Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Makolo, Kodi Chitsanzo Chanu Chimaphunzitsa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—1999 | July 1
    • Makolo, Kodi Chitsanzo Chanu Chimaphunzitsa Chiyani?

      “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; ndipo yendani m’chikondi.”​—AEFESO 5:1, 2.

      1. Kodi Yehova anapereka malangizo otani ku banja loyambirira?

      YEHOVA ndiye Woyambitsa makonzedwe a banja. Banja lililonse lilipo chifukwa cha iye popeza kuti iye ndiye amene anakhazikitsa banja loyambirira napatsa anthu aŵiri oyambawo mphamvu za kubala. (Aefeso 3:14, 15) Anapatsa Adamu ndi Hava malangizo ofunika pa ntchito yawo ndiponso anawapatsa mpata wokwanira woti iwo aone wokha mmene angamachitire ntchitoyo. (Genesis 1:28-30; 2:15-22) Adamu ndi Hava atachimwa, mikhalidwe imene mabanja anafunika kulimbana nayo inakhala yovuta kwambiri. Komabe, mwachikondi Yehova anapereka zitsogozo zimene zikathandiza atumiki ake kulimbana ndi mikhalidwe imeneyo.

      2. (a)  Ndi m’njira ziti zimene Yehova wachirikizira malangizo olembedwa ndi apakamwa? (b) Kodi makolo afunika kudzifunsa funso lotani?

      2 Monga Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova wachita zinthu zambiri kuposa kungopereka malangizo olembedwa onena za zimene tiyenera kuchita ndi zimene tiyenera kupeŵa. M’nthaŵi zakale ankaphatikiza malangizo olembedwa ndi apakamwa kudzera mwa ansembe ndi aneneri ndiponso mitu ya mabanja. Kodi iye akugwiritsa ntchito ndani kupereka malango apakamwa amenewo m’masiku athu ano? Akulu achikristu ndiponso makolo. Ngati ndinu kholo, kodi mukuchita mbali yanu kuti mulangize banja lanu m’njira za Yehova?​—Miyambo 6:20-23.

      3. Kodi mitu ya mabanja ingaphunzire chiyani kwa Yehova ponena za kuphunzitsa kogwira mtima?

      3 Kodi malangizo otero ayenera kuperekedwa motani m’banja? Yehova akutipatsa chitsanzo. Iye amanena momveka bwino chimene chili chabwino ndi chimene chili choipa, ndipo mokoma mtima amabwerezabwereza. (Eksodo 20:4, 5; Deuteronomo 4:23, 24; 5:8, 9; 6:14, 15; Yoswa 24:19, 20) Amagwiritsa ntchito mafunso opangitsa kuganiza. (Yobu 38:4, 8, 31) Mwa mafanizo ndi zitsanzo za zochitika zenizeni m’moyo, amasonkhezera malingaliro athu ndi kuumba mitima yathu. (Genesis 15:5; Danieli 3:1-29) Makolo, pamene mukuphunzitsa ana anu, kodi mumayesa kutsatira chitsanzo chimenechi?

      4. Kodi timaphunziranji kwa Yehova ponena za kupereka chilango, ndipo kodi n’chifukwa chiyani chilango chili chofunika?

      4 Yehova amamamatira pa chimene chili cholondola, komanso amamvetsa bwino zotsatira za kupanda ungwiro. Motero asanapereke chilango, iye amaphunzitsa ndipo amachenjeza ndi kukumbutsa anthu opanda ungwiro mobwerezabwereza. (Genesis 19:15, 16; Yeremiya 7:23-26) Popereka chilango, amalanga moyenera, salanga mopitirira muyeso. (Salmo 103:10, 11; Yesaya 28:26-29) Ngati mmenemu ndi mmene timachitira ndi ana athu, zimapereka umboni wakuti Yehova timamudziŵa, ndipo kudzakhala kosavuta kwa iwonso kuti amudziŵe.​—Yeremiya 22:16; 1 Yohane 4:8.

      5. Kodi makolo angaphunzirenji kwa Yehova pankhani ya kumvetsera?

      5 Modabwitsa kwambiri, Yehova amamvetsera monga Atate wachikondi wa kumwamba. Iye sangopereka malamulo. Amatilimbikitsa kuti tizimukhuthulira zamumtima mwathu. (Salmo 62:8) Ndipo ngati malingaliro amene timamuuza sali olondola kwenikweni, satidzudzula ndi mawu ozaza kuchokera kumwamba. Iye amatiphunzitsa moleza mtima. Motero, uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: “Khalani akutsanza a Mulungu,” ulidi woyenerera kwambiri! (Aefeso 4:31–5:1) Yehova amaperekadi chitsanzo chabwino kwambiri kwa makolo pamene akuyesa kulangiza ana awo! Chili chitsanzo chimene chimatifika pamtima ndi kutipangitsa kufuna kuyenda m’njira yake ya moyo.

      Zimene Chitsanzo Chimachita

      6. Kodi kaonedwe ka zinthu ndi chitsanzo cha makolo zimasonkhezera ana awo motani?

      6 Kuwonjezera pa malango apakamwa, ana amasonkhezeredwa kwambiri ndi chitsanzo. Kaya makolo akufuna kapena sakufuna, ana awo adzatengera iwo basi. Zingawasangalatse makolo​—nthaŵi zina zingawadabwitse​—pamene amva ana awo akunena zinthu zimene iwowo ananena. Pamene khalidwe ndi kaonedwe ka zinthu ka makolo kasonyeza kuyamikira kwambiri zinthu zauzimu, zimenezi zimasonkhezera ana kuchita zinthu bwino.​—Miyambo 20:7.

      7. Kodi Yefita monga kholo anaonetsa chitsanzo chotani kwa mwana wake wamkazi, ndipo panali zotsatira zotani?

      7 Zimene chitsanzo cha makolo chimachita zikusonyezedwa bwino m’Baibulo. Yefita, amene Yehova anamugwiritsa ntchito kutsogolera Aisrayeli kuti apambane polimbana ndi a Amoni, analinso kholo. Nkhani yonena za yankho lake kwa mfumu ya a Amoni imasonyeza kuti Yefita anali kuŵerenga kaŵirikaŵiri mbiri ya zochita za Yehova ndi Aisrayeli. Iye anatchula bwino lomwe zochitika za m’mbiri imeneyo, ndipo anasonyeza chikhulupiriro cholimba mwa Yehova. Mosakayikira, chitsanzo chake chinathandiza mwana wake wamkazi kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso mzimu wodzimana umene anaonetsa mwa kukhala mu utumiki wodzipereka kwa Yehova kwa moyo wake wonse ali wosakwatiwa.​—Oweruza 11:14-27, 34-40; yerekezerani ndi Yoswa 1:8.

      8. (a) Kodi ndi malingaliro abwino otani amene makolo ake a Samueli anasonyeza? (b) Kodi zimenezo zinamupindulitsa motani Samueli?

      8 Samueli anali mwana wa chitsanzo chabwino ndiponso anali mneneri wokhulupirika kwa Mulungu pa moyo wake wonse. Kodi mukufuna kuti ana anu adzakhale monga mmene iye analili? Lingalirani chitsanzo chimene makolo ake a Samueli, Elikana ndi Hana, anapereka. Ngakhale kuti zinthu m’nyumba mwawo sizinali bwino, iwo nthaŵi zonse anali kupita ku Silo kukalambira, kumalo amene chihema chopatulika chinalili. (1 Samueli 1:3-8, 21) Taonani malingaliro akuya amene Hana anali nawo pamene anali kupemphera. (1 Samueli 1:9-13) Onani mmene onse aŵiri anaonera kufunika kwa kukwaniritsa chilichonse chimene analonjeza kwa Mulungu. (1 Samueli 1:22-28) Mosakayikira chitsanzo chawo chabwino chinathandiza Samueli kukhala ndi mikhalidwe imene inamuthandiza kulondola njira yoyenera​—ngakhale pamene anthu amene anali kukhala nawo amene ankaoneka kuti anali kutumikira Yehova sanasonyeze ulemu uliwonse ku njira za Mulungu. M’kupita kwa nthaŵi, Yehova anapatsa Samueli udindo wokhala mneneri Wake.​—1 Samueli 2:11, 12; 3:1-21.

      9. (a) Ndi zochitika za panyumba zotani zimene zinamusonkhezera Timoteo? (b) Kodi Timoteo anadzakhala munthu wotani?

