Nyimbo 140
Kuyembekeza pa Yehova
1. Chifundo chanu Mulungu
Chatisunga ife!
Zifundo zanu zisathe
Kwa ife tonsefe!
2. Zifundo zanu Yehova,
Ziri zatsopano.
Muli wokhulupirika
Kwa odalira’nu.
3. Kuli kwabwino kwa munthu
Kusenza goliro,
Kuyembekezera M’lungu,
Pomtumikirabe.
4. Yehova M’lungu ndiwathu.
O tisonyezetu
Mkhalidwe wofatsa m’moyo,
Pophunzira zanu!