-
MulunguKukambitsirana za m’Malemba
-
-
kanthu timawona umboni wakuti mphamvu yokoka iriko. Ndiponso sitimawona fungo, koma mphuno zathu zimanunkhiza. Ndiponso sitingathe kuwona mphepo youlutsa mawu, koma makutu athu amamva. Chotero timakhulupirira zinthu zimene sitimawona—malinga ngati pali chifukwa chabwino chakutero, kodi sichoncho?’ (3) ‘Eya, kodi pali umboni wakuti Mulungu wosawonekayo alikodi? (Gwiritsirani ntchito mawu patsamba 307, pamutu waung’ono wakuti “Kodi pali zifukwa zabwino zokhulupirira Mulungu?”)’
‘Ndiri ndi lingaliro langalanga ponena za Mulungu’
Mungayankhe kuti: ‘Ndiri wokondwa kumva kuti inu mwalingalira nkhaniyi ndi kuti mumakhulupirira Mulungu. Ntakufunsani kuti, Kodi lingaliro lanu nlotani ponena za Mulungu?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Ndithudi inu mumazindikira kuti kuli kofunika kutsimikizira kuti chirichonse chimene timakhulupirira nchogwirizana ndi zimene Mulungu mwiniyo amanena. Ndingagaŵane nanu mfundo imodzi yokha kuchokera m’Baibulo pankhaniyi? (Sal. 83:18)’
-
-
MwaziKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Mwazi
Tanthauzo: Nsanganizo ya madzi yozizwitsadi imene imazungulira m’mitsempha ya anthu ndi zinyama zambiri za maselo ochuluka, kupereka chakudya ndi mpweya, kutulutsa zonyasa, ndi kuchita mbali yaikulu m’kutetezera thupi kuti lisagwidwe ndi nthenda. Mwazi ngwophatikizidwa kwambiri m’kugwira ntchito kwa moyo kotero kuti Baibulo limati “Moyo wa nyama ukhala m’mwazi.” (Lev. 17:11) Monga Magwero a moyo, Yehova wapereka malangizo otsimikizirika ponena za mmene mwazi ungagwiritsiridwire ntchito.
Akristu akulamulidwa ‘kusala mwazi’
Mac. 15:28, 29, NW: “Mzimu woyera ndi ife [bungwe lolamulira lampingo Wachikristu] tawona kuti nkwabwino kusakuwonjezerani katundu wina wolemera, koposa zinthu zoyenera izi, kupitirizabe kupeŵa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi mwazi ndi zinthu zopotoledwa [kapena, zophedwa popanda kukhetsa mwazi wawo] ndi dama. Ngati musunga zinthu zimenezi mosamalitsa, mudzalemerera. Thanzi labwino kwa inu.” (Panopa kudyedwa kwa mwazi kwalingana ndi kulambira mafano ndi dama, zinthu zimene sitiyenera kufuna kuzichita.)
-