Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi Mboni za Yehova zimalandira majekeseni okhala ndi mbali za mwazi, monga ngati immune globulin kapena albumin?
Ena amatero, akumakhulupirira kuti Malemba samaletsa mwachindunji kulandira jekeseni wokhala ndi mlingo wochepa, kapena mbali, zotengedwa ku mwazi.
Poyambapo Mlengi anaika thayo pa anthu onse kupeŵa kudya mwazi: “Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu . . . Koma nyama, m’mene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.” (Genesis 9:3, 4) Mwazi unali wopatulika ndipo chotero ukanagwiritsidwa ntchito popereka nsembe pokha. Ngati sunagwiritsidwe ntchito mwanjira imeneyo, uwo unayenera kufotseredwa pansi.—Levitiko 17:13, 14; Deuteronomo 12:15, 16.
Ichi sichinali chiletso wamba chosakhalitsa kwa Ayuda. Kufunika kwa kusala mwazi kunalongosoledwanso kwa Akristu. (Machitidwe 21:25) Mowazinga iwo mu Ufumu wa Roma, lamulo la Mulungu linali kuswedwa kaŵirikaŵiri, popeza kuti anthu ankadya chakudya chopangidwa ndi mwazi. Linkaswedwanso pazifukwa za “mankhwala”; Tertullian akusimba kuti anthu ena ankamwa mwazi akumaganiza kuti ungachiritse khunyu. ‘Ankamwa ndi ludzu laumbombo mwazi wa apandu ophedwa m’bwalo.’ Iye anawonjezera kuti: “Njira zanu zoipa nzomvetsa manyazi pamaso pa Akristu, amene sakhala konse ndi mwazi wa nyama pa zakudya zawo.” Mboni za Yehova lerolino nzogamulapo kusalakwira lamulo la Mulungu, mosasamala kanthu kuti nchozoloŵereka motani kwa ena kudya chakudya chopangidwa ndi mwazi. M’ma 1940, kuthiridwa mwazi kunkagwiritsiridwa ntchito mofala, ndipo Mboni zinazindikira kuti kumvera Mulungu kunafunikira kuti apeŵenso kuthiridwa mwazi, ngakhale adokotala atakukakamiza.
Poyamba, kuthiridwa mwazi kochuluka kunali kwa mwazi wathunthu. Pambuyo pake, ofufuza anayamba kulekanitsa mwazi m’mbali zake zazikulu, popeza adokotala anatsimikizira kuti wodwala wina sangafunikire mbali zonse zazikulu za mwazi. Atampatsa iye mbali imodzi yokha, chingakhale ndi ngozi yochepa kwa iye, ndipo adokotala angagwiritsire ntchito yaikulu mwazi umene ali nawo.
Mwazi wa anthu ungalekanitsidwe kukhala mbali yodera yokhala ndi maselo ndiponso mbali ya madzi achikasu (plasma, kapena serum). Mbali yokhala ndi maselo (yokhalamo maperesenti 45) njopangidwa ndi amene mofala amadziŵika kukhala maselo ofiira, maselo oyera, ndi maplatelet. Maperesenti 55 enawo ndi plasma. Iyi njopangidwa ndi maperesenti 90 a madzi, koma imanyamula unyinji wochepa wa maproteni ambiri, mahormone, mchere, ndi maenzyme. Lerolino, mwazi wambiri woperekedwa umalekanitsidwa m’mbali zake zazikulu. Wodwala wina angathiridwe plasma (mwimwake FFP, fresh frozen plasma [plasma yatsopano yoziziritsidwa]) kuchiritsa shoko. Koma wodwala wopereŵera mwazi angapatsidwe maselo ofiira a mu nkhokwe, ndiko kuti, maselo ofiira amene anasungidwa ndi kuikidwa m’madzi kenaka nkuthiridwa m’thupi. Maplatelet ndi maselo oyera amathiridwanso koma mochepera.
M’nthaŵi za Baibulo anthu anali asanapange maluso oterowo ogwiritsira ntchito mbali zimenezi. Mulungu adangolamula kuti: ‘Musale mwazi.’ (Machitidwe 15:28, 29) Koma kodi nchifukwa ninji aliyense ayenera kuganiza kuti pakakhala kusiyana kaya ngati mwaziwo unali wathunthu kapena unalekanitsidwa m’mbali zimenezi? Ngakhale kuti anthu ena ankamwa mwazi, Akristu anakana ngakhale ngati zinatanthauza imfa. Kodi mukuganiza kuti iwo akanavomereza mosiyana ngati munthu wina anasonkhanitsa mwaziwo, kuuleka kuti ugaŵanike, ndipo kenaka nkuwapatsa plasma yokha kapena uŵende wokha, mwinamwake m’masosichi amwazi? Ndithudi, ayi! Chotero, Mboni za Yehova sizimavomereza kuthiridwa mwazi wathunthu kapena mbali zake zazikulu (maselo ofiira, maselo oyera, maplatelet, kapena plasma) zogwiritsiridwa ntchito kukwaniritsa cholinga chofananacho.
Komabe, monga mmene funsolo likusonyezera, asayansi aphunzira ponena za mbali za mwazi ndi mmene angazigwiritsire ntchito. Zochitika zambiri zimakhudza maproteni a plasma—maglobulin, albumin, ndi fibrinogen. Mwachidziŵikire, kogwiritsiridwa ntchito mofala monga mankhwala ndiko kulasa immune globulin. Kodi nchifukwa ninji zimenezo zimachitidwa?
Thupi lanu lingatulutse maantibody (asilikali a thupi) olimbana ndi matenda ena, kukupatsani chitetezo chokhalitsa. Ameneŵa ndiwo maziko opatsidwira katemera pasadakhale (toxoid) wolimbana ndi polio, matsagwidi, rubella (chikuku), diphtheria-tetanus-pertussis, ndi malungo a typhoid. Komabe, ngati wina wavumbulidwa posachedwa ku matenda ena owopsya, asing’anga angavomereze jekeseni wa serum (antitoxin) kumpatsa chitetezo chosakhalitsa cha panthaŵi yomweyo. Kufikira posachedwapa majekeseni oterowo apangidwa mwakuchotsa immune globulin, imene imakhala ndi asilikali a thupi kuchokera kwa munthu wotetezeredwa kale.a Chitetezo chosakhalitsa chotengedwa ku jekeseni yoteroyo sichikhalitsa, popeza kuti asilikali a thupi oloŵetsedwa m’thupiwo m’kupita kwa nthaŵi amatuluka m’dongosolo lake.
Polingalira lamulo la ‘kusala mwazi,’ Akristu ena alingalira kuti sayenera kulandira jekeseni wa immune globulin (proteni), ngakhale kuti inali mbali ya mwazi yokha. Kaimidwe kawo nkomveka ndipo kosavuta—amakana mbali ya mwazi mu mpangidwe uliwonse kapena unyinji.
Ena alingalira kuti serum (antitoxin), monga ngati immune globulin, yokhala ndi mbali yochepa yokha ya plasma ya mwazi wa woperekayo ndipo yogwiritsiridwa ntchito kuwonjezera kulimbana kwa thupi lawo ndi matenda, ngosafanana ndi kuthiridwa mwazi kochilikiza moyo. Chotero zikumbumtima zawo sizingawaletse kulandira immune globulin kapena mbali zakutizakuti zofanana nayo.b Iwo angalingalire kuti kwa iwo chosankha chidzakhala pa kaya ngati ali ofunitsitsa kulandira ngozi zaumoyo zoloŵetsedwamo m’jekeseni yopangidwa ndi mwazi wa munthu wina.
Nchodziŵika kuti dongosolo la mwazi wa mkazi wapakati nlosiyana ndi la mluza wokhala m’chibaliro chake; mitundu yawo ya mwazi kaŵirikaŵiri imakhala yosiyana. Mayiyo samapatsira mwazi wake kwa mluzawo. Zinthu zopangidwa (maselo) zochokera ku mwazi wa mayiyo sizimapita kwa mluzawo kudutsa nsapo, osatinso plasma. Kwenikwenidi, ngati mwangozi inayake mwazi wa mayiyo ndi wa mluza usakanizikana, vuto laumoyo lingabuke (kusasakanizikana kwa Rh kapena ABO). Komabe, zinthu zina zochokera ku plasma zimadutsa kuloŵa dongosolo la mwazi la mluzawo. Kodi maproteni a plasma, onga ngati immune globulin ndi albumin amadutsa? Inde, ena amadutsa.
Mkazi wapakati ali ndi dongosolo lamphamvu mwa limene immune globulin ina imachoka ku mwazi wa mayiyo kupita ku mwazi wa mluzawo. Chifukwa chakuti kayendedwe kachibadwa kameneka ka asilikali a thupi kupita ku mluza kamachitika m’mimba zonse, ana amabadwa ndi mlingo wachibadwa wa kutetezeredwa ku matenda ena.
Nzofanana ndi albumin, imene adokotala angavomereze kukhala mankhwala a shoko kapena mikhalidwe ina.c Ofufuza atsimikizira kuti albumin yochokera ku plasma imatumizidwanso, ngakhale kuti mochepa kwambiri, kudutsa nsapo kuchokera kwa mayi kupita kwa mluza wake.
Kunena kuti mbali zina za proteni yochokera ku plasma zimayenda mwachibadwa kuloŵa m’dongosolo la mwazi la munthu wina (mluza) chingakhale cholingalira china cha Mkristu pamene akulingalira kaya ngati angalandire kuthiridwa immune globulin, albumin, kapena majekeseni olingana ndi awa a mbali za plasma. Munthu wina angaganize kuti m’chikumbumtima chake chabwino angatero; winawake angaganize kuti sangatero. Aliyense ayenera kugamula nkhaniyo mwaumwini pamaso pa Mulungu.
[Mawu a M’munsi]
a Ndi maluso a DNA yosakanizidwa, kapena uinjiniya wa majini, asayansi akupanga zinthu zofananazo zimene sizipangidwa ndi mwazi.
b Chitsanzo chimodzi ndicho Rh immune globulin, imene adokotala angavomereze pamene pali kusagwirizana kwa Rh ya nakubala ndi mluza wake. Ina ndi Factor VIII, imene imaperekedwa kwa odwala hemophilia.
c Umboni ukusonyeza kuti madzi opanda mwazi oulowa m’malo monga ngati (hetastarch [HES]) angagwiritsiridwe ntchito mokhutiritsa kuchiritsa shoko ndi mikhalidwe ina imene nthaŵi zakale madzi a albumin ankagwiritsiridwa ntchito.