Nyimbo 175
Miyamba Imalengeza Ulemelero wa Mulungu
1. Miyamba ilengeza za Yehova;
Tiziwona ntchito zake mlengalenga.
Usana umtamandadi;
Usiku usonyezatu mphamvu yake.
2. Lamulo la Yehova ndi langwiro,
Malangizo ake achititsa nzeru.
Ndipo malamulo ake;
Asangalatsa mtima ndi maso athu.
3. Kuwopa Yehova kuli kwanzeru.
Ziweruzo zake ziri zolungama
Ndi zofunika kwambiri,
Zosangalatsa pakudya, ngati uchi.
4. Tiyamika ka’mba ka malamulo;
Tidzapeza mphotho ngati tiwasunga.
Mumaganizo ndi mawu
Zipezedwe zowonadi, ’mbuye Mfumu.