      9 Kodi mukufuna kuti mwana wanu adzakhale ngati Timoteo, amene pamene anali mnyamata anakhala mnzake wa mtumwi Paulo wogwira naye ntchito? Abambo ake a Timoteo anali wosakhulupirira, koma amayi ake ndi agogo ake anapereka chitsanzo chabwino cha kuyamikira zinthu zauzimu. Mosakayikira zimenezi zinathandiza kuyala maziko abwino a moyo wa Timoteo monga Mkristu. Timauzidwa kuti amayi ake, a Yunike, ndi agogo ake a Loisi anali ndi “chikhulupiriro chosanyenga.” Moyo wawo monga Akristu sunali wachinyengo; anakhaladi mogwirizana ndi zimene ankati anali kukhulupirira, ndipo anamuphunzitsanso mwanayo Timoteo kuchita chimodzimodzi. Timoteo anasonyeza kuti anali munthu wodalirika ndi kuti analidi kusamala za ubwino wa ena.​—2 Timoteo 1:5; Afilipi 2:20-22.

      10. (a) Kodi ndi zitsanzo zotani zimene sizili za panyumba zimene zingakhudze ana athu? (b) Kodi tiyenera kuchitanji pamene zinthu zimenezi zionekera m’kalankhulidwe ndi zochita za ana athu?

      10 Zitsanzo zimene zimakhudza ana athu si zapanyumba zokha. Pali ana ena amene amakhala nawo kusukulu, aphunzitsi amene ntchito yawo ndi kuumba maganizo athete, anthu amene amakhulupirira zolimba kuti aliyense ayenera kuchita mogwirizana ndi miyambo yachikhalire ya mtunduwo kapena ya m’deralo, anthu otchuka a zamaseŵera amene zochita zawo zimatamandidwa ponseponse, ndi akuluakulu aboma amene khalidwe lawo limasimbidwa m’nkhani. Ana ena miyandamiyanda aonaponso nkhanza za nkhondo. Kodi tiyenera kudabwa ngati zinthu zimenezi zionekera m’kalankhulidwe kapena zochita za ana athu? Kodi timachita motani iwo akatero? Kodi kudzudzula kapena kulangiza mwaukali kungathetse vutolo? M’malo mokamba ndi ana athu mwamsanga, kodi sikungakhale bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi pali chilichonse m’njira imene Yehova amachitira nafe zinthu chimene chingathandize kuzindikira mmene ndingachitire ndi mkhalidwewu?’​—Yerekezerani ndi Aroma 2:4.

      11. Pamene makolo achita zolakwa, kodi zimenezi zingakhudze motani khalidwe la ana awo?

      11 Zoonadi, makolo opanda ungwiro sadzachita zinthu m’njira yabwino kwambiri nthaŵi zonse. Iwo adzakhala ndi zolakwitsa ndithu. Pamene ana azindikira zimenezi, kodi zidzawachititsa kusapereka ulemu kwa makolo awo? Zingatero, makamaka ngati makolo amayesa kupeputsa zolakwa zawo mwa kusonyeza ulamuliro wawo mwaukali. Koma pangachitike zosiyana kwambiri ngati makolo ali odzichepetsa ndiponso ngati avomereza zolakwa zawo mosavuta. Mwakutero, iwo angapereke chitsanzo chabwino kwambiri kwa ana awo, amene afunika kuphunzira kuchita zofananazo.​—Yakobo 4:6.

      Zimene Chitsanzo Chathu Chingaphunzitse

      12, 13. (a) Kodi ana ayenera kuphunziranji pankhani ya chikondi, ndipo kodi ndi motani mmene zimenezi zingaphunzitsidwire bwino kwambiri? (b) Kodi ndi chifukwa chiyani kuli kofunika kuti ana aphunzire za chikondi?

      12 Pali maphunziro amtengo wapatali ambirimbiri amene angaphunzitsidwe bwino kwambiri pamene malango apakamwa aphatikizidwa ndi chitsanzo chabwino. Talingaliraniko ochepa.

      13 Kusonyeza chikondi chopanda dyera: Phunziro limodzi mwa maphunziro ofunika kwambiri oyenera kuchirikizidwa ndi chitsanzo ndilo tanthauzo la chikondi. “Tikonda ife, chifukwa anayamba [Mulungu] kutikonda.” (1 Yohane 4:19) Iye ndiye Gwero ndi chitsanzo chapamwamba kwambiri cha chikondi. Chikondi cha lamulo chimenechi, a·gaʹpe, chikutchulidwa m’Baibulo nthaŵi zoposa 100. Ndiwo mkhalidwe umene umadziŵikitsa Akristu oona. (Yohane 13:35) Chikondi choterechi chifunika kusonyezedwa kwa Mulungu ndi Yesu Kristu ndiponso ndi anthu kwa wina ndi mnzake​—ngakhalenso kwa anthu amene satisangalatsa. (Mateyu 5:44, 45; 1 Yohane 5:3) Chikondi chimenechi poyamba chiyenera kukhala m’mitima mwathu ndi kumaoneka m’miyoyo yathu kuti tichiphunzitse mogwira mtima kwa ana athu. Zochita zimanena zambiri kusiyana ndi mawu. M’banja ana ayenera kuona chikondi ndi mikhalidwe ina yofanana nacho, monga kuyanjana, komanso ayenera kumamva kuti amakondedwa. Popanda zinthu zimenezi, mwana amakwinimbira m’kakulidwe kake kakuthupi, kamaganizo, ndi kamalingaliro. Ana ayeneranso kuona mmene chikondi ndi kuyanjana zimasonyezedwera bwino kwa Akristu anzawo amene sali a m’banjamo.​—Aroma 12:10; 1 Petro 3:8.

      14. (a) Kodi ana angaphunzitsidwe motani kugwira bwino ntchito yokhutiritsa? (b) Kodi zimenezi zingachitidwe motani m’mikhalidwe ya banja lanu?

      14 Kuphunzira kugwira ntchito: Ntchito ndi mbali yofunika kwambiri ya moyo. Kuti munthu azidzimva kuti ndi wofunika, iye ayenera kuphunzira kugwira bwino ntchito. (Mlaliki 2:24; 2 Atesalonika 3:10) Ngati mwana apatsidwa ntchito zimene analangizidwa pang’ono chabe mmene angazigwirire ndiyeno kenaka ndi kukalipidwa chifukwa chosazigwira bwino, ndi zokayikitsa kuti adzaphunzira kugwira bwino ntchito. Koma pamene ana aphunzira mwa kugwira ntchito pamodzi ndi makolo awo ndiponso ndi kumawayamikira moyenerera, iwo angathedi kuphunzira mmene angamagwirire ntchito yokhutiritsa. Pamene chitsanzo cha makolo chiphatikizapo kulongosola mmene zikuchitikira, ana angaphunzire osati kokha kugwira ntchito komanso kugonjetsa mavuto, kulimbikira kugwira ntchito mpaka itatha, ndiponso kuganiza ndi kusankha zochita. M’kuchita kotereku iwo angathandizidwe kuzindikira kuti Yehovanso amagwira ntchito, kuti iye amagwira bwino ntchito, ndi kuti Yesu amatsanzira Atate ake. (Genesis 1:31; Miyambo 8:27-31; Yohane 5:17) Ngati ndinu alimi pabanja lanu kapena ngati mumagulitsa malonda, ena a m’banja lanu angamagwirire ntchito pamodzi. Kapena mwina amayi angaphunzitse mwana wawo wamwamuna kapena wamkazi kuphika ndi kutsuka ziwiya mukatha kudya. Atate amene amagwirira ntchito kutali ndi nyumba yawo angakonze kugwira ntchito za pakhomopo pamodzi ndi ana awo. Zilidi zothandiza kwambiri pamene makolo akumbukira kuti sangofunika kuonetsetsa kuti ntchito za mwamsanga zili kugwiridwa komanso kuti akukonzekeretsa ana za moyo wawo!

      15. Kodi maphunziro okhudza chikhulupiriro angaperekedwe motani? Perekani chitsanzo.

      15 Kukhalabe ndi chikhulupiriro pokumana ndi mavuto: Chikhulupiriro chilinso mbali yofunika kwambiri ya moyo wathu. Pamene mukambirana za chikhulupiriro pa phunziro labanja, ana angaphunzire kuchifotokoza. Iwo angazindikirenso umboni umene umapangitsa chikhulupiriro kuyamba kukula m’mitima yawo. Koma pamene aona makolo awo akusonyeza chikhulupiriro chosagwedera pokumana ndi mayesero aakulu, zotsatira zake zingakhale kwa moyo wonse. Wophunzira Baibulo wina ku Panama anaopsezedwa ndi mwamuna wake kuti adzamuthamangitsa panyumba ngati sasiya kutumikira Yehova. Komabe, ndi ana ake ang’ono anayi, iye nthaŵi zonse anali kuyenda pansi ulendo wa makilomita 16 ndiyeno ndi kukwera basi n’kuyenda makilomita 30 kuti akafike pa Nyumba ya Ufumu yapafupi ndi kwawo. Polimbikitsidwa ndi chitsanzo chimenecho, achibale ake ena okwana ngati 20 atsatira njira ya choonadi.

      Kupereka Chitsanzo pa Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku

      16. Kodi ndi chifukwa chiyani kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kuli koyenera?

      16 Chimodzi mwa zizoloŵezi zabwino koposa zimene banja lililonse lingapange​—chizoloŵezi chimene chidzapindulitsa makolo ndi kukhala chitsanzo chakuti ana atsanzire​—ndicho kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse. Ngati kuli kotheka, ŵerengani Baibulo tsiku lililonse. Si kuchuluka kwa zimene mwaŵerenga kumene kuli kofunika kwambiri. Chimene chili chofunika kwambiri ndi chakuti kodi mumaŵerenga kaŵirikaŵiri motani ndiponso m’njira yotani. Kwa ana, mungawonjezere pa kuŵerenga Baibulo kumvetsera makaseti a Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ngati alipo m’chinenero chanu. Kuŵerenga m’Mawu a Mulungu tsiku lililonse kumatithandiza kuika patsogolo malingaliro a Mulungu. Ndipo ngati kuŵerenga Baibulo koteroko kuchitidwa osati kokha ndi anthu ena chabe koma ndi mabanja, izi zingathandize mabanja athunthu kuyenda m’njira za Yehova. Ndi m’khalidwe umenewu umene seŵero lakuti Mabanja​—Pangani Kuŵerenga Baibulo kwa Tsiku ndi Tsiku Kukhala Chizoloŵezi Chanu! linalimbikitsa pa Misonkhano Yachigawo yaposachedwapa ya “Njira ya Moyo ya Mulungu.”​—Salmo 1:1-3.

      17. Kodi kuŵerenga Baibulo kwa banja ndi kuloweza malemba akuluakulu kumathandiza motani kugwiritsa ntchito uphungu wopezeka pa Aefeso 6:4?

      17 Kuŵerenga Baibulo monga banja kukugwirizana ndi zimene mtumwi Paulo analemba m’kalata yake youziridwa yopita kwa Akristu a ku Efeso, kuti: “Atate . . . musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Kodi zimenezi zikutanthauzanji? Kwenikweni “chilangizo” chimatanthauza “kuikapo maganizo”; motero atate achikristu akulimbikitsidwa kuika maganizo a Yehova Mulungu mwa ana awo​—kuthandiza ana kudziŵa malingaliro a Mulungu. Kulimbikitsa ana kuloweza malemba akuluakulu kungathandize kukwaniritsa zimenezi. Cholinga ndi chakuti malingaliro a Yehova azitsogolera maganizo a ana kotero kuti zikhumbo zawo ndi zochita zawo mwapang’onopang’ono zidzafika posonyeza miyezo ya Mulungu kaya akhale ndi makolo awo kapena ayi. Baibulo ndilo maziko a maganizo ameneŵa.​—Deuteronomo 6:6, 7.

      18. Poŵerenga Baibulo, kodi ndi chiyani chimene chingafunike kuti (a) mulimvetse bwinobwino? (b) mupindule ndi uphungu umene lili nalo? (c) muchite mogwirizana ndi zimene limavumbula ponena za chifuno cha Yehova? (d) mupindule ndi zimene limanena pa maganizo ndi zochita za anthu?

      18 Zoonadi, ngati Baibulo liti likhudze miyoyo yathu, tifunika kumvetsa zimene limanena. Kwa anthu ambiri, izi zingafune kuti aŵerenge mbali zina maulendo angapo. Kuti timvetsetsedi mawu ena, tingafunike kuyang’ana matanthauzo a mawuwo mu dikishonale kapena mu Insight on the Scriptures. Ngati lemba lili ndi uphungu kapena lamulo, khalani ndi nthaŵi yokwanira yokamba za mikhalidwe m’masiku athu ano imene imapangitsa lembalo kukhala loyenerera. Ndiyeno mungafunse kuti, ‘Kodi kugwiritsa ntchito uphungu umenewu kungatithandize bwanji?’ (Yesaya 48:17, 18) Ngati lembalo likunena za mbali ina ya chifuno cha Yehova, funsani kuti, ‘Kodi zimenezi zikukhudza bwanji moyo wathu?’ Mwina mukuŵerenga nkhani imene ikunena za khalidwe la anthu ndi zochita zawo. Kodi pamoyo wawo iwo anali kukumana ndi mavuto otani? Kodi iwo anachita nawo motani mavutowo? Kodi tingapindule motani ndi chitsanzo chawo? Nthaŵi zonse khalani ndi nthaŵi yokwanira yokambirana kufunika kwa nkhaniyo m’moyo wathu lerolino.​—Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:11.

      19. Mwa kukhala otsanza a Mulungu, kodi tidzakhala tikupereka chiyani kwa ana athu?

      19 Ndi njiratu yabwino kwambiri yochititsira malingaliro a Mulungu kukhazikika m’maganizo ndi m’mitima yathu! Motero tidzathandizidwadi kukhala “akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Ndipo tidzapereka chitsanzo chimene chidzakhaladi chofunika kuti ana athu atsanzire.

      Kodi Mukukumbukira?

      ◻ Kodi makolo angapindule motani ndi chitsanzo cha Yehova?

      ◻ Kodi ndi chifukwa chiyani kupereka malango apakamwa kwa ana kuyenera kuphatikizidwa ndi chitsanzo chabwino cha makolo?

      ◻ Kodi ndi maphunziro ena ati amene amaphunzitsidwa bwino kwambiri ndi chitsanzo cha makolo?

      ◻ Kodi ndi motani mmene tingapindulire mokwanira ndi kuŵerenga Baibulo kwa banja?

  • Phunzirani Mawu A Mulungu Mokhazikika Monga Banja
    Nsanja ya Olonda—1999 | July 1
    • Phunzirani Mawu A Mulungu Mokhazikika Monga Banja

      “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.”​—MATEYU 4:4.

      1. Kodi Baibulo limanenanji za udindo wa mitu ya mabanja wophunzitsa ana awo njira za Yehova?

      YEHOVA MULUNGU nthaŵi ndi nthaŵi anali kukumbutsa mitu ya mabanja za udindo wawo wophunzitsa ana awo. Malangizo oterowo ankakonzekeretsa anawo mmene anayenera kukhalira ndi moyo panthaŵiyo ndiponso ankawathandiza kukonzekera za moyo wa m’tsogolo. Mngelo amene anali kuimira Mulungu anafotokozera Abrahamu udindo wake wophunzitsa banja lake kotero kuti iwo “asunge njira ya Yehova.” (Genesis 18:19) Makolo achiisrayeli anauzidwa kuti azifotokozera ana awo mmene Mulungu anawalanditsira mu Igupto ndiponso mmene anawapatsira Chilamulo pa Phiri la Sinai, mu Horebe. (Eksodo 13:8, 9; Deuteronomo 4:9, 10; 11:18-21) Mitu ya mabanja yachikristu ikulimbikitsidwa kulera ana awo “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Ngakhale kuli kwakuti kholo limodzi lokha n’limene limatumikira Yehova, kholo limenelo liyenera kuyesetsa kuphunzitsa anawo njira za Yehova.​—2 Timoteo 1:5; 3:14, 15.

      2. Kodi phunziro labanja ndi lofunika ngati m’banjamo mulibe ana? Longosolani.

      2 Izi sizitanthauza kuti mabanja amene ali ndi ana okha ndiwo ayenera kuphunzira Mawu a Mulungu. Pamene mwamuna ndi mkazi akhala ndi phunziro labanja ngakhale iwo alibe ana m’banjamo, zimasonyeza kuti amayamikira kwambiri zinthu zauzimu.​—Aefeso 5:25, 26.

      3. Kodi n’chifukwa chiyani kuchita phunziro labanja nthaŵi zonse kuli kofunika?

      3 Kuti papezeke mapindu ochuluka, malangizo ayenera kuperekedwa nthaŵi ndi nthaŵi, mogwirizana ndi phunziro limene Yehova anaphunzitsa Aisrayeli m’chipululu lakuti: “Munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka mkamwa mwa Yehova.” (Deuteronomo 8:3) Malinga ndi mikhalidwe ya banjalo, mabanja ena angakonze zomaphunzira mlungu uliwonse; ena angamakhale ndi nthaŵi pang’ono tsiku lililonse yoti aphunzire. Zilizonse zimene mungasankhe kuchita, musangosiya kuti phunzirolo lizichitika mwangozi. ‘Wombolani nthaŵi’ yochita phunziro. Mtengo umene mumalipira pa nthaŵi yotereyi ndi njira yanzeru yosungira chuma. Miyoyo ya anthu a m’banja lanu ili pachiswe.​—Aefeso 5:15-17, NW; Afilipi 3:16.

      Zolinga Zofunika Kuzikumbukira

      4, 5. (a) Kupyolera mwa Mose, kodi Yehova anauza makolo chiyani kukhala cholinga chofunika pophunzitsa ana awo? (b) Kodi zimenezi lerolino zikuphatikizapo chiyani?

      4 Pamene muchititsa phunziro labanja, lidzakhala lopindulitsa kwambiri ngati muli ndi zolinga zenizeni. Talingalirakoni zochepa izi.

      5 Paphunziro lililonse, yesetsani kukulitsa chikondi pa Yehova Mulungu. Pamene Aisrayeli anasonkhana m’zigwa za Moabu, asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawachititsa kulingalira za chimene Yesu Kristu kenako anadzatcha kuti “lamulo lalikulu . . . la m’chilamulo.” Kodi linali chiyani? “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.” (Mateyu 22:36, 37; Deuteronomo 6:5) Mose analimbikitsa Aisrayeli kuika zimenezi m’mitima mwawo ndi kuphunzitsa ana awo. Zimenezi zinafuna kubwereza, kupeza zifukwa zokondera Yehova, kuthetsa malingaliro ndi makhalidwe amene angapinge kusonyeza chikondi chimenecho, ndiponso kumaonetsa kuti amakonda Yehova m’miyoyo yawo. Kodi ana athunso amafunika malangizo ofananawo? Inde! Ndipo iwonso afunika kuthandizidwa ‘kudula mitima yawo,’ ndiko kuti, kuchotsa chilichonse chimene chingajejemetse chikondi chawo kwa Mulungu. (Deuteronomo 10:12, 16; Yeremiya 4:4) Mwa zinthu zojejemetsa zimenezo pangakhale chilakolako cha zinthu za dziko lapansi ndi kufuna mipata yoloŵerera mu zochita zake. (1 Yohane 2:15, 16) Chikondi chathu pa Yehova chiyenera kukhala chosonyeza ntchito, choonekeratu, chotisonkhezera kuchita zinthu zokondweretsa Atate wathu wakumwamba. (1 Yohane 5:3) Kuti phunziro lathu labanja likhale ndi mapindu okhalitsa, phunziro lililonse liyenera kuchititsidwa m’njira imene idzalimbitsa chikondi chimenechi.

      6. (a) Kodi chofunika ndi chiyani kuti tipereke chidziŵitso cholongosoka? (b) Kodi Malemba amagogomezera motani kufunika kwa chidziŵitso cholongosoka?

      6 Perekani chidziŵitso cholongosoka cha zimene Mulungu amafuna. Kodi zimenezi zimaphatikizaponji? Zimaphatikizapo zambiri zoposa kungodziŵa chabe kuŵerenga yankho m’magazini kapena m’buku. Kaŵirikaŵiri zimafuna kukambirana kuti mutsimikize kuti mawu ofunika ndi mfundo zikuluzikulu zamvetsetsedwa bwino. Chidziŵitso cholongosoka ndi mbali yofunika kwambiri povala umunthu watsopano, pokumbukira zinthu zofunikadi kwambiri pamene tikulimbana ndi mavuto m’moyo, ndiponso, pochita zimene zimakondweretsadi Mulungu.​—Afilipi 1:9-11; Akolose 1:9, 10; 3:10.

      7. (a) Kodi ndi kugwiritsa ntchito mafunso ati kumene kungathandize banja kugwiritsa ntchito nkhani imene laphunzira? (b) Kodi Malemba amagogomezera motani phindu la cholinga chimenechi?

      7 Athandizeni kugwiritsa ntchito zimene akuphunzira. Ndi cholinga chimenechi m’maganizo, paphunziro lililonse labanja, funsani kuti: ‘Kodi nkhani imeneyi iyenera kukhudza miyoyo yathu motani? Kodi pakufunika kuti tisinthe zimene tikuchita tsopano? Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kufuna kusintha?’ (Miyambo 2:10-15; 9:10; Yesaya 48:17, 18) Kulingalira mokwanira mmene tingagwiritsire ntchito zinthu zimene tikuphunzira kungakhale mbali yofunika kwambiri pa kukula kwauzimu kwa anthu a m’banja.

      Gwiritsani Ntchito Mwanzeru Zida Zophunzitsira

      8. Kodi kagulu ka kapolo kapereka zida zotani zophunzirira Baibulo?

      8 “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wapereka zida zochuluka zimene zingagwiritsidwe ntchito pophunzira. Magazini ya Nsanja ya Olonda, yogwiritsidwa ntchito pamodzi ndi Baibulo, ikupezeka m’zinenero 131. Pali mabuku ophunzirira Baibulo m’zinenero 153, mabolosha m’zinenero 284, makaseti omvetsera m’zinenero 61, mavidiyokaseti m’zinenero 41, ngakhalenso pologalamu yapakompyuta yochitira kafukufuku m’Baibulo m’zinenero 9!​—Mateyu 24:45-47.

      9. Kodi uphungu umene uli m’malemba amene asonyezedwa m’ndime ino tingaugwiritse ntchito motani pamene tikuchita phunziro labanja la Nsanja ya Olonda?

      9 Mabanja ambiri amagwiritsa ntchito nthaŵi ya phunziro labanja kukonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda lampingo. Zimenezitu ndi zothandiza kwambiri! Nsanja ya Olonda imakhala ndi chakudya chauzimu chofunika kwambiri chimene chimaperekedwa kuti chilimbikitse anthu a Yehova padziko lonse. Pamene muphunzira Nsanja ya Olonda monga banja, chitani zambiri kuposa pa kuŵerenga ndime ndi kuyankha mafunso osindikizidwa. Funitsitsani kuti mumvetsetse. Khalani ndi nthaŵi yokwanira yoŵerenga malemba amene asonyezedwa koma osagwidwa mawu. Funsani a m’banjamo kuti afotokoze mmene malembawo akugwirizanira ndi zimene zikutchulidwa m’ndime imene mukukambiranayo. Pangitsani mitima kuloŵetsedwamo.​—Miyambo 4:7, 23; Machitidwe 17:11.

      10. Kodi ndi chiyani chimene chingachitike kuti ana aloŵetsedwe m’phunziro ndi kuti nthaŵiyo ikhale yosangalatsa kwa iwo?

      10 Ngati m’banja lanu muli ana, kodi mungachitenji kuti mupangitse phunziro lanu kukhala osati chabe chizoloŵezi cha banjalo koma nthaŵi yomangirirana, yokondweretsa, ndiponso yosangalatsa? Yesetsani kuchititsa aliyense kuloŵetsedwamo m’njira yoyenera kotero kuti malingaliro akhalebe ali pa nkhani imene mukuphunzirayo. Pamene kuli kotheka, konzani kuti mwana aliyense akhale ndi Baibulo lakelake ndiponso magazini yophunziridwa. Potsatira chikondi chimene Yesu anasonyeza, kholo lingakhale moyandikana kwambiri ndi mwana wamng’ono, mwina lingayangate mwanayo. (Yerekezerani ndi Marko 10:13-16.) Mutu wabanja angauze mwana wamng’ono kuti alongosole chithunzi chimene chili pankhani yomwe ikuphunziridwayo. Mwana wokulirapo angauzidwiretu kuti adzaŵerenge lemba lina. Mwana wamkulu angauzidwe kutchula mbali zimene nkhani yophunziridwayo ingagwiritsidwe ntchito.

      11. Kodi ndi zida zophunzitsira zina ziti zimene zaperekedwa, ndipo kumene zimenezi zimapezeka, kodi zingagwiritsidwe ntchito mopindulitsa motani pa phunziro labanja?

      11 Ngakhale kuti mungakhale mukukambirana nkhani ya mu Nsanja ya Olonda, musaiwale zida zina zophunzirira zimene zimapezeka m’zinenero zambiri. Ngati pakufunika kudziŵa za zonse zimene zinachitika panthaŵiyo kapena pakufunika kulongosola mawu ena a m’Baibulo, Insight on the Scriptures ingakuthandizeni. Mafunso ena angayankhidwe mwa kugwiritsa ntchito Watch Tower Publications Index kapena pologalamu yapakompyuta yochitira kafukufuku imene Sosaite imapereka. Kuphunzira kugwiritsa ntchito zida zimenezi, ngati zilipo m’chinenero chanu, kungakhale mbali yofunika kwambiri ya phunziro labanja. Pokhala ndi cholinga chodzutsa chidwi cha ana, mungapatulenso nthaŵi ina ya phunziro lanulo kuti muonere mbali ina ya imodzi mwa mavidiyo ophunzitsa a Sosaite kapena kumvetsera kambali kena ka seŵero la pakaseti ndiyeno ndi kuzikambirana. Kugwiritsa ntchito bwino zida zophunzirira zimenezi kungathandize kupangitsa phunziro lanu labanja kukhala losangalatsa ndi lopindulitsa kwa banja lonse.

      Sinthani Mogwirizana ndi Zofunika pa Banja Lanu

      12. Kodi phunziro labanja lingathandize motani pochita ndi nkhani zofunika kwambiri pa banja?

      12 Kungakhale kuti banja lanu nthaŵi zambiri limaphunzira nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yophunziridwa mlungu umenewo. Komano onetsetsani zimene zikuchitika m’banja lanu. Ngati amayi sagwira ntchito yolembedwa, akhoza kumacheza ndi anawo tsiku lililonse pamene abwerako kusukulu. Zochitika zina angazithetse panthaŵiyo; zina zingafune chisamaliro chowonjezeka. Pakakhala nkhani zofunika kwambiri pa banjapo, musazinyalanyaze. (Miyambo 27:12) Zimenezi zingakhale osati kokha mavuto a kusukulu komanso zochitika zina. Sankhani nkhani yoyenerera, ndipo mudziŵitsiretu banja lonse zimene mudzaphunzira.

      13. Kodi ndi chifukwa chiyani kungakhale kothandiza kuti banja likambirane mmene lingapiririre umphaŵi?

      13 Mwachitsanzo, mbali yaikulu ya dziko lapansi ili paumphaŵi wadzaoneni; motero m’madera ambiri kungakhale kofunika kukambirana mmene mungapiririre vutoli. Kodi phunziro labanja lokhudza mikhalidwe imene ikuchitikadi pamoyo ndiponso mapulinsipulo a Baibulo lingakhale lothandiza ku banja lanu?​—Miyambo 21:5; Mlaliki 9:11; Ahebri 13:5, 6, 18.

      14. Kodi ndi mikhalidwe iti imene ingapangitse kukambirana kwa banja mmene Yehova amaonera chiwawa, nkhondo, ndi uchete wachikristu kukhala kwapanthaŵi yake?

      14 Nkhani ina yofunika kukambirana ndiyo chiwawa. Tonsefe tifunika kukhomereza zolimba m’maganizo ndi m’mitima mwathu mmene Yehova amaionera nkhaniyi. (Genesis 6:13; Salmo 11:5) Phunziro labanja la nkhani imeneyi ingakhale nthaŵi yabwino yokambirana mmene ana angachitire ndi ana a ndewu kusukulu, kaya kuti iwo aphunzire maluso omenyera, ndiponso mmene angasankhire zosangulutsa zoyenera. Mikangano yachiwawa ili ponseponse; pafupifupi m’dziko lililonse muli mwina nkhondo yapachiŵeniŵeni, mkangano wa zandale kapena wautundu, kapena muli nkhondo za magulu achifwamba. Motero, banja lanu lingafunike kukambirana mmene lingakhalirebe ndi khalidwe lachikristu pakati pa magulu odana.​—Yesaya 2:2-4; Yohane 17:16.

      15. Kodi malangizo onena za kugonana ndi ukwati ayenera kuperekedwa motani kwa ana?

      15 Pamene ana akukula, amafunika kulangizidwa za kugonana ndi ukwati, mogwirizana ndi msinkhu wawo. Pa chikhalidwe cha anthu ena makolo ochuluka sakamba ndi ana awo nkhani za kugonana. Popeza kuti sanalangizidwe, ana angauzidwe zolakwika ndi achinyamata ena, ndipo zotsatira zake zingakhale zoipa kwambiri. Kodi sikungakhale bwino kutsanzira Yehova, amene amapereka uphungu wachindunji komanso wabwino pankhaniyi m’Baibulo? Uphungu waumulungu udzathandiza ana athu kumadzilemekeza nthaŵi zonse ndi kumapatsa ulemu anthu osiyana nawo ziwalo. (Miyambo 5:18-20; Akolose 3:5; 1 Atesalonika 4:3-8) Ngakhale kuti nkhani zimenezi munazikambapo kale, musazengereze kuzikambanso. Popeza kuti pakubuka mikhalidwe yatsopano, kubwereza ndi kofunika.

      16. (a) M’mabanja ambiri, kodi phunziro labanja limachitika liti? (b) Kodi mwathetsa bwanji mavuto kuti mukhale ndi phunziro labanja lokhazikika?

      16 Kodi phunziro labanja lingachitidwe liti? Potsatira mabanja a Beteli padziko lonse lapansi, mabanja ambiri amakhala ndi phunziro lawo labanja Lolemba madzulo. M’mabanja ena ndi zosiyana. Ku Argentina banja lina la anthu 11, momwe munali ana 9, nthaŵi zonse linali kudzuka 5 koloko mmaŵa uliwonse kuti lipange phunziro labanja. Kunali kosatheka kupeza nthaŵi ina chifukwa chosiyana ntchito zimene anali kugwira. Zinali zovuta, koma zinakhomereza kufunika kwa phunziro labanja m’maganizo ndi m’mitima mwa ana. Ku Philippines mkulu wina anali kuchita phunziro labanja mokhazikika ndi mkazi wake ndi ana awo atatu pamene anali kukula. Mkati mwa mlungu makolowo analinso kuphunzira ndi mwana aliyense payekha kuti aliyense apange choonadi kukhala chakechake. Ku United States, mlongo wina amene mwamuna wake si wa Mboni mmaŵa uliwonse amaperekeza ana ake kukakwera basi ya kusukulu kwawo. Pamene akuyembekeza basiyo, amatha mphindi pafupifupi khumi akuŵerenga ndi kukambirana nkhani yophunzira yoyenerera ya Malemba, ndiyeno amayiwo amapereka pemphero lalifupi anawo asanakwere basiyo. Ku Democratic Republic of Congo, mkazi wina amene mwamuna wake wosakhulupirira anachoka panyumbapo amafunika kuyesetsa kuti aphunzire chifukwa sanaphunzire kwenikweni kusukulu. Mwana wake wamwamuna wamkulu amamuthandiza mwa kumabwera mlungu uliwonse kudzachititsa phunziro limene pamakhala amayi akewo ndi azibale ake ang’onoang’ono. Amayiwo amapereka chitsanzo chabwino mwa kukonzekera mwakhama. Kodi pali mkhalidwe wina umene umapangitsa kukhala kovuta kuti m’banja lanu muzikhala ndi phunziro labanja mokhazikika? Musasiye. Funani madalitso a Yehova moona mtima pa kuyesayesa kwanu kuti mukhale ndi phunziro la Baibulo lokhazikika.​—Marko 11:23, 24.

      Mapindu a Kuchita Khama

      17. (a) Kuti mukhale ndi phunziro labanja lokhazikika, kodi chimafunika ndi chiyani? (b) Ndi chochitika chiti chimene chikusonyeza kufunika kwakuti banja lizilangizidwa njira za Yehova nthaŵi zonse?

      17 Kulinganiza zinthu ndi kofunika. Kuchita khama ndi kofunikanso. Koma mapindu amene amapezeka m’phunziro labanja lokhazikika alidi oyenera zimenezo. (Miyambo 22:6; 3 Yohane 4) Ku Germany, Franz ndi Hilda, anali ndi banja la ana 11. Patatha zaka zochuluka, mwana wawo wamkazi Magdalena anati: “Masiku ano chimene ndimaona kuti chinali chofunika koposa ndi chakuti panalibe tsiku ndi limodzi lomwe limene sitinalandirepo malangizo auzimu.” Pamene mzimu wautundu unakula kwambiri mu ulamuliro wa Adolf Hitler, atate ake a Magdalena anagwiritsa ntchito Baibulo kukonzekeretsa banja lawo pa ziyeso zimene anaona kuti zinali kubwera. M’kupita kwa nthaŵi, ana ang’onoang’ono a m’banjalo anagwidwa ndi kupita nawo kusukulu yosintha khalidwe la akaidi; ena a m’banjamo anamangidwa ndi kukawaika m’ndende ndi m’misasa yachibalo. Ena anaphedwa. Chikhulupiriro cha onsewo chinalimbabe​—osati kokha panthaŵi imeneyo ya kuzunzidwa mwakhanza, komanso, kwa amene anapulumuka, m’zaka zimene zinatsatira.

      18. Kodi zoyesayesa za makolo opanda mnzawo wamuukwati zafupidwa motani?

      18 Makolo ambiri amene alibe mnzawo wamuukwati, komanso amene amasiyana zikhulupiriro ndi mnzawo wamuukwati, nawonso apereka malango a m’Baibulo mokhazikika kwa ana awo. Ku India, mayi wina, wamasiye, anayesetsa kukhomereza kukonda Yehova mwa ana ake aŵiri. Komabe, anakhumudwa kwambiri pamene mwana wake wamwamuna anasiya kuyanjana ndi anthu a Yehova. Iye anapempha Yehova kuti amukhululukire zolakwa zilizonse zimene anachita pophunzitsa mwana wakeyo. Komatu mwanayo sanaiwaliretu zimene anaphunzira. Patatha zaka zoposa khumi, anabwerera napita patsogolo kwambiri mwauzimu, ndipo anadzakhala mkulu mumpingo. Tsopano iye ndi mkazi wake akutumikira monga atumiki anthaŵi zonse achipainiya. Makolo amene alabadira uphungu wa Yehova ndi gulu lake wopereka malango a m’Baibulo nthaŵi zonse m’banja lawo alidi oyamikira kwambiri! Kodi inu m’banja lanu mukugwiritsa ntchito uphungu umenewo?

      Kodi Mungalongosole?

      ◻ Kodi ndi chifukwa chiyani phunziro labanja lokhazikika lili lofunika?

      ◻ Kodi zolinga zathu ziyenera kukhala zotani paphunziro labanja lililonse?

      ◻ Kodi tapatsidwa zida zophunzirira zotani?

      ◻ Kodi tingasinthe motani phunziro kuti ligwirizane ndi zofunika pabanjapo?

      [Chithunzi patsamba 15]

      Zolinga zenizeni zidzalimbikitsa phunziro lanu labanja

  • Mabanja, Tamandani Mulungu Monga Mbali ya Mpingo Wake
    Nsanja ya Olonda—1999 | July 1
    • Mabanja, Tamandani Mulungu Monga Mbali ya Mpingo Wake

      “M’masonkhano ndidzalemekeza Yehova.”​—SALMO 26:12.

      1. Kuphatikiza pa kuphunzira ndi kupemphera kunyumba, kodi mbali ina yofunika ya kulambira koona ndi iti?

      KULAMBIRA Yehova sikuphatikizapo kupemphera ndi kuphunzira Baibulo kunyumba kokha komanso zochita zina monga mbali ya mpingo wa Mulungu. Aisrayeli akale analamulidwa ‘kusonkhanitsa anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang’ono,’ kuti aphunzire chilamulo cha Mulungu kotero kuti akayende m’njira yake. (Deuteronomo 31:12; Yoswa 8:35) Onse okalamba komanso ‘anyamata ndi anamwali’ analimbikitsidwa kutenga mbali m’kutamanda dzina la Yehova. (Salmo 148:12, 13) Makonzedwe ofananawo akugwiranso ntchito mumpingo wachikristu. M’Nyumba za Ufumu padziko lonse lapansi, amuna, akazi, ndi ana momasuka amatengamo mbali m’zochitika zimene zimaloŵetsamo omvetsera, ndipo ambiri amasangalala kwambiri pochita zimenezi.​—Ahebri 10:23-25.

      2. (a) Kodi ndi chifukwa chiyani kukonzekera kuli chinthu chofunika kwambiri pothandiza ana kusangalala ndi misonkhano? (b) Kodi ndi chitsanzo chayani chimene chili chofunika?

      2 Zoonadi, ndi kovuta kuthandiza ana kukhala ndi chizoloŵezi chabwino cha zochita zampingo. Ngati ana ena amene amafika pamisonkhano ndi makolo awo amaoneka kuti sasangalala nayo, kodi vuto lingakhale chiyani? Zoonadi, ana ambiri amakhala tcheru kwa nthaŵi yochepa ndipo zinthu sizikhalira kuwatopetsa. Kukonzekera kungathandize kuthetsa vuto limeneli. Popanda kukonzekera, misonkhano singakhale yatanthauzo lililonse kwa ana. (Miyambo 15:23) Popanda kukonzekera, kudzakhala kovuta kuti iwo apite patsogolo mwauzimu kumene kumadzetsa chikhutiro. (1 Timoteo 4:12, 15) Kodi tingachite chiyani? Choyamba, makolo afunika kudzifunsa ngati iwowo amakonzekera misonkhano. Chitsanzo chawo n’chisonkhezero champhamvu. (Luka 6:40) Kulinganiza bwino phunziro labanja kulinso kofunika kwambiri.

      Kuumba Mtima

      3. Paphunziro labanja, kodi ndi chifukwa chiyani muyenera kuyesetsa mwapadera kuti muumbe mitima, ndipo kodi zimenezi zimafunanji?

      3 Nthaŵi ya phunziro labanja iyenera kukhala nthaŵi osati chabe yodzaza chidziŵitso m’mitu komanso iyenera kukhala nthaŵi youmba mitima. Izi zimafuna kuti muzizindikira mavuto amene anthu a m’banja lanu akukumana nawo ndi kusonyeza chisamaliro chachikondi kwa aliyense m’banjamo. Yehova ‘amayesa mtima.’​—1 Mbiri 29:17.

      4. (a) Kodi kukhala “wosoŵa nzeru” kumatanthauzanji? (b) Kodi ‘kulandira nzeru’ kumaphatikizapo chiyani?

      4 Kodi Yehova amapezanji pamene ayesa mitima ya ana athu? Ambiri anganene kuti amakonda Mulungu, ndipo zimenezi ndi zoyamikirika. Komabe, mwana kapena munthu amene akuphunzira kumene za Yehova sadziŵa njira zochuluka za Yehova. Chifukwa chakuti ndi mwana, iye angakhale “wosoŵa nzeru,” monga momwe Baibulo limanenera. Mwinamwake si zolinga zake zonse zimene zili zoipa, koma pamatenga nthaŵi kuti munthu apangitse mtima wake kukhala mumkhalidwe umene umasangalatsadi Mulungu. Izi zimaphatikizapo kuchititsa maganizo ako, zokhumba zako, zokonda zako, malingaliro ako, ndi zolinga zako m’moyo kukhala zogwirizana ndi zimene Mulungu amavomereza, kufika pamene zimenezi zingakhale zotheka kwa anthu opanda ungwiro. Pamene munthu aumba umunthu wake wamkati moteromo m’njira yaumulungu, ndiye kuti iye ‘akulandira nzeru.’​—Miyambo 9:4; 19:8.

      5, 6. Kodi makolo angawathandize bwanji ana awo ‘kulandira nzeru’?

      5 Kodi makolo angathandize ana awo ‘kulandira nzeru’? Zoonadi, palibe munthu amene angapatse munthu mnzake mtima wabwino. Aliyense wa ife anapatsidwa ufulu wakudzisankhira, ndipo zambiri zimadalira pa zimene ifeyo timalingalira. Komabe mwa kuzindikira, makolo nthaŵi zambiri angachititse mwana wawo kunena zakukhosi kwake, akumazindikira zimene zili mumtima mwake ndiponso mbali zimene akufunika thandizo. Gwiritsani ntchito mafunso onga akuti ‘Kodi ukumva bwanji ndi zimenezi?’ ndi ‘Kodi ukufuna utachita chiyani kwenikweni?’ Ndiyeno, mvetserani modekha. Musachite zinthu mopsa mtima. (Miyambo 20:5) Ndi kofunika kukhala wachifundo, womvetsetsa, ndi wachikondi ngati mukufuna kuwafika pamtima.

      6 Kuti mulimbikitse malingaliro abwino, nthaŵi ndi nthaŵi kambiranani za chipatso cha mzimu​—mbali yake iliyonse​—ndipo nonse pamodzi monga banja yesetsani kuchikulitsa. (Agalatiya 5:22, 23) Kulitsani chikondi pa Yehova ndi Yesu Kristu, osati chabe mwakungonena kuti tiyenera kuwakonda koma kulongosola zifukwa zake tiyenera kuwakonda ndiponso mmene tingasonyezere chikondi chimenecho. (2 Akorinto 5:14, 15) Limbitsani chikhumbo chochita zimene zili zabwino mwa kulingalira za mapindu amene adzakhalapo. Kulitsani chikhumbo chokana maganizo oipa, nkhani zachabe, ndi khalidwe loipa mwa kukambirana kuipa kwa zinthu zimenezo. (Amosi 5:15; 3 Yohane 11) Sonyezani mmene maganizo, zolankhula, ndi khalidwe​—kaya zabwino kapena zoipa​—zingakhudzire unansi wa munthu ndi Yehova.

      7. Kodi ndi chiyani chimene tingachite pothandiza ana kulimbana ndi mavuto ndi kusankha zochita m’njira imene idzawapangitsa kukhalabe oyandikana ndi Yehova?

      7 Pamene mwana ali ndi vuto kapena akufunika kupanga chosankha chachikulu, tingamufunse kuti: ‘Kodi ukuganiza kuti Yehova amaziona bwanji zimenezi? Kodi ukudziŵa chiyani chokhudza Yehova chimene chikukupangitsa kunena zimenezi? Kodi wapemphera kwa iye za zimenezi?’ Mwa kuyamba mwamsanga monga momwe mungathere, thandizani ana anu kukhala ndi moyo umene nthaŵi zonse umayesetsa moona mtima kuzindikira chifuno cha Mulungu ndiyeno ndi kuchichita. Pamene afika pokhala ndi unansi wathithithi ndi Yehova, iwo adzasangalala kuyenda m’njira zake. (Salmo 119:34, 35) Zimenezi zidzawapangitsa kuyamikira mwayi woyanjana ndi mpingo wa Mulungu woona.

      Kukonzekera Misonkhano ya Mpingo

      8. (a) Kodi ndi chiyani chimene chingatithandize kuti phunziro lathu labanja liziphatikizapo nkhani iliyonse yofunika kuisamalira? (b) Kodi phunziro limeneli ndi lofunika bwanji?

      8 Pali nkhani zambiri zimene timafunika kuzisamalira panthaŵi ya phunziro labanja. Kodi zonsezo mungazikwanitse bwanji panthaŵiyo? Ndi kosatheka kuchita zonse panthaŵi imodzi. Koma mudzaona kuti zimathandiza mukakhala ndi mpambo wa zofunika kuchita. (Miyambo 21:5) Upendeni nthaŵi ndi nthaŵi, ndipo onani zimene zikufunika kuzisamalira mwapadera. Khalani wachidwi ndi mmene aliyense m’banjamo akupitira patsogolo. Makonzedwe ameneŵa a phunziro labanja ali mbali yofunika ya maphunziro achikristu, otikonzekeretsa kukhala ndi moyo tsopano ndiponso moyo wosatha umene ukubwera.​—1 Timoteo 4:8.

      9. Kodi ndi zolinga ziti zokhudza kukonzekera misonkhano zimene tingagwirirepo ntchito pang’onopang’ono panthaŵi ya maphunziro athu abanja?

      9 Kodi phunziro lanu labanja limaphatikizapo kukonzekera misonkhano ya mpingo? Pali zinthu zambiri zimene mungamagwirirepo ntchito mwapang’onopang’ono pamene mukuphunzira pamodzi. Zina mwa zimenezi zingatenge milungu ingapo, zina miyezi, zina mwina ngakhale zaka kuti muzikwanitse. Lingalirani zolinga izi: (1) aliyense m’banjamo kukhala wokonzeka kukayankha pamisonkhano ya mpingo; (2) aliyense ayenera kuyesetsa kuti aziyankha m’mawu akeake; (3) kuphatikiza malemba m’mayankho; ndi (4) kupenda nkhaniyo ndi cholinga chofuna kuona mmene munthuwe ungaigwiritse ntchito. Zonsezi zingathandize munthu kupanga choonadi kukhala chakechake.​—Salmo 25:4, 5.

      10. (a) Kodi tingasamalire motani uliwonse wa misonkhano yathu ya mpingo? (b) Kodi ndi chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?

      10 Ngakhale ngati nthaŵi zambiri phunziro lanu labanja limakhala pa phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu umenewo, musanyalanyaze kufunika kwakuti munthu aliyense payekha kapena banja lonse pamodzi lizikonzekera Phunziro la Buku la Mpingo, Sukulu ya Utumiki Wateokalase, ndi Msonkhano wa Utumiki. Zimenezinso ndi mbali zofunika za pologalamu yotiphunzitsa kuyenda m’njira ya Yehova. Mwa nthaŵi ndi nthaŵi mungathe kumakonzekera misonkhano pamodzi monga banja. Mwa kuchitira zinthu pamodzi, mudzawongolera maluso anu akuphunzira. Chotsatira chake, mudzapeza mapindu ochuluka pamisonkhano yeniyeniyo. Mwa zinthu zina, kambiranani mapindu a kukonzekera misonkhano imeneyi nthaŵi zonse ndi kufunika koika nthaŵi yeniyeni yochitira zimenezi.​—Aefeso 5:15-17.

      11, 12. Kodi kukonzekera kuimba pampingo kudzatipindulitsa motani, ndipo kodi zimenezi tingazichite motani?

      11 Pa Misonkhano Yachigawo ya “Njira ya Moyo ya Mulungu,” tinalimbikitsidwa kukonzekera mbali inanso ya misonkhano yathu​—kuimba nyimbo. Kodi mwatsatira zimenezi? Kuchita zimenezi kungathandize kukhomereza choonadi cha Baibulo m’maganizo ndi m’mitima mwathu ndipo panthaŵi yofananayo kungakulitse kusangalala kwathu ndi misonkhano ya mpingo.

      12 Kukonzekera kumene kumaphatikizapo kuŵerenga ndi kukambirana matanthauzo a mawu ena amene ali m’nyimbo zondandalikitsidwa kungatithandize kuti tiziimba mochokera pansi pamtima. Mu Israyeli wakale, zida zoimbira zinali kugwiritsidwa ntchito kwambiri polambira. (1 Mbiri 25:1; Salmo 28:7) Kodi alipo wina m’banja lanu amene amagwiritsa ntchito chida choimbira? Bwanji osagwiritsa ntchito chida chimenecho pochita pulakatesi imodzi mwa nyimbo za Ufumu za mlungu umenewo, ndiyeno imbani nyimboyo monga banja. Njira ina ndiyo kugwiritsa ntchito makaseti ojambulidwa a nyimbozo. M’mayiko ena abale athu amaimba bwino kwambiri ndi pakamwa pokha opanda zida zoimbira. Pamene akuyenda panjira kaya akugwira ntchito zawo m’munda, kaŵirikaŵiri amakonda kuimba nyimbo zimene zidzaimbidwa pa misonkhano ya mpingo mlungu umenewo.​—Aefeso 5:19.

      Kukonzekera Utumiki Wakumunda kwa Banja

      13, 14. Kodi ndi chifukwa chiyani kukambirana kwa banja kumene kumakonzekeretsa mitima yathu kaamba ka utumiki wakumunda kuli kofunika kwambiri?

      13 Kuchitira umboni kwa ena za Yehova ndi chifuno chake ndi mbali yofunika ya moyo wathu. (Yesaya 43:10-12; Mateyu 24:14) Kaya ndife ana kapena achikulire, timasangalala kwambiri ndi ntchito imeneyi ndipo timapeza mapindu ochuluka ngati takonzekera. Kodi zimenezi tingazichite motani m’banja?

      14 Mofanana ndi nkhani zonse zokhudza kulambira kwathu, ndi kofunika kukonzekeretsa mitima yathu. Tifunika kukambirana osati kokha zimene tikukachita komanso chifukwa chake tikukachita zimenezo. M’masiku a Mfumu Yehosafati, anthu analangizidwa m’chilamulo cha Mulungu, koma Baibulo limatiuza kuti iwo “sadakonzere mitima yawo.” Zimenezi zinawapangitsa kukhala osatetezeka ku zinthu zimene zikanawapatutsa pa kulambira koona. (2 Mbiri 20:33; 21:11) Cholinga chathu sichakuti tizitha chabe kupereka lipoti la maola amene tathera mu utumiki wakumunda, komanso sichakungogaŵira mabuku. Utumiki wathu uyenera kukhala chisonyezero cha chikondi chathu pa Yehova ndiponso pa anthu amene akufuna mwayi wosankha moyo. (Ahebri 13:15) Ndiyo ntchito imene ife tili “antchito anzake a Mulungu.” (1 Akorinto 3:9) Ndi mwayi waukulu bwanji! Pamene tikuchita utumiki, timatero mogwirizana ndi angelo oyera. (Chivumbulutso 14:6, 7) Ndi nthaŵi inanso yabwino iti imene ingakhalepo yokulitsira kuyamikira zimenezi kuposa pamene banja likukambirana, kaya ndi paphunziro lathu la mlungu ndi mlungu kapena pokambirana lemba logwirizana ndi zimenezi kuchokera mu Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku!

      15. Kodi ndi nthaŵi iti imene tingakonzekere utumiki wakumunda monga banja?

      15 Kodi inu nthaŵi ndi nthaŵi mumagwiritsa ntchito nthaŵi ya phunziro lanu labanja kuthandiza anthu a m’banja lanu kukonzekera utumiki wakumunda wa mlunguwo? Kuchita zimenezi kungakhale kopindulitsa kwambiri. (2 Timoteo 2:15) Zingathandize kuti utumiki wawo ukhale watanthauzo ndi waphindu. Nthaŵi zina, mungapatule nthaŵi yonse ya phunziro kuti mukonzekere zimenezi. Kaŵirikaŵiri, mungamakambirane mbali zina za utumiki wakumunda kwa kanthaŵi kochepa mukamaliza phunziro labanja kapena nthaŵi ina mkati mwa mlunguwo.

      16. Fotokozani phindu la sitepe lililonse lotchulidwa m’ndime ino.

      16 Mungakhale ndi masitepe angapo oti muzikonzekera monga banja, masitepe onga aŵa: (1) Kukonzekera ulaliki woyesereredwa bwino kwambiri komanso lemba loti likaŵerengedwe ngati mpata ukalola. (2) Ngati ndi kotheka, onetsetsani kuti aliyense ali ndi chikwama chakechake cha mu utumiki wakumunda, Baibulo, notibuku, cholembera kapena pensulo, mathirakiti, ndi mabuku ena omwe ali mumkhalidwe wabwino. Chikwama cha mu utumiki sichiyenera kuchita kukhala chamtengo wapatali, koma chiyenera kukhala chaudongo. (3) Kambiranani malo amene mungachite umboni wamwamwayi ndi mmene mungauchitire. Mbali iliyonse ya malangizo ameneŵa itsatireni komanso nthaŵi imene mumayendera limodzi mu utumiki wakumunda. Perekani malingaliro othandiza, koma musapereke uphungu pa mfundo zochuluka.

      17, 18. (a) Kodi ndi kukonzekera monga banja kotani kumene kungathandize kuti utumiki wathu wakumunda ukhale waphindu kwambiri? (b) Kodi ndi mbali iti ya kukonzekera kumeneku imene ingamachitidwe mlungu uliwonse?

      17 Mbali yaikulu ya ntchito imene Yesu Kristu anapatsa otsatira ake ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 28:19, 20) Kupanga ophunzira kumafuna zambiri kuposa chabe kulalikira. Kumafuna kuphunzitsa. Kodi phunziro lanu labanja lingakuthandizeni motani kukwanitsa kuchita zimenezi?

      18 Monga banja, kambiranani anthu amene kungakhale bwino kuwafikiranso paulendo wobwereza. Ena a iwo angakhale atatenga mabuku; ena mwina anangomvetsera. Mungakhale mutakumana nawo pantchito ya kunyumba ndi nyumba kapena pochita umboni wamwamwayi kumsika kapena kusukulu. Lolani kuti Mawu a Mulungu akutsogolereni. (Salmo 25:9; Ezekieli 9:4) Sankhani aliyense wa inu amene akufuna kumuchezera mlungu umenewo. Kodi mukakamba chiyani? Kukambirana kwa banja kungathandize aliyense m’banjamo kukonzekera. Dziŵani malemba enieni amene mudzakambirana ndi anthu ochita chidwi ndiponso mfundo zoyenera za mu bolosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena mu buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Musayese kulongosola zinthu zambirimbiri pa ulendo umodzi. Musiyireni funso mwininyumba limene mudzayankhe paulendo wanu wotsatira. Bwanji osakonza kuti zikhale mbali ya zochita za mlungu uliwonse za banja lanu kulinganiza maulendo obwereza amene aliyense adzapanga, nthaŵi imene adzachita zimenezo, ndi zimene akuyembekeza kukakwaniritsa. Kuchita zimenezi kungathandize kuti utumiki wakumunda wa banja lonselo ukhale wopindulitsa kwambiri.

      Pitirizani Kuwaphunzitsa Njira ya Yehova

      19. Kuti anthu a m’banja lanu apitirize kuyenda m’njira ya Yehova, kodi iwo afunika kumatani, ndipo kodi ndi chiyani chimene chimapangitsa zimenezi?

      19 Kukhala mutu wabanja m’dziko loipali si chinthu chapafupi. Satana ndi ziŵanda zake akuyesetsa kuwononga mkhalidwe wauzimu wa atumiki a Yehova. (1 Petro 5:8) Ndiponso, lerolino makolo mukukumana ndi mavuto ambiri, makamaka inu makolo amene mulibe mnzanu wamuukwati. Ndi kovuta kupeza nthaŵi yochita zinthu zonse zimene mumafuna kuchita. Koma n’koyenera kuyesetsa, ngakhale ngati mutamagwiritsa ntchito lingaliro limodzi lokha panthaŵi imodzi, ndipo pang’onopang’ono kudzawongolera pologalamu yanu ya phunziro labanja. Kuona anthu amene mumakhala nawo pamodzi akuyenda mokhulupirika m’njira ya Yehova, ndi mphotho yosangalatsa kwambiri. Kuti ayende bwinobwino m’njira ya Yehova, anthu a m’banja lanu afunika kumasangalala popezeka pamisonkhano yampingo ndi pochita utumiki wakumunda. Kuti zimenezi zitheke, kukonzekera kumafunika​—kukonzekera kumene kumaumba mtima ndi kukonzekeretsa aliyense kutengamo mbali mwatanthauzo.

      20. Kodi ndi chiyani chimene chingathandize makolo ambiri kukhala ndi chimwemwe chonga chotchulidwa pa 3 Yohane 4?

      20 Ponena za anthu amene anawathandiza mwauzimu, mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti ali kuyenda m’choonadi.” (3 Yohane 4) Maphunziro abanja amene amachititsidwa m’maganizo muli zolinga zenizeni ndiponso mitu ya mabanja imene imachita zinthu mwachifundo ndi mothandiza pa zofunika zilizonse za anthu a m’banja lawo angathandize kwambiri kuti banjalo likhale ndi chimwemwe choterocho. Mwa kukulitsa kuyamikira njira ya moyo ya Mulungu, makolo amathandiza banja lawo kusangalala ndi njira ya moyo yabwino kwambiri.​—Salmo 19:7-11.

      Kodi Mungalongosole?

      ◻ Kodi ndi chifukwa chiyani kukonzekera misonkhano kuli kofunika kwambiri kwa ana athu?

      ◻ Kodi makolo angawathandize motani ana awo ‘kulandira nzeru’?

      ◻ Kodi phunziro lathu labanja lingathandize motani kukonzekera misonkhano yonse?

      ◻ Kodi kukonzekera utumiki wakumunda monga banja kungatithandize motani kukhala ogwira mtima kwambiri?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena