Nyimbo 135
Yehova, Malo Athu Okhalamo
1. Ya malo athu okhalamo
Mumibadwo yathu yonse.
Musanapangetu mapiri,
Inu munalipo kale.
Ndinu M’lungu wanthaŵi zonse;
Kuzaka zosatha konse.
Chinkana tiri ngati ‘fumbi,’
Munatikonda kwambiri.
2. Zaka chikwi kwa inu ziri
Ngati dzulo lapitali.
Munthu afanana ndi msipu
Aphukira ndi kufota.
Tikhala makumi asanu
N’aŵiri pena atatu;
Koma zaka zathu nzovuta,
Zodzazidwa ndi chisoni.
3. Mutiphunzitse kuŵerenga
Masiku tisangalale.
Mitima ikhale ndi nzeru,
Milomo itamandenu.
Yehova khalani wokondwa
Po’na atumiki anu.
Limbikitsani ntchito yathu;
Manja athu mulimbitse.