ndi Mulungu. Chotero yembekezerani pa Yehova. Lezani mtima!

[Mawu a M’munsi]

a Dzina lasinthidwa.

[Zithunzi patsamba 10]

Kodi ndinu woleza mtima motani m’moyo wa tsiku ndi tsiku?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena