Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Yehova Anayankha Mapemphero Anga!”
    Nsanja ya Olonda—1996 | October 15
    • “Yehova Anayankha Mapemphero Anga!”

      PADZIKO lonse, Mboni za Yehova zikuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba pafupifupi mamiliyoni asanu ndi anthu amene akufuna kupeza chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu ndi chifuno chake chabwino kwambiri kaamba ka anthu. Ngakhale ana pakati pa Mboni za Yehova akukhala ndi phande mu ntchitoyi. Mwachitsanzo, lingalirani za mnyamata wina wotchedwa Joel. Iye anasonyeza kudzipatulira kwake kwa Yehova ndipo anabatizidwa pausinkhu wa zaka zisanu ndi zinayi. Patapita chaka anali ndi chokumana nacho ichi:

      “Pamene ndinali mu utumiki, ndinakumana ndi mkazi wina wotchedwa Candy. Ndinamsonyeza brosha lakuti ‘Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.’ Iyeyo anali nalo kale, chotero ndinamsonyeza buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Limenelonso anali nalo kale. Ndiyeno ndinaganiza kuti, ‘Ndimpempha mkaziyu kuphunzira naye Baibulo.’ Anavomera!

      “Mchemwali wa Candy, amene anali kudwala kwambiri kansa, anabwera kudzakhala naye. Ndiponso, Candy anali kuphunzira unesi. Chotero kwa nyengo ina, phunziro la Baibulolo linaimitsidwa. Koma ine ndi makolo anga tinapitiriza kumfikira tikumasiya magazini kwa iyeyo kapena kwa mwamuna wake, Dick. Anatiuza kuti anali kuika magaziniwo pambali pa mbedi wake ndipo ankawaŵerenga usiku.

      “Potsirizira pake, mchemwali wa Candy anamwalira. Ine ndi Atate ndi Amayi tinakambitsirana ndi Candy za mkhalidwe wa akufa. Anasankha zopitiriza phunziro lake la Baibulo. Tsiku lina, tinafunsa Dick ngati akanakonda kuphunzira limodzi ndi Candy ndi kuchititsa phunzirolo kukhala la banja. Iyeyo anaganiza kuti limenelo linali lingaliro labwino. Chotero tsopano, ine limodzi ndi Atate, ndikuphunzira ndi Dick ndi Candy yemwe. Iwo akupita patsogolo bwino kwambiri ndipo amayamikira kwambiri phunziro la Baibulo.

      “Ndinali kupemphera kuti ndikhale ndi phunziro la Baibulo, ndipo Yehova anayankha mapemphero anga!”

  • Kodi Mungakonde Kuchezeredwa?
    Nsanja ya Olonda—1996 | October 15
    • Kodi Mungakonde Kuchezeredwa?

      Ngakhale m’dziko lino lodzala ndi mavuto, mungakhoze kupeza chimwemwe kuchokera m’chidziŵitso cholongosoka Chabaibulo chonena za Mulungu, Ufumu wake, ndi chifuno chake chabwino kwambiri kwa anthu. Ngati mungafune chidziŵitso chowonjezereka kapena ngati mungakonde kuti wina adze kudzachita nanu phunziro Labaibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera pandandanda ya patsamba 2.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena