Nyimbo 101
Kusonyeza Kudera Nkhaŵa ndi “Gulu la Nkhosa la Mulungu”
1. Yesu ndi Mbusa wabwino,
Adera nkhaŵa nkhosa.
Anatigula ifetu.
Tiphunzira zambiri.
2. Mkulu ndi Mbusa wamng’ono;
Ayang’anira “nkhosa.”
Akhazikitse chitsanzo
Ndi kukhala wamaso.
3. ‘Dyetsa Nkhosa’ ati Yesu
Kwa munthu wachikondi.
Mwachikondi ndi modekha,
Thandizani onsewo.
4. Monga gulu la mtendere—
Tiri ndi madalitso.
Yehova ndi Yesu Kristu
Amatiweta ife.