Pemphererani Thandizo la Yehova
1 Yesu anagogomezera ophunzira ake kufunika kwa madalitso a Yehova pa utumiki wawo. (Mat. 9:37, 38) Mapemphero athu ochokera pansi pa mtima a chitamando ndi chiyamiko pamodzi ndi kupempha moonadi ndi mapembedzero, amasonyeza kudalira kwathu konse Yehova kaamba ka thandizo lake. (Afil. 4:6, 7) Malemba amatilimbikitsa kupitirizabe kupemphera “pemphero lonse ndi pembedzero,” ndipo izi zingagwire ntchito pa mapemphero athu okhudza utumiki.—Aef. 6:18.
2 Timatamanda Yehova m’pemphero chifukwa cha mikhalidwe yake yapadera ndi zochita zake. Timamutamandanso monga Wotipatsa uthenga wabwino umene timalalika. N’gwoyenera kumutamanda chifukwa iye yekha ndi amene amapangitsa utumiki wathu kukhala wachipambano.—Sal. 127:1.
3 Mapemphero athu a chiyamiko amasonyeza kuyamikira kwathu chidziŵitso chimene Yehova watipatsa ponena za chifuno ndi cholinga chake. Kodi si mwayi kugaŵana choonadi cha Ufumu ndi ena? Timathokoza Yehova kaamba ka zonse zimene timachita mu utumiki.—Sal. 107:8; Aef. 5:20.
4 Moyenerera, timapempha thandizo kwa Yehova kuti tipeze anthu amene angavomere pempho lathu la phunziro la Baibulo ndi kuti tikhudze mitima yawo ndi choonadi. Mwa kupereka mapemphero amenewa, timatsimikiza kuti Mulungu yekha ndiye angapangitse ntchito yathu ya utumiki kukhala yobala zipatso.—1 Akor. 3:5-7.
5 Mlongo wina ankadzimva kuti mayi wina panjira yake ya magazini sanali kuŵerenga Nsanja za Olonda ndi Galamukani! Posafuna kuti magazini ofunikawa azingowonongeka, anapempha Yehova kuti ngati mayi ameneyu sanali kuwaŵerenga, asamawalandire. Mlongoyu atapitako nthaŵi ina, mwamuna wa mayiyu anati: “Zikomo kwambiri pomatibweretsera magazini amenewa nthaŵi zonse. Ndimawaŵerenga ndipo ndimawakonda kwambiri.”
6 Modzichepetsa komanso ndi mtima wonse, tingam’pemphe Yehova kuti atithandize mmene tingachitire ndi anthu amphwayi ndi onyoza komanso mmene tingagonjetsere kuopa anthu kuti tipitirizebe kuchitira umboni kwa ena molimba mtima. (Mac. 4:31) Ngati tipitirizabe kupemphera “pemphero lonse ndi pembedzero” pamene tikuchitabe utumiki wathu wopatulika mokhulupirika, tingakhale ndi chidaliro chakuti Yehova atithandiza.—1 Yoh. 3:22.