Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Tchimo
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Kodi uchimo umayambukira motani unansi wa munthu ndi Mulungu?

      1 Yoh. 3:4, 8: “Yense wakuchita tchimo achitanso kusayeruzika; ndipo tchimo ndiro kusayeruzika. Iye wochita tchimo ali wochokera mwa Mdyerekezi.” (Mawuŵa ngamphamvu chotani nanga! Awo amene mwadala amasankha njira ya uchimo, akumauchita mwachizoloŵezi, amawonedwa ndi Mulungu kukhala apandu. Njira imene iwo asankha ndiyo imene Satana mwiniyo anatenga poyamba.)

      Aroma 5:8, 10: “Pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife. . . . pokhala ife adani ake tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake.” (Tawonani kuti ochimwa akutchulidwa kukhala adani a Mulungu. Pamenepo, ndikwanzeru chotani nanga, kuti ife tipindule ndi makonzedwe amene Mulungu wapanga akuyanjanitsidwa naye!)

      1 Tim. 1:13: “Anandichitira chifundo [akutero mtumwi Paulo], popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira.” (Koma pamene anasonyezedwa njira yolungama ndi Ambuye, iye sanaleke kuilondola.)

      2 Akor. 6:1, 2: “Ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu, (pakuti anena, M’nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m’tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza; tawonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, tawonani, tsopano ndiro tsiku la chipulumutso.)” (Tsopano ndiyo nthaŵi pamene mwaŵi wa chipulumutso uli wopezeka. Mulungu sadzapereka kukoma mtima kwachifundo kotero kwa mtundu wa anthu kunthaŵi zonse. Chotero, chisamaliro chifunikira kusonyezedwa kuti tisaphonye chifuno chake.)

      Kodi mpumulo kumkhalidwe wathu wauchimo ngwothekera motani?

      Wonani mutu waukulu wakuti “Dipo.”

  • Tsiku la Kubadwa
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Tsiku la Kubadwa

      Tanthauzo: Tsiku la kubadwa kwa munthu kapena kufika kwa tsikulo chaka ndi chaka. Mmalo ena kufika kwa tsiku lakubadwa kwa munthu chaka chirichonse, makamaka la mwana, kumakumbukiridwa ndi phwando ndi kuperekedwa kwa mphatso. Sichiri chizoloŵezi Chabaibulo.

      Kodi maumboni a Baibulo a mapwando a tsiku la kubadwa amawachititsa kukhala mumkhalidwe wovomerezeka? Baibulo limangotchula maumboni aŵiri okha a mapwando otero:

      Gen. 40:20-22: “Ndipo panali tsiku lachitatu ndiro tsiku la kubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero . . . Ndipo anabwezanso wopereka chikho kuntchito yake . . . Koma anampachika wophika mkate wamkulu.”

      Mat. 14:6-10: “Pakufika tsiku lakubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pakati pawo, namkondweretsa Herode. Pomwepo iye anamlonjeza chilumbirire, kumpatsa iye chimene chirichonse akapempha. Ndipo iye, atampangira amake, nati, Ndipatseni inu kuno m’mbizi mutu wa Yohane M’batizi, . . . Anatumiza mnyamata, namdula mutu Yohane m’nyumba yandende.”

      Chirichonse chimene chiri m’Baibulo chiri ndi chifukwa chake. (2 Tim. 3:16, 17) Mboni za Yehova zimazindikira kuti Mawu a Mulungu amanena mosavomereza mapwando a masiku a kubadwa ndipo chotero sizimawachita.

      Kodi ndimotani mmene Akristu oyambirira ndi Ayuda a m’nthaŵi za Baibulo anawonera mapwando a masiku akubadwa?

      “Lingaliro laphwando la tsiku lakubadwa linali kutali ndi malingaliro a Akristu onse a m’nyengo iyi.”—The History of the Christian Religion and Church, During the Three First Centuries (New York, 1848), Augustus Neander (lotembenuzidwa ndi Henry John Rose), p. 190.

      “Ahebri apambuyo pake anawona kuchita phwando la masiku akubadwa kukhala mbali ya kulambira mafano, lingaliro limene likatsimikiziridwa kwambiri ndi zimene anawona m’mapwando wamba ogwirizanitsidwa ndi masiku amenewa.”—The Imperial Bible-Dictionary (London, 1874), lolembedwa ndi Patrick Fairbairn, Vol. I, p. 225.

      Kodi nchiyani chimene chiri magwero a miyambo yofala yogwirizanitsidwa ndi mapwando a masiku akubadwa?

      “Miyambo yosiyanasiyana imene anthu lerolino amachita pamasiku awo a kubadwa iri ndi mbiri yaitali. Magwero ake ndiwo matsenga ndi chipembedzo. Zizoloŵezi zakupereka mafuno

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena