Nyimbo 169
Nyimbo Yatsopano
1. Imba kwa Mbuye nyimbo yachikondwelero;
Ya zinthu wachita ndi za kudzachita.
Tama mkonowo, ndi dzanja lake lamanja;
Waweruza anthu onse molungama.
(Korasi)
2. Fu’la mokondwa kwa Yehova dziko lonse;
Imbani kwa M’lungu zitamando zanu.
Tama Yehova, imbani pamaso pake,
Zoimbira zonse zigwirizanedi.
(Korasi)
3. Nyanja yamphamvu zonse za m’mwemo zibume,
Okhala padziko aimbe mokondwa.
Madzi akondwe mitsinje isangalale,
Mitunda nayonso iimbe ponsepo.
(KORASI)
Imbani!
Nyimbo Yatsopano.
Imbani!
Yehova ndi Mfumu